< Yesaya 5 >
1 Ndidzamuyimbira bwenzi langa nyimbo yokamba za munda wake wa mpesa: Wokondedwa wanga anali ndi munda wamphesa pa phiri la nthaka yachonde.
2 Anatipula nachotsa miyala yonse ndipo anawokamo mipesa yabwino kwambiri. Anamanga nsanja yolondera pakati pa mundawo ndipo anasemanso mopsinyira mphesa mʼmundamo. Ndipo iye anayembekezera kuti mundawo udzabala mphesa zabwino, koma ayi, unabala mphesa zosadya.
3 “Tsopano, inu amene mumakhala mu Yerusalemu ndi inu anthu a ku Yuda, weruzani pakati pa ine ndi munda wanga wa mpesawu.
4 Kodi nʼchiyaninso china chimene ndikanachitira munda wanga wa mpesa kupambana chomwe ndawuchitira kale? Pamene ndinkayembekezera kuti udzabala mphesa zabwino, bwanji unabala mphesa zosadya?
5 Tsopano ndikuwuzani chimene ndidzawuchitire munda wanga wa mpesa: ndidzachotsa mpanda wake, ndipo mundawo udzawonongeka; ndidzagwetsa khoma lake, ndipo nyama zidzapondapondamo.
6 Ndidzawusandutsa tsala, udzakhala wosatengulira ndi wosalimira ndipo mudzamera mkandankhuku ndi minga ina. Ndidzalamula mitambo kuti isagwetse mvula pa mundapo.”
7 Munda wamphesa wa Yehova Wamphamvuzonse ndi Aisraeli, ndipo anthu a ku Yuda ndiwo minda yake yomukondweretsa. Ndipo Iye ankayembekezera chiweruzo cholungama, mʼmalo mwake anaona kuphana; mʼmalo mwa chilungamo Iye anamva kulira kwa anthu ozunzika.
8 Tsoka kwa inu amene mumangokhalira kulumikiza nyumba, ndipo mumangokhalira kuwonjezera minda, mpaka mutalanda malo onse kuti muzikhalamo nokha mʼdzikomo.
9 Yehova Wamphamvuzonse wayankhula ine ndikumva kuti, “Ndithudi nyumba zambirizo zidzasanduka mabwinja, nyumba zazikulu zokongolazo zidzakhala zopanda anthu.
10 Munda wamphesa wa maekala khumi udzatulutsa vinyo wodzaza mbiya imodzi, kufesa madengu khumi a mbewu, zokolola zake zidzangodzaza dengu limodzi.”
11 Tsoka kwa iwo amene amadzuka mmamawa nathamangira chakumwa choledzeretsa, amene amamwa mpaka usiku kufikira ataledzera kotheratu.
12 Pa maphwando awo pamakhala azeze, apangwe, matambolini, zitoliro ndi vinyo, ndipo sasamala ntchito za Yehova, salemekeza ntchito za manja ake.
13 Motero anthu anga adzatengedwa ukapolo chifukwa cha kusamvetsa zinthu; atsogoleri awo olemekezeka adzafa ndi njala, ndipo anthu wamba ochuluka adzafa ndi ludzu.
14 Nʼchifukwa chake ku manda sikukhuta ndipo kwayasama kwambiri kukamwa kwake; mʼmandamo mudzagweranso anthu otchuka a mu Yerusalemu pamodzi ndi anthu wamba ochuluka; adzagweramo ali wowowo, nʼkuledzera kwawoko. (Sheol )
15 Ndipo munthu aliyense adzatsitsidwa, anthu onse adzachepetsedwa, anthu odzikuza adzachita manyazi.
16 Koma Yehova Wamphamvuzonse adzalemekezedwa chifukwa cha chiweruzo chake cholungama. Ndipo Mulungu woyera adzadzionetsa kuti ndi woyera pochita chilungamo chake.
17 Tsono nkhosa zidzadya pamenepo ngati pabusa pawo; ana ankhosa adzadya mʼmabwinja a anthu olemera.
18 Tsoka kwa amene amadzikokera tchimo ndi zingwe zachinyengo, ndipo amadzikokera zoyipa ndi zingwe zokokera ngolo,
19 amene amanena kuti, “Yehova afulumire, agwire ntchito yake mwamsanga kuti ntchitoyo tiyione. Ntchito zionekere, zimene Woyerayo wa Israeli akufuna kuchita, zichitike kuti tizione.”
20 Tsoka kwa amene zoyipa amaziyesa zabwino ndipo zabwino amaziyesa zoyipa, amene mdima amawuyesa kuwala ndipo kuwala amakuyesa mdima, amene zowawasa amaziyesa zotsekemera ndipo zotsekemera amaziyesa zowawasa.
21 Tsoka kwa amene amadziona ngati anzeru ndipo amadziyesa ochenjera.
22 Tsoka kwa zidakwa zimene zimayika mtima pa vinyo ndipo ndi akatswiri posakaniza zakumwa,
23 amene amamasula olakwa chifukwa cha chiphuphu koma amayipitsa mlandu wa munthu wosalakwa.
24 Nʼchifukwa chake monga momwe moto umawonongera chiputu ndipo monga momwe udzu wowuma umapsera mʼmalawi a moto, momwemonso mizu yawo idzawola ndipo maluwa awo adzafota ndi kuwuluka ngati fumbi; chifukwa akana malamulo a Yehova Wamphamvuzonse, ndipo anyoza mawu a Woyerayo wa Israeli.
25 Nʼchifukwa chake mkwiyo wa Yehova wayakira anthu ake; watambasula dzanja lake pa anthuwo ndipo akuwakantha Mapiri akugwedezeka, ndipo mitembo ya anthu yangoti mbwee mʼmisewu ngati zinyalala. Komabe ngakhale watero, mkwiyo wake sunaleke, dzanja lake likanali chitambasulire;
26 Yehova wakweza mbendera kuyitana mtundu wa anthu akutali, akuyitana anthuwo ndi likhweru kuti abwere kuchokera ku mathero a dziko lapansi. Awo akubwera, akubweradi mofulumira kwambiri!
27 Palibe ndi mmodzi yemwe amene akutopa kapena kupunthwa, palibe amene akusinza kapena kugona; palibe lamba wa mʼchiwuno amene akumasuka, palibe chingwe cha nsapato chimene chaduka.
28 Mivi yawo ndi yakuthwa, mauta awo onse ndi okoka, ziboda za akavalo awo nʼzolimba ngati mwala wansagalabwi, magaleta awo ndi aliwiro ngati kamvuluvulu.
29 Kufuwula kwawo kuli ngati kubangula kwa mkango, amabangula ngati misona ya mkango; imadzuma pamene ikugwira nyama ndipo imapita nayo popanda ndi mmodzi yemwe woyipulumutsa.
30 Tsiku limenelo mitundu ya anthu idzabangula ngati mkokomo wa madzi a mʼnyanja. Ndipo wina akakayangʼana dzikolo adzangoona mdima ndi zovuta; ngakhale kuwala kudzasanduka mdima chifukwa cha mitambo.