< Yesaya 53 >

1 Ndani wakhulupirira zimene tanenazi; kapena ndani amene Yehova wamuzindikiritsa mphamvu zake?
我們所傳的有誰信呢? 耶和華的膀臂向誰顯露呢?
2 Iye anakula ngati mphukira pamaso pake, ndiponso ngati muzu mʼnthaka yowuma. Iye analibe thupi labwino kapena nkhope yokongola yoti ife nʼkumamuchewukira, analibe maonekedwe woti ife nʼkumamukhumbira.
他在耶和華面前生長如嫩芽, 像根出於乾地。 他無佳形美容; 我們看見他的時候, 也無美貌使我們羨慕他。
3 Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu, munthu amene moyo wake unali wamasautso, wozolowera zowawa, ndipo anali ngati munthu amene anzake amaphimba nkhope zawo akamuona. Iye ananyozedwa, ndipo ife sitinamuyese kanthu.
他被藐視,被人厭棄; 多受痛苦,常經憂患。 他被藐視, 好像被人掩面不看的一樣; 我們也不尊重他。
4 Ndithudi, iye anamva zowawa mʼmalo mwa ife; ndipo anasautsidwa mʼmalo mwathu. Koma ife tinkaganiza kuti ndi Mulungu amene akumulanga, kumukantha ndi kumusautsa.
他誠然擔當我們的憂患, 背負我們的痛苦; 我們卻以為他受責罰, 被上帝擊打苦待了。
5 Koma iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu, ndipo anamuzunza chifukwa cha zoyipa zathu; iye analangidwa kuti ife tikhale ndi mtendere, ndipo ndi mabala ake ife tinachiritsidwa.
哪知他為我們的過犯受害, 為我們的罪孽壓傷。 因他受的刑罰,我們得平安; 因他受的鞭傷,我們得醫治。
6 Ife tonse, ngati nkhosa, tasochera, aliyense mwa ife akungodziyendera; ndipo Yehova wamusenzetsa zoyipa zathu zonse.
我們都如羊走迷; 各人偏行己路; 耶和華使我們眾人的罪孽都歸在他身上。
7 Anthu anamuzunza ndi kumusautsa, koma sanayankhule kanthu. Monga mwana wankhosa wopita naye kokamupha amachitira, kapena monga nkhosa imakhalira duu poyimeta, momwemonso iye sanatsekule pakamwa pake.
他被欺壓, 在受苦的時候卻不開口; 他像羊羔被牽到宰殺之地, 又像羊在剪毛的人手下無聲, 他也是這樣不開口。
8 Atatha kumugwira mwankhanza ndikumuyimba mlandu, kenaka anapita naye kukamupha. Ndipo ndani amene analabadirako za zidzukulu zake, poona kuti iye anachotsedwa mʼdziko la anthu amoyo? Ndani anaganizirapo poona kuti iye anakanthidwa chifukwa cha zolakwa za anthu anga?
因受欺壓和審判,他被奪去, 至於他同世的人,誰想他受鞭打、 從活人之地被剪除, 是因我百姓的罪過呢?
9 Anamukonzera manda ake pamodzi ndi anthu oyipa ndipo anamuyika mʼmanda pamodzi ndi anthu achuma, ngakhale kuti iye sanachite za chiwawa, kapena kuyankhula za chinyengo.
他雖然未行強暴, 口中也沒有詭詐, 人還使他與惡人同埋; 誰知死的時候與財主同葬。
10 Komatu ndi Yehova amene anafuna kuti amuzunze ndi kumusautsa. Yehova anapereka moyo wa mtumiki wake kuti ukhale nsembe yoperekedwa chifukwa cha zolakwa. Tsono iye adzaona zidzukulu zake ndipo adzakhala ndi moyo wautali, ndipo chifuniro cha Yehova chidzachitika mwa iye.
耶和華卻定意將他壓傷, 使他受痛苦。 耶和華以他為贖罪祭。 他必看見後裔,並且延長年日。 耶和華所喜悅的事必在他手中亨通。
11 Atatha mazunzo a moyo wake, adzaona kuwala, ndipo adzakhutira. Mwa nzeru zake mtumiki wanga wolungamayo adzalungamitsa anthu ambiri, popeza adzasenza zolakwa zawo.
他必看見自己勞苦的功效, 便心滿意足。 有許多人因認識我的義僕得稱為義; 並且他要擔當他們的罪孽。
12 Motero Ine ndidzamupatsa ulemu pamodzi ndi akuluakulu, adzagawana zofunkha ndi ankhondo amphamvu, popeza anapereka moyo wake mpaka kufa, ndipo anamuyika mʼgulu la anthu olakwa kuti akhululukidwe. Pakuti iye anasenza machimo a anthu ambiri, ndipo anawapempherera anthu olakwa.
所以,我要使他與位大的同分, 與強盛的均分擄物。 因為他將命傾倒,以致於死; 他也被列在罪犯之中。 他卻擔當多人的罪, 又為罪犯代求。

< Yesaya 53 >