< Yesaya 51 >

1 “Mverani Ine, inu amene mukufuna chipulumutso ndiponso amene mumafunafuna Yehova: Taganizani za thanthwe kumene munasemedwa ndipo ku ngwenya kumene anakukumbani;
“Nisikilizeni, ninyi mnaofuatia haki na mnaomtafuta Bwana: Tazameni mwamba ambako mlichongwa, na mahali pa kuvunjia mawe ambako mlichimbwa;
2 taganizani za Abrahamu, kholo lanu, ndi Sara, amene anakubalani. Pamene ndinkamuyitana nʼkuti alibe mwana, koma ndinamudalitsa ndi kumupatsa ana ambiri.
mwangalieni Abrahamu, baba yenu, na Sara, ambaye aliwazaa. Wakati nilipomwita alikuwa mmoja tu, nami nikambariki na kumfanya kuwa wengi.
3 Yehova adzatonthozadi Ziyoni, ndipo adzachitira chifundo mabwinja ake onse; Dziko lake la chipululu adzalisandutsa ngati Edeni, malo ake owuma ngati munda wa Yehova. Anthu adzayimba nyimbo zonditamanda ndi kundiyamika.
Hakika Bwana ataifariji Sayuni, naye atayaangalia kwa huruma magofu yake yote; atayafanya majangwa yake yawe kama Edeni, nazo sehemu zake zisizolimika ziwe kama bustani ya Bwana. Shangwe na furaha zitakuwako ndani yake, shukrani na sauti za kuimba.
4 “Mverani Ine, anthu anga: tcherani khutu, inu mtundu wanga: malangizo adzachokera kwa Ine; cholungama changa chidzawunikira anthu a mitundu yonse.
“Nisikilizeni, watu wangu; nisikieni, taifa langu: Sheria itatoka kwangu; haki yangu itakuwa nuru kwa mataifa.
5 Ndili pafupi kubwera kudzawombola anthu anga. Ndidzabwera mofulumira ngati kuwunika kudzapulumutsa anthu anga; ndipo ndidzalamulira anthu a mitundu yonse. Mayiko akutali akundiyembekezera. Iwo akudikira kuti ndidzawapulumutse.
Haki yangu inakaribia mbio, wokovu wangu unakuja, nao mkono wangu utaleta hukumu kwa mataifa. Visiwa vitanitegemea na kungojea mkono wangu kwa matumaini.
6 Kwezani maso anu mlengalenga, yangʼanani pansi pa dziko; mlengalenga udzazimirira ngati utsi, dziko lapansi lidzatha ngati chovala ndipo anthu ake adzafa ngati nsabwe. Koma chipulumutso changa chidzakhala mpaka muyaya, chilungamo changa chidzakhala cha nthawi zonse.
Inueni macho yenu mbinguni, mkaitazame dunia chini; mbingu zitatoweka kama moshi, dunia itachakaa kama vazi, na wakazi wake kufa kama mainzi. Bali wokovu wangu utadumu milele, haki yangu haitakoma kamwe.
7 “Mverani Ine, inu amene mukudziwa choonadi, anthu inu amene mukusunga malangizo anga mʼmitima yanu; musaope kudzudzulidwa ndi anthu kapena kuopsezedwa akamakulalatirani.
“Nisikieni, ninyi mnaojua lililo sawa, ninyi watu ambao mna sheria yangu mioyoni mwenu: Msiogope mashutumu ya wanadamu wala msitiwe hofu na matukano yao.
8 Pakuti njenjete idzawadya ngati chovala; mbozi idzawadya ngati thonje. Koma chilungamo changa chidzakhala mpaka muyaya, chipulumutso changa chidzakhala mpaka mibadomibado.”
Kwa maana nondo atawala kama vazi, nao funza atawatafuna kama sufu. Lakini haki yangu itadumu milele, wokovu wangu kwa vizazi vyote.”
9 Dzambatukani, dzambatukani! Valani zilimbe, Inu Yehova; dzambatukani, monga munkachitira masiku amakedzana, monga nthawi ya mibado yakale. Si ndinu kodi amene munaduladula Rahabe, amene munabaya chinjoka cha mʼnyanja chija?
Amka, Amka! Jivike nguvu, ewe mkono wa Bwana, Amka, kama siku zilizopita, kama vile vizazi vya zamani. Si ni wewe uliyemkata Rahabu vipande vipande, uliyemchoma yule joka?
10 Kodi sindinu amene munawumitsa nyanja yayikulu, madzi ozama kwambiri aja? Kodi sindinu amene munapanga njira pa madzi ozama, kuti anthu amene munawapulumutsa awoloke powuma?
Si ni wewe uliyekausha bahari, maji ya kilindi kikuu, uliyefanya barabara katika vilindi vya bahari ili waliokombolewa wapate kuvuka?
11 Anthu amene Yehova anawawombola adzabwerera nakafika ku Ziyoni nyimbo ili pakamwa; chimwemwe chamuyaya chizidzaonekera pa nkhope zawo. Adzakhala ndi chikondwerero ndi chimwemwe, chisoni ndi kubuwula zidzathawa.
Wale waliolipiwa fidia na Bwana watarudi. Wataingia Sayuni wakiimba; furaha ya milele itakuwa taji juu ya vichwa vyao. Furaha na shangwe zitawapata, huzuni na kulia kwa uchungu kutatoweka.
12 Yehova akuti, “Ndinetu amene ndimakutonthozani mtima. Chifukwa chiyani mukuopa munthu woti adzafa? Mukuopa munthu woti monga udzu sadzakhalitsa.
“Mimi, naam mimi, ndimi niwafarijie ninyi. Ninyi ni nani hata kuwaogopa wanadamu wanaokufa, wanadamu ambao ni majani tu,
13 Koma inu mumayiwala Yehova Mlengi wanu, amene anayala za mlengalenga ndi kuyika maziko a dziko lapansi. Inu nthawi zonse mumaopsezedwa chifukwa cha ukali wa anthu okuponderezani amene angofuna kukuwonongani. Kodi uli kuti tsopano ukali wa anthu okuponderezaniwo?
kwamba mnamsahau Bwana Muumba wenu, aliyezitanda mbingu na kuiweka misingi ya dunia, kwamba mnaishi katika hofu siku zote kwa sababu ya ghadhabu ya mdhalimu, ambaye nia yake ni kuangamiza? Iko wapi basi ghadhabu ya mdhalimu?
14 Amʼndende adzamasulidwa posachedwa; sadzalowa mʼmanda awo, kapena kusowa chakudya.
Wafungwa waliojikunyata kwa hofu watawekwa huru karibuni; hawatafia kwenye gereza lao, wala hawatakosa chakula.
15 Pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndimavundula nyanja kotero mafunde ake amakokoma. Dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
Kwa maana Mimi ndimi Bwana, Mungu wako, ambaye huisukasuka bahari ili mawimbi yake yangurume: Bwana Mwenye Nguvu Zote ndilo jina lake.
16 Ndayika mawu anga mʼkamwa mwanu ndipo ndakuphimbani ndi mthunzi wa dzanja langa. Ine ndimayika pa malo pake zinthu za mlengalenga, ndipo ndinayika maziko a dziko lapansi, ndimawuza anthu a ku Ziyoni kuti, ‘Ndinu anthu anga.’”
Nimeweka maneno yangu kinywani mwako na kukufunika kwa uvuli wa mkono wangu: Mimi niliyeweka mbingu mahali pake, niliyeweka misingi ya dunia, niwaambiaye Sayuni, ‘Ninyi ni watu wangu.’”
17 Dzambatuka, dzambatuka! Imirira iwe Yerusalemu. Iwe amene wamwa chikho cha mkwiyo chimene Yehova anakupatsa. Iwe amene unagugudiza chikho chochititsa chizwezwe.
Amka, amka! Simama, ee Yerusalemu, wewe uliyekunywa kutoka mkono wa Bwana kikombe cha ghadhabu yake, wewe uliyekunywa mpaka kufikia machujo yake, kikombe kile cha kunywea kiwafanyacho watu kuyumbayumba.
18 Mwa ana onse amene anabereka, panalibe ndi mmodzi yemwe anamutsogolera; mwa ana onse amene analera, panalibe ndi mmodzi yemwe anamugwira dzanja.
Kati ya wana wote aliowazaa hakuwepo hata mmoja wa kumwongoza, kati ya wana wote aliowalea hakuwepo hata mmoja wa kumshika mkono.
19 Mavuto awiriwa akugwera iwe. Dziko lako lasakazika ndi kuwonongeka. Anthu afa ndi njala ndi lupanga. Ndani angakumvere chisoni? Ndani angakutonthoze?
Majanga haya mawili yamekuja juu yako: ni nani awezaye kukufariji? Maangamizi, uharibifu, njaa na upanga: ni nani awezaye kukutuliza?
20 Ana ako akomoka; ali lambalamba pa msewu, ngati mphoyo yogwidwa mu ukonde. Ukali wa Yehova ndi chidzudzulo chake zidzawagwera.
Wana wako wamezimia, wamelala kwenye mwanzo wa kila barabara, kama swala aliyenaswa kwenye wavu. Wamejazwa na ghadhabu ya Bwana na makaripio ya Mungu wako.
21 Nʼchifukwa chake imva izi iwe amene ukuvutika, iwe amene waledzera, koma osati ndi vinyo.
Kwa hiyo sikiliza hili, wewe uliyeteswa, uliyelewa, lakini si kwa mvinyo.
22 Ambuye Yehova wanu, Mulungu amene amateteza anthu ake akuti, “Taona, ndachotsa mʼdzanja lako chikho chimene chimakuchititsa kudzandira; sudzamwanso chikho cha ukali wanga.
Hili ndilo asemalo Bwana Mwenyezi wako, Mungu wako, yeye ambaye huwatetea watu wake: “Tazama, nimeondoa mkononi mwako kikombe kilichokufanya uyumbayumbe; kutoka kikombe hicho, kikombe cha kunywa cha ghadhabu yangu, kamwe hutakunywa tena.
23 Ndidzapereka chikhocho kwa anthu amene amakuzunza, amene ankakuwuza kuti, ‘gona pansi tikuyende pa msana.’ Ndipo msana wako anawuyesa pansi popondapo, ngati msewu woti ayendepo.”
Nitakiweka mikononi mwa watesi wako, wale waliokuambia, ‘Anguka kifudifudi ili tuweze kutembea juu yako.’ Ukaufanya mgongo wako kama ardhi, kama njia yao ya kupita.”

< Yesaya 51 >