< Yesaya 52 >
1 Dzambatuka, dzambatuka iwe Ziyoni, vala zilimbe. Vala zovala zako zokongola, iwe Yerusalemu, mzinda wopatulika. Pakuti kuyambira tsopano anthu osachita mdulidwe ndi odetsedwa sadzalowanso pa zipata zako.
2 Sasa fumbi lako; imirira nukhale pa mpando waufumu, iwe Yerusalemu. Inu omangidwa a ku Ziyoni, masulani maunyolo amene ali mʼkhosi mwanumo.
3 Pakuti Yehova akuti, “Sindinalandirepo kanthu pamene ndinakugulitsani, choncho mudzawomboledwa wopanda ndalama.”
4 Pakuti Ambuye Yehova akuti, “Poyamba paja anthu anga anapita kukakhala ku Igupto; nawonso Asiriya awapondereza popanda chifukwa.”
5 Tsopano Ine Yehova ndikuti, “Kodi nditani pakuti anthu anga atengedwa ukapolo osaperekapo kanthu, amene amawalamulira amawanyoza,” akutero Yehova. “Ndipo tsiku lonse, akungokhalira kuchita chipongwe dzina langa.
6 Tsono tsiku limenelo anthu anga adzadziwa dzina langa; kotero adzadziwa kuti ndi Ine amene ndikuyankhula, Indedi, ndine.”
7 Ngokongoladi mapazi a amithenga obweretsa nkhani yabwino amene akuyenda pa mapiri. Iwo akukubweretserani nkhani zabwino za mtendere, chisangalalo ndi chipulumutso. Iwo akubwera kudzawuza anthu a ku Ziyoni kuti, “Mulungu wako ndi mfumu!”
8 Mverani! Alonda anu akukweza mawu awo; akuyimba pamodzi mwachimwemwe. Popeza akuona chamaso kubwera kwa Yehova ku Yerusalemu.
9 Imbani pamodzi mofuwula nyimbo zachimwemwe, inu mabwinja a Yerusalemu, pakuti Yehova watonthoza mtima anthu ake, wapulumutsa Yerusalemu.
10 Yehova wagwiritsa ntchito mphamvu zake zopatulika pamaso pa anthu a mitundu yonse, ndipo anthu onse a dziko lapansi adzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.
11 Nyamukani, nyamukani, chokaniko ku Babuloniko! Musakhudze kanthu kodetsedwa! Inu amene mumanyamula ziwiya za Yehova tulukanimo ndipo mudziyeretse.
12 Koma simudzachoka mofulumira kapena kuchita chothawa; pakuti Yehova adzayenda patsogolo panu, Mulungu wa Israeli adzakutetezani kumbuyo kwanu.
13 Taonani, mtumiki wanga adzapambana pa ntchito yake adzakwezedwa ndi kulemekezedwa ndipo adzalandira ulemu waukulu kwambiri.
14 Anthu ambiri atamuona anadzidzimuka, chifukwa nkhope yake inali itasakazika; sinalinso ngati ya munthu. Ndipo thupi lake linasakazika; silinalinso ngati la munthu.
15 Momwemonso anthu a mitundu yonse adzadodoma naye, ndipo mafumu adzatseka pakamwa pawo kusowa chonena chifukwa cha iye. Pakuti zinthu zimene iwo sanawuzidwepo, adzaziona, ndipo zimene sanazimvepo, adzazimvetsa.