< Yesaya 55 >

1 “Bwerani, inu nonse amene muli ndi ludzu, bwerani madzi alipo; ndipo inu amene mulibe ndalama bwerani, mudzagule chakudya kuti mudye! Bwerani mudzagule vinyo ndi mkaka osalipira ndalama, osalipira chilichonse.
הוֹי כׇּל־צָמֵא לְכוּ לַמַּיִם וַאֲשֶׁר אֵֽין־לוֹ כָּסֶף לְכוּ שִׁבְרוּ וֶאֱכֹלוּ וּלְכוּ שִׁבְרוּ בְּלוֹא־כֶסֶף וּבְלוֹא מְחִיר יַיִן וְחָלָֽב׃
2 Chifukwa chiyani ndalama zanu mukuwonongera zinthu zimene samadya, ndipo mukuwononga malipiro anu pa zinthu zimene sizikhutitsa? Tamverani, mvetsetsani zimene ndikunena kuti mudye zimene zili zabwino; ndipo mudzisangalatse.
לָמָּה תִשְׁקְלוּ־כֶסֶף בְּלוֹא־לֶחֶם וִיגִֽיעֲכֶם בְּלוֹא לְשׇׂבְעָה שִׁמְעוּ שָׁמוֹעַ אֵלַי וְאִכְלוּ־טוֹב וְתִתְעַנַּג בַּדֶּשֶׁן נַפְשְׁכֶֽם׃
3 Tcherani makutu ndipo mubwere kwa Ine; mvereni Ine, kuti mukhale ndi moyo. Ndidzachita nanu pangano losatha, chikondi changa chija chosasinthika ndi chodalirika ndinalonjeza Davide.
הַטּוּ אׇזְנְכֶם וּלְכוּ אֵלַי שִׁמְעוּ וּתְחִי נַפְשְׁכֶם וְאֶכְרְתָה לָכֶם בְּרִית עוֹלָם חַֽסְדֵי דָוִד הַנֶּֽאֱמָנִֽים׃
4 Taonani, ine ndamusankha kuti akhale mboni yanga kwa mitundu ya anthu, kuti akhale mtsogoleri ndi wolamulira mitundu ya anthu.
הֵן עֵד לְאוּמִּים נְתַתִּיו נָגִיד וּמְצַוֵּה לְאֻמִּֽים׃
5 Ndithu inu mudzayitanitsa mitundu ya anthu imene simuyidziwa, ndipo mitundu ya anthu imene sikudziwani idzabwera ndi liwiro kwa inu. Izi zidzatero chifukwa Yehova Mulungu wanu, Woyerayo wa Israeli, wakuvekani ulemerero.”
הֵן גּוֹי לֹֽא־תֵדַע תִּקְרָא וְגוֹי לֹֽא־יְדָעוּךָ אֵלֶיךָ יָרוּצוּ לְמַעַן יְהֹוָה אֱלֹהֶיךָ וְלִקְדוֹשׁ יִשְׂרָאֵל כִּי פֵאֲרָֽךְ׃
6 Funafunani Yehova pamene Iye akupezeka. Mupemphere kwa Iye pamene ali pafupi.
דִּרְשׁוּ יְהֹוָה בְּהִמָּֽצְאוֹ קְרָאֻהוּ בִּֽהְיוֹתוֹ קָרֽוֹב׃
7 Woyipa asiye makhalidwe ake oyipa, ndipo wosalungama asinthe maganizo ake oyipa. Abwerere kwa Yehova, ndipo adzamuchitira chifundo, ndi kwa Mulungu wathu, pakuti adzamukhululukira koposa.
יַעֲזֹב רָשָׁע דַּרְכּוֹ וְאִישׁ אָוֶן מַחְשְׁבֹתָיו וְיָשֹׁב אֶל־יְהֹוָה וִֽירַחֲמֵהוּ וְאֶל־אֱלֹהֵינוּ כִּֽי־יַרְבֶּה לִסְלֽוֹחַ׃
8 “Pakuti maganizo anga siwofanana ndi maganizo anu, ngakhale njira zanu si njira zanga,” akutero Yehova.
כִּי לֹא מַחְשְׁבוֹתַי מַחְשְׁבוֹתֵיכֶם וְלֹא דַרְכֵיכֶם דְּרָכָי נְאֻם יְהֹוָֽה׃
9 “Monga momwe mlengalenga muli kutali ndi dziko lapansi, momwemonso zochita zanga nʼzolekana kutali ndi zochita zanu, ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.
כִּֽי־גָבְהוּ שָׁמַיִם מֵאָרֶץ כֵּן גָּבְהוּ דְרָכַי מִדַּרְכֵיכֶם וּמַחְשְׁבֹתַי מִמַּחְשְׁבֹֽתֵיכֶֽם׃
10 Monga mvula ndi chisanu chowundana zimatsika kuchokera kumwamba, ndipo sizibwerera komweko koma zimathirira dziko lapansi. Ndipo zimameretsa ndi kukulitsa zomera kenaka nʼkupatsa mlimi mbewu ndi chakudya.
כִּי כַּאֲשֶׁר יֵרֵד הַגֶּשֶׁם וְהַשֶּׁלֶג מִן־הַשָּׁמַיִם וְשָׁמָּה לֹא יָשׁוּב כִּי אִם־הִרְוָה אֶת־הָאָרֶץ וְהוֹלִידָהּ וְהִצְמִיחָהּ וְנָתַן זֶרַע לַזֹּרֵעַ וְלֶחֶם לָאֹכֵֽל׃
11 Ndi mmenenso amachitira mawu ochokera mʼkamwa mwanga. Sadzabwerera kwa Ine kopanda phindu lake, koma adzachita zonse zimene ndifuna, ndipo adzakwaniritsa cholinga chimene ndinawatumira.
כֵּן יִהְיֶה דְבָרִי אֲשֶׁר יֵצֵא מִפִּי לֹא־יָשׁוּב אֵלַי רֵיקָם כִּי אִם־עָשָׂה אֶת־אֲשֶׁר חָפַצְתִּי וְהִצְלִיחַ אֲשֶׁר שְׁלַחְתִּֽיו׃
12 Inu mudzatuluka mu mzindawo mwachimwemwe ndipo adzakutsogolerani mwamtendere; mapiri ndi zitunda zidzakuyimbirani nyimbo, ndipo mitengo yonse yamʼthengo idzakuwombereni mʼmanja.
כִּֽי־בְשִׂמְחָה תֵצֵאוּ וּבְשָׁלוֹם תּוּבָלוּן הֶהָרִים וְהַגְּבָעוֹת יִפְצְחוּ לִפְנֵיכֶם רִנָּה וְכׇל־עֲצֵי הַשָּׂדֶה יִמְחֲאוּ־כָֽף׃
13 Mʼmalo mʼmene tsopano muli mitengo ya minga mudzamera mitengo ya payini, ndipo kumene kuli mkandankhuku kudzamera mchisu. Zimenezi zidzakhala chikumbutso cha Yehova, ngati chizindikiro chamuyaya, chimene sichidzafafanizika konse.”
תַּחַת הַֽנַּעֲצוּץ יַעֲלֶה בְרוֹשׁ (תחת) [וְתַחַת] הַסִּרְפַּד יַעֲלֶה הֲדַס וְהָיָה לַֽיהֹוָה לְשֵׁם לְאוֹת עוֹלָם לֹא יִכָּרֵֽת׃

< Yesaya 55 >