< Yesaya 46 >

1 Beli wagwada pansi, Nebo wawerama; nyama zonyamula katundu za nyamula milungu yawo. Mafano awo asanduka katundu wolemera pa msana pa ngʼombe. Asandukadi ngati katundu pa msana pa nyama zotopa.
כָּרַע בֵּל קֹרֵס נְבוֹ הָיוּ עֲצַבֵּיהֶם לַחַיָּה וְלַבְּהֵמָה נְשֻׂאֹתֵיכֶם עֲמוּסוֹת מַשָּׂא לַעֲיֵפָֽה׃
2 Nyamazo zikuwerama ndi kufuna kugwa ndi milunguyo; sizikutha kupulumutsa katunduyo, izo zomwe zikupita ku ukapolo.
קָרְסוּ כָֽרְעוּ יַחְדָּו לֹא יָכְלוּ מַלֵּט מַשָּׂא וְנַפְשָׁם בַּשְּׁבִי הָלָֽכָה׃
3 Mverani Ine, Inu nyumba ya Yakobo, inu nonse otsala a mʼnyumba ya Israeli, Ine ndakhala ndi kukusamalirani kuyambira mʼmimba ya amayi anu, ndakhala ndikukunyamulani chibadwire chanu.
שִׁמְעוּ אֵלַי בֵּית יַעֲקֹב וְכׇל־שְׁאֵרִית בֵּית יִשְׂרָאֵל הַֽעֲמֻסִים מִנִּי־בֶטֶן הַנְּשֻׂאִים מִנִּי־רָֽחַם׃
4 Mpaka pamene mudzakalambe ndi kumera imvi ndidzakusamalirani ndithu. Ndinakulengani ndipo ndidzakunyamulani, ndidzakusamalirani ndi kukulanditsani.
וְעַד־זִקְנָה אֲנִי הוּא וְעַד־שֵׂיבָה אֲנִי אֶסְבֹּל אֲנִי עָשִׂיתִי וַאֲנִי אֶשָּׂא וַאֲנִי אֶסְבֹּל וַאֲמַלֵּֽט׃
5 “Kodi inu mudzandifanizira ndi yani, kapena mufananitsa ndi yani? Kodi mudzandiyerekeza kapena kundifanizitsa ndi yani?
לְמִי תְדַמְּיוּנִי וְתַשְׁווּ וְתַמְשִׁלוּנִי וְנִדְמֶֽה׃
6 Anthu ena amakhuthula golide mʼzikwama zawo ndipo amayeza siliva pa masikelo; amalemba ntchito mʼmisiri wosula kuti awapangire mulungu, kenaka iwo amagwada pansi ndikupembedza kamulunguko.
הַזָּלִים זָהָב מִכִּיס וְכֶסֶף בַּקָּנֶה יִשְׁקֹלוּ יִשְׂכְּרוּ צוֹרֵף וְיַעֲשֵׂהוּ אֵל יִסְגְּדוּ אַף־יִֽשְׁתַּחֲוֽוּ׃
7 Amanyamula nʼkumayenda nayo milunguyo pa mapewa awo; amayikhazika pa malo pake ndipo imakhala pomwepo. Singathe kusuntha pamalo pakepo. Ngakhale wina apemphere kwa milunguyo singathe kuyankha; kapena kumupulumutsa ku mavuto ake.
יִשָּׂאֻהוּ עַל־כָּתֵף יִסְבְּלֻהוּ וְיַנִּיחֻהוּ תַחְתָּיו וְיַֽעֲמֹד מִמְּקוֹמוֹ לֹא יָמִישׁ אַף־יִצְעַק אֵלָיו וְלֹא יַעֲנֶה מִצָּרָתוֹ לֹא יוֹשִׁיעֶֽנּוּ׃
8 “Kumbukirani zimenezi ndipo muchite manyazi, Muzilingalire mu mtima, inu anthu owukira.
זִכְרוּ־זֹאת וְהִתְאֹשָׁשׁוּ הָשִׁיבוּ פוֹשְׁעִים עַל־לֵֽב׃
9 Kumbukirani zinthu zakale zinthu zamakedzana; chifukwa Ine ndine Mulungu ndipo palibe wina ofanana nane.
זִכְרוּ רִאשֹׁנוֹת מֵעוֹלָם כִּי אָנֹכִי אֵל וְאֵין עוֹד אֱלֹהִים וְאֶפֶס כָּמֽוֹנִי׃
10 Ndinaneneratu zakumathero kuchokera pachiyambi pomwe. Kuyambira nthawi yamakedzana ndinaloseratu zoti zidzachitike. Ndikanena zimene ndifuna kuchita ndipo zimachitikadi. Chilichonse chimene ndafuna ndimachichita.
מַגִּיד מֵֽרֵאשִׁית אַחֲרִית וּמִקֶּדֶם אֲשֶׁר לֹא־נַֽעֲשׂוּ אֹמֵר עֲצָתִי תָקוּם וְכׇל־חֶפְצִי אֶעֱשֶֽׂה׃
11 Ndikuyitana chiwombankhanga kuchokera kummawa. Ndikuyitana kuchokera ku dziko lakutali munthu amene adzakwaniritsa cholinga changa. Zimene ndanena ndidzazikwaniritsadi; zimene ndafuna ndidzazichitadi.
קֹרֵא מִמִּזְרָח עַיִט מֵאֶרֶץ מֶרְחָק אִישׁ (עצתו) [עֲצָתִי] אַף־דִּבַּרְתִּי אַף־אֲבִיאֶנָּה יָצַרְתִּי אַף־אֶעֱשֶֽׂנָּה׃
12 Ndimvereni, inu anthu owuma mtima, inu amene muli kutali ndi chipulumutso.
שִׁמְעוּ אֵלַי אַבִּירֵי לֵב הָרְחוֹקִים מִצְּדָקָֽה׃
13 Ndikubweretsa pafupi tsiku la chipulumutso changa; sichili kutali. Tsikulo layandikira ndipo sindidzachedwa kukupulumutsani ndi kupereka ulemerero wanga kwa Israeli.
קֵרַבְתִּי צִדְקָתִי לֹא תִרְחָק וּתְשׁוּעָתִי לֹא תְאַחֵר וְנָתַתִּי בְצִיּוֹן תְּשׁוּעָה לְיִשְׂרָאֵל תִּפְאַרְתִּֽי׃

< Yesaya 46 >