< Yesaya 49 >
1 Mverani Ine, inu anthu a pa zilumba tcherani khutu, inu anthu a mayiko akutali: Yehova anandiyitana ine ndisanabadwe, ananditchula dzina ndili mʼmimba ya amayi anga.
諸島嶼,請聽我!遠方的人民,請靜聽!上主由母腹中就召叫了我,自母胎中就給我起了名字。
2 Iye anasandutsa pakamwa panga kukhala ngati lupanga lakuthwa, anandibisa mu mthunzi wa dzanja lake; Iye anandisandutsa ngati muvi wakuthwa ndipo anandibisa mʼchimake.
他使我的口好似利劍,將我掩護在他的手蔭下,使我像一支磨光的箭,將我隱藏在他的箭囊中。
3 Iye anati kwa ine, “Ndiwe mtumiki wanga, Israeli. Anthu adzanditamanda chifukwa cha iwe.”
他對我說:你是我的僕人,是我驕矜的「以色列。」
4 Koma Ine ndinati, “Ine ndinkaganiza kuti ndinagwira ntchito ndi kuwononga mphamvu zanga pachabe, koma ayi, zondiyenera zili mʼmanja a Yehova, ndipo mphotho yanga ili mʼmanja mwa Mulungu wanga.”
但是我說:「我白白勤勞了,我枉費了氣力而毫無益處;但是我的權利是在上主那裏,我的報酬在我的天主面前。」
5 Yehova anandiwumba ine mʼmimba mwa amayi anga kuti ndikhale mtumiki wake kuti ndibweze fuko la Yakobo kwa Iye ndi kusonkhanitsa Israeli kwa Iye, choncho ndimalemekezeka mʼmaso mwa Yehova, ndipo ndimapeza mphamvu mwa Mulungu wanga.
我在上主眼中是光榮的,天主是我的力量。那由母胎形成我作他的僕人,將雅各伯領回到他前,並把以色列聚在他前的上主,如今說:「
6 Yehovayo tsono akuti, “Nʼchinthu chochepa kwambiri kwa iwe kuti ukhale mtumiki wanga, kuti udzutse mafuko a Yakobo ndi kuwabweretsa kwawo Aisraeli amene anapulumuka. Choncho iwe udzakhala ngati chowunikira, udzafikitsa uthenga wa chipulumutso changa ku mathero a dziko lapansi.”
你作我的僕人,復興雅各伯支派,領回以色列遺留下的人,還是小事,我更要使你作萬民的光明,使我的救恩達於地極。」
7 Yehova Mpulumutsi ndi Woyerayo wa Israeli akuyankhula, Woyerayo wa Israeli akunena, amene mitundu ya anthu inamuda, amenenso anali kapolo wa mafumu ankhanza uja kuti, “Mafumu adzaona ntchito ya chipulumutso changa ndipo adzayimirira. Akalonga nawonso adzagwada pansi. Zimenezi zidzachitika chifukwa cha Yehova amene ndi wokhulupirika ndi Woyerayo wa Israeli amene wakusankha iwe.”
上主,以色列的救主和聖者,向那極受輕慢,為列國所憎惡,且作統治者奴役的人這樣說:「列王必要見而起立,諸侯必要見而下拜:這是因為上主忠實可靠,以色列的聖者揀選了你的緣故。」
8 Yehova akuti, “Pa nthawi imene ndinakukomera mtima ndinakuyankha, ndipo pa tsiku lachipulumutso ndinakuthandiza; ndinakusunga ndi kukusandutsa kuti ukhale pangano kwa anthu, kuti dziko libwerere mwakale ndi kuti cholowa changa chowonongeka chija ndichigawegawenso.
上主這樣說:在悅納的時候,我俯允了你;在救恩的日期,我幫助了你;我必保護你,使你作為人民的盟約,復興國家,分得荒蕪的產業,
9 Ndidzawuza a mʼndende kuti atuluke ndi a mu mdima kuti aonekere poyera. “Adzapeza chakudya mʼmphepete mwa njira ndi msipu pa mʼmalo owuma.
好向俘虜說:「你們出來罷!」向在黑暗中的人說:「你們出現罷!」他們將在各路上被牧放,他們的牧場是在一切荒嶺上。
10 Iwo sadzamva njala kapena ludzu, kutentha kwa mʼchipululu kapena dzuwa silidzawapsereza; chifukwa Iye amene amawachitira chifundo adzawatsogolera ndi kuwaperekeza ku akasupe a madzi.
他們不餓也不渴,熱風和列日也不損傷他們,因為那憐憫他們的率領著他們,引領他們到水泉傍。
11 Mapiri anga onse ndidzawasandutsa njira yoyendamo, ndipo misewu yanga yayikulu ndidzayikweza.
我要使我的一切山嶺變為大路,並把我的街道修高。
12 Taonani, anthu anga adzachokera kutali, ena kumpoto, ena kumadzulo, enanso adzachokera ku chigawo cha Asuwani.”
看啊!有的由遠方而來,有的由北方和西方而來,還有些由息寧而來。
13 Imbani mwachimwemwe, inu zolengedwa zamlengalenga; kondwera, iwe dziko lapansi; imbani nyimbo inu mapiri! Pakuti Yehova watonthoza mtima anthu ake, ndipo wachitira chifundo anthu ake ovutika.
諸天要歡樂,大地要踴躍,山嶺要歡呼高唱,因為上主安慰了他的百姓,憐恤了他受苦的人們。
14 Koma Ziyoni anati, “Yehova wandisiya, Ambuye wandiyiwala.”
熙雍曾說過:「上主離棄了我,吾主忘掉了我。」
15 “Kodi amayi angathe kuyiwala mwana wawo wakubere ndi kusachitira chifundo mwana amene anabereka iwo eni? Ngakhale iye angathe kuyiwala, Ine sindidzakuyiwala iwe!
婦女豈能忘掉自己的乳嬰﹖出為人母的,豈能忘掉親生的兒子﹖縱然她們能忘掉,我也不能忘掉你啊﹖
16 Taona, ndakulemba iwe mʼzikhantho zanga; makoma ako ndimawaona nthawi zonse.
看哪!我已把你刻在我的手掌上,你的城牆時常在我的眼前。
17 Amisiri odzakumanganso akubwerera mofulumira, ndipo amene anakupasula akuchokapo.
建築你的工人急速動工,那毀滅你和破壞你的,要離你遠去。
18 Kweza maso ako ndipo uyangʼaneyangʼane ana ako onse akusonkhana ndipo akubwera kwa iwe. Yehova akuti, ‘Ine Yehova wamoyo, anthu ako adzakhala ngati chinthu chodzikongoletsa chimene mkwatibwi wavala pa mkono pake.’
你舉目四望罷!他們都已集合到你這裏來;我永遠生活--上主的斷語--他們必如裝飾品穿戴在你身上,把你裝扮得有如新娘。
19 “Ngakhale unasanduka bwinja ndi kuwonongedwa ndipo dziko lako ndi kusakazidwa, chifukwa cha kuchuluka kwa anthu malo okhalamo adzakhala operewera ndipo amene anakuwononga iwe aja adzakhala kutali.
至於你的廢址,你那荒蕪和遭蹂躪之地,如今為你的居民都太狹小了,因為吞噬你的人已遠離他去。
20 Ana obadwa nthawi yako yachisoni adzanena kuti, ‘Malo ano atichepera, tipatse malo ena woti tikhalemo.’
連你在不孕期中所生的子女也要說給你聽:「這地方為我太狹小了,請給我一個住處罷!」
21 Tsono iwe udzadzifunsa kuti, ‘Kodi ndani anandiberekera ana amenewa? Ana anga onse anamwalira ndipo sindinathenso kukhala ndi ana ena; ndinapita ku ukapolo ndipo ndinachotsedwa. Ndani anawalera ana amenewa? Ndinatsala ndekha, nanga awa, achokera kuti?’”
那時你心裏會問:「誰給我生育了這些人呢﹖我原是不妊不孕的,【且是流放被逐的,】這些人是誰給我養大的﹖看!我本是孤苦零丁的,他們卻是從那裏來的﹖」
22 Zimene Ambuye Yehova akunena ndi izi, “Taonani, Ine ndidzakodola Anthu a mitundu ina kuti abwere. Ndidzawakwezera anthu a mitundu ina mbendera yanga kuti abwere. Tsono adzabwera ndi ana ako aamuna atawanyamula mʼmanja mwawo ndipo adzanyamula ana ako aakazi pa mapewa awo.
吾主上主這樣說:「看!我要向列邦高舉我的手,向萬民樹起我的旗幟;他們必要把你的兒子抱在懷中帶來,把你的女兒放在肩上背來。
23 Mafumu adzakhala abambo wongokulera ndipo akazi a mafumu adzakhala amayi wongokulera. Iwo adzagwetsa nkhope zawo pansi. Ndiye inu mudzazindikira kuti Ine ndine Yehova; iwo amene amadalira Ine sadzakhumudwa.”
列王要作你的養父,皇后要當你的保姆。他們要在你面前俯伏在地,並要舔去你腳上的塵土;那時你將知道:我是上主;凡仰賴我的,決不會蒙羞。」
24 Kodi mungathe kulanda anthu ankhondo zofunkha zawo, kapena kupulumutsa anthu ogwidwa mʼdzanja la munthu wankhanza?
獵物豈能由勇士手中奪回﹖俘虜豈能由強者手中救出﹖
25 Koma zimene Yehova akunena ndi izi, “Ankhondo adzawalanda amʼndende awo, ndipo munthu woopsa adzamulanda zofunkha zawo; ndidzalimbana ndi amene amalimbana nanu, ndipo ndidzapulumutsa ana anu.
但是,上主這樣說:「俘虜必要由勇士手中奪回,獵物必要由強者手中救出。我必與同你爭奪的人爭奪,我必拯救你的子孫。
26 Anthu amene anakuponderezani adzadya mnofu wawo omwe; adzamwa magazi awo omwe ngati aledzera ndi vinyo. Zikadzatero anthu onse adzadziwa kuti Ine Yehova, ndine Mpulumutsi wanu, Momboli wanu, Wamphamvu wa Yakobo.”
我要使壓迫你的人吃自己的肉,喝自己的血如喝新酒。如此,凡有血肉的人都知道我是上主,是你的拯救者,是你的救主,是雅各伯的大能者。」