< Yesaya 47 >
1 “Tsika, ndi kukhala pa fumbi, iwe namwali, Babuloni; khala pansi wopanda mpando waufumu, iwe namwali, Kaldeya pakuti sadzakutchulanso wanthete kapena woyenera kumugwira mosamala.
2 Tenga mphero ndipo upere ufa; chotsa nsalu yako yophimba nkhope kwinya chovala chako mpaka ntchafu ndipo woloka mitsinje.
3 Maliseche ako adzakhala poyera ndipo udzachita manyazi. Ndidzabwezera chilango ndipo palibe amene adzandiletse.”
4 Woyerayo wa Israeli ndiye Mpulumutsi wathu, dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
5 “Khala chete, ndipo lowa mu mdima, iwe namwali, Kaldeya; chifukwa sadzakutchulanso mfumukazi ya maufumu.
6 Ndinawakwiyira anthu anga, osawasamalanso. Ndinawapereka manja mwako, ndipo iwe sunawachitire chifundo. Iwe unachitira nkhanza ngakhale nkhalamba.
7 Iwe unati, ‘Ine ndidzakhalapo nthawi zonse ngati mfumukazi.’ Koma sunaganizire zinthu izi kapena kusinkhasinkha za mmene ziti zidzathere.
8 “Ndipo tsopano, tamvera, iwe wongokonda zokondweretsawe, amene ukukhala mosatekesekawe, umaganiza mu mtima mwako kuti, ‘Ine ndi Ine, ndipo kupatula ine palibenso wina. Sindidzakhala konse mkazi wamasiye, ndipo ana anga sadzamwalira.’
9 Koma mʼkamphindi, ndiponso tsiku limodzi, zinthu ziwiri izi zidzakuchitikira: ana ako kukufera komanso kukhala mkazi wamasiye. Zimenezi zidzakuchitikira kwathunthu ngakhale ali ndi amatsenga ambiri ndi mawula amphamvu.
10 Iwe unkadalira kuyipa kwako ndipo unati, ‘Palibe amene akundiona.’ Kuchenjera ndi nzeru zako zidzakusokoneza, choncho ukuganiza mu mtima mwako kuti, ‘Ine ndine basi, ndipo kupatula ine palibenso wina.’
11 Ngozi yayikulu idzakugwera ndipo sudzadziwa momwe ungayipewere ndi matsenga ako. Mavuto adzakugwera ndipo sudzatha kuwachotsa; chipasupasu chimene iwe sukuchidziwa chidzakugwera mwadzidzidzi.
12 “Pitiriza tsono kukhala ndi matsenga ako, pamodzi ndi nyanga zako zochulukazo, wakhala ukuzigwiritsa ntchito kuyambira ubwana wako. Mwina udzatha kupambana kapena kuopsezera nazo adani ako.
13 Malangizo onse amene unalandira angokutopetsa basi! Abwere patsogolopa anthu amene amatanthauzira za kumwamba kuti adzakupulumutseni. Abwere amene amayangʼana nyenyezi, ndi kumalosera mwezi ndi mwezi zimene ziti zidzakuchitikire.
14 Ndithudi, anthuwo ali ngati phesi; adzapsa ndi moto. Sangathe kudzipulumutsa okha ku mphamvu ya malawi a moto. Awa si makala a moto woti wina nʼkuwotha; kapena moto woti wina nʼkuwukhalira pafupi.
15 Umu ndi mmene adzachitire amatsenga, anthu amene wakhala ukugwira nawo ntchito ndi kuchita nawo malonda chiyambire cha ubwana wako. Onse adzamwazika ndi mantha, sipadzakhala ndi mmodzi yemwe wokupulumutsa.”