< Yesaya 48 >
1 “Mverani izi, inu nyumba ya Yakobo, inu amene amakutchani dzina lanu Israeli, ndinu a fuko la Yuda, inu mumalumbira mʼdzina la Yehova, ndi kupemphera kwa Mulungu wa Israeli, ngakhale osati mʼchoonadi kapena mʼchilungamo.
audite hoc domus Iacob qui vocamini nomine Israhel et de aquis Iuda existis qui iuratis in nomine Domini et Dei Israhel recordamini non in veritate neque in iustitia
2 Komabe inu mumadzitcha nzika za mzinda wopatulika ndipo mumadalira Mulungu wa Israeli, amene dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse:
de civitate enim sancta vocati sunt et super Deum Israhel constabiliti sunt Dominus exercituum nomen eius
3 Zimene zinachitika poyamba ndinalosera kalekale, zinatuluka mʼkamwa mwanga ndipo ndinazilengeza; tsono mwadzidzidzi ndinachitapo kanthu ndipo zinachitikadi.
priora ex tunc adnuntiavi et ex ore meo exierunt et audita feci ea repente operatus sum et venerunt
4 Pakuti Ine ndinadziwa kuti iwe ndiwe nkhutukumve wa nkhongo gwaa, wa mutu wowuma.
scivi enim quia durus es tu et nervus ferreus cervix tua et frons tua aerea
5 Ine ndinakuwuziratu zinthu izi kalekale lomwe; zisanachitike ndinazilengezeratu kwa iwe kuti unganene kuti, ‘Fano langa ndilo lachita zimenezi, kapena kuti fano langa losema ndi kamulungu kanga kachitsulo ndiwo analamula kuti zimenezi zichitike.’
praedixi tibi ex tunc antequam venirent indicavi tibi ne forte diceres idola mea fecerunt haec et sculptilia mea et conflatilia mandaverunt ista
6 Inu munamva zinthu zimenezi. Kodi inu simungazivomereze? “Kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo ndidzakuwuzani zinthu zatsopano zinthu zobisika zimene simunazidziwe konse.
quae audisti vide omnia vos autem non adnuntiastis audita feci tibi nova ex nunc et conservata quae nescis
7 Zinthu zimenezi zikulengedwa tsopano lino, osati kalekale; munali musanazimve mpaka lero lino. Choncho inu simunganene kuti, ‘Zimenezi ndiye ayi, ndinazidziwa kale.’
nunc creata sunt et non ex tunc et ante diem et non audisti ea ne forte dicas ecce cognovi ea
8 Inu simunazimvepo kapena kuzidziwa; makutu anu sanali otsekuka. Tsono Ine ndinadziwa bwino kuti ndinu anthu achiwembu ndi kuti chiyambire ubwana wanu munatchedwa owukira.
neque audisti neque cognovisti neque ex tunc aperta est auris tua scio enim quia praevaricans praevaricabis et transgressorem ex ventre vocavi te
9 Ine ndikuchedwetsa mkwiyo wanga chifukwa cha dzina langa. Ndikukulezerani ukali wanga kuti anthu andilemekeze. Sindidzakuwonongani kotheratu.
propter nomen meum longe faciam furorem meum et laude mea infrenabo te ne intereas
10 Taonani, ndinakuyeretsani ngati siliva; ndinakuyesani mʼngʼanjo yamasautso.
ecce excoxi te sed non quasi argentum elegi te in camino paupertatis
11 Chifukwa cha ulemu wanga, chifukwa cha ulemu wanga Ine ndikuchita zimenezi. Ndingalole bwanji kuti ndinyozeke? Ulemerero wanga sindidzawupereka kwa wina.
propter me propter me faciam ut non blasphemer et gloriam meam alteri non dabo
12 “Tamvera Ine, iwe Yakobo, Israeli, amene ndinakuyitana: Mulungu uja Woyamba ndi Wotsiriza ndine.
audi me Iacob et Israhel quem ego voco ego ipse ego primus et ego novissimus
13 Inde dzanja langa linamanga maziko a dziko lapansi, dzanja langa lamanja linafunyulula mlengalenga. Ndi mawu anga ndinalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
manus quoque mea fundavit terram et dextera mea mensa est caelos ego vocabo eos et stabunt simul
14 “Sonkhanani pamodzi inu nonse ndipo mvetserani: Ndani mwa mafano anu amene analoseratu za zinthu izi? Wokondedwa wa Yehova uja adzachita zomwe Iye anakonzera Babuloni; dzanja lake lidzalimbana ndi Kaldeya.
congregamini omnes vos et audite quis de eis adnuntiavit haec Dominus dilexit eum faciet voluntatem suam in Babylone et brachium suum in Chaldeis
15 Ine, Inetu, ndayankhula; ndi kumuyitana ndidzamubweretsa ndine ndipo adzakwaniritsa zolinga zake.
ego ego locutus sum et vocavi eum adduxi eum et directa est via eius
16 “Bwerani pafupi ndipo mvetserani izi: “Kuyambira pachiyambi sindinayankhule mobisa; pa nthawi imene zinkachitika zimenezi Ine ndinali pomwepo.” Ndipo tsopano Ambuye Yehova wandipatsa Mzimu wake ndi kundituma.
accedite ad me et audite hoc non a principio in abscondito locutus sum ex tempore antequam fieret ibi eram et nunc Dominus Deus misit me et spiritus eius
17 Yehova, Mpulumutsi wanu, Woyerayo wa Israeli akuti, “Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsa kuti upindule, ndimakutsogolera pa njira yoyenera kuyitsata.
haec dicit Dominus redemptor tuus Sanctus Israhel ego Dominus Deus tuus docens te utilia gubernans te in via qua ambulas
18 Ngati iwe ukanangosamalira zolamulira zanga, bwenzi mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chipulumutso chako ngati mafunde a pa nyanja.
utinam adtendisses mandata mea facta fuisset sicut flumen pax tua et iustitia tua sicut gurgites maris
19 Zidzukulu zako zikanachuluka ngati mchenga, ana ako akanachuluka ngati fumbi; dzina lawo silikanachotsedwa pamaso panga ndipo silikanafafanizidwa konse.”
et fuisset quasi harena semen tuum et stirps uteri tui ut lapilli eius non interisset et non fuisset adtritum nomen eius a facie mea
20 Tulukani mʼdziko la Babuloni! Thawani dziko la Kaldeya! Lengezani zimenezi ndi mawu a chisangalalo ndipo muzilalikire mpaka kumathero a dziko lapansi; muzinena kuti, “Yehova wawombola Yakobo mtumiki wake.”
egredimini de Babylone fugite a Chaldeis in voce exultationis adnuntiate auditum facite hoc efferte illud usque ad extrema terrae dicite redemit Dominus servum suum Iacob
21 Iwo sanamve ludzu pamene Yehova ankawatsogolera mʼchipululu; anawapatsa madzi otuluka mʼthanthwe; anangʼamba thanthwelo ndipo munatuluka madzi.
non sitierunt in deserto cum educeret eos aquam de petra produxit eis et scidit petram et fluxerunt aquae
22 “Palibe mtendere kwa anthu ochimwa,” akutero Yehova.
non est pax dicit Dominus impiis