< Yesaya 54 >
1 “Sangalala, iwe mayi wosabala, iwe amene sunabalepo mwana; imba nyimbo, ndi kufuwula mwachimwemwe, iwe amene sunamvepo ululu wa pobereka; chifukwa mkazi wosiyidwa adzakhala ndi ana ambiri kuposa mkazi wokwatiwa,” akutero Yehova.
2 Kulitsa malo omangapo tenti yako, tambasula kwambiri nsalu zake, usaleke; talikitsa zingwe zako, limbitsa zikhomo zako.
3 Pakuti udzasendeza malire ako kumanja ndi kumanzere; ndipo zidzukulu zako zidzalanda dziko la anthu a mitundu ina ndipo zidzakhala mʼmizinda yawo yosiyidwa.
4 “Usachite mantha; sadzakunyozanso. Usakhumudwe; sudzapeputsidwanso. Udzayiwala za manyazi zimene zinakuchitikira nthawi ya unyamata wako ndipo za manyazi zimene zinakuchitikira pa nthawi ya umasiye wako sudzazikumbukanso.
5 Pakuti Mlengi wako ali ngati mwamuna wako, dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse. Woyerayo wa Israeli ndiye Mpulumutsi wanu; dzina lake ndi Mulungu wa dziko lonse lapansi.
6 Yehova wakuyitananso, uli ngati mkazi wosiyidwa ndi wodzaza ndi chisoni mu mtima, mkazi amene anakwatiwa pa unyamata wake kenaka nʼkukanidwa,” akutero Mulungu wako.
7 “Kwa kanthawi kochepa, Ine ndinakusiya, koma ndidzakutenganso chifukwa ndimakukonda kwambiri.
8 Ndinakufulatira kwa kanthawi kochepa ndili wokwiya kwambiri. Koma ndi kukoma mtima kwanga kwa muyaya, ndidzakuchitira chifundo,” akutero Yehova Mpulumutsi wako.
9 “Kwa ine zimenezi zili ngati mmene zinalili mʼnthawi ya Nowa. Monga ndinalumbira nthawi imeneyo kuti sindidzawononganso dziko lapansi ndi madzi. Kotero tsopano ndalumbira kuti sindidzakupseraninso mtima, sindidzakudzudzulaninso.
10 Ngakhale mapiri atagwedezeka ndi zitunda kusunthidwa, koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha. Pangano langa lamtendere silidzasintha,” akutero Yehova amene amakuchitira chifundo.
11 “Iwe mzinda wozunzika, wokunthidwa ndi namondwe ndiponso wopanda wokutonthoza, Ine ndidzakongoletsa miyala yako. Maziko ako ndidzamanga ndi miyala ya safiro.
12 Ndidzamanga nsanja zako zankhondo ndi miyala yokongola ya rubi. Ndidzamanga zipata zako ndi miyala yonyezimira ngati moto, ndipo linga lako lonse lidzakhala la miyala yamtengowapatali.
13 Yehova adzaphunzitsa ana ako onse, ndipo ana ako adzakhala ndi mtendere wochuluka.
14 Udzakhazikika mʼchilungamo chenicheni: Sudzakhalanso wopanikizika, chifukwa sudzaopa kanthu kalikonse. Sudzakhalanso ndi mantha chifukwa manthawo sadzafika pafupi ndi iwe.
15 Ngati wina adzakuthirani nkhondo, si ndine amene ndachititsa; aliyense amene adzalimbana nanu adzagonja chifukwa cha iwe.
16 “Taona, ndi Ine amene ndinalenga munthu wosula zitsulo amene amakoleza moto wamakala ndi kusula zida zoti azigwiritse ntchito. Ndipo ndine amene ndinalenga munthu wosakaza kuti awononge;
17 palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke, ndipo onse okuneneza pa mlandu udzawatsutsa. Umu ndimo adzapezekere atumiki a Yehova. Chipambano chawo chichokera kwa Ine,” akutero Yehova.
A Dove is Sent Forth from the Ark