< Yesaya 45 >

1 Yehova akuyankhula ndi wodzozedwa wake Koresi amene anamugwira dzanja lamanja kuti agonjetse mitundu ya anthu ndi kuwalanda mafumu zida zawo zankhondo, ndi kutsekula zitseko kuti zipatazo zisadzatsekedwenso ndi ichi:
Hæc dicit Dominus christo meo Cyro, cuius apprehendi dexteram, ut subiiciam ante faciem eius Gentes, et dorsa regum vertam, et aperiam coram eo ianuas, et portæ non claudentur.
2 Ine ndidzayenda patsogolo pako, ndi kusalaza mapiri; ndidzaphwanya zitseko za mkuwa ndi kuthyola mipiringidzo ya chitsulo.
Ego ante te ibo: et gloriosos terræ humiliabo: portas æreas conteram, et vectes ferreos confringam.
3 Ndidzakupatsa chuma chobisika mu mdima, katundu wa pamalo obisika, kotero kuti udziwe kuti Ine ndine Yehova Mulungu wa Israeli, amene ndakuyitana pokutchula dzina.
Et dabo tibi thesauros absconditos, et arcana secretorum: ut scias quia ego Dominus, qui voco nomen tuum, Deus Israel.
4 Chifukwa cha mtumiki wanga Yakobo, chifukwa cha wosankhidwa wanga Israeli, Ine ndakuyitana pokutchula dzina ndipo ndakupatsa dzina laulemu ngakhale iwe sukundidziwa Ine.
Propter servum meum Iacob, et Israel electum meum, et vocavi te nomine tuo: assimilavi te, et non cognovisti me.
5 Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina; kupatula Ine palibenso Mulungu wina. Ndidzakupatsa mphamvu, ngakhale sukundidziwa Ine,
Ego Dominus, et non est amplius: extra me non est deus: accinxi te, et non cognovisti me:
6 kotero kuti kuchokera kummawa mpaka kumadzulo anthu adzadziwa kuti palibe wina koma Ine ndekha. Ine ndine Yehova, ndipo palibenso wina.
Ut sciant hi, qui ab ortu solis, et qui ab occidente, quoniam absque me non est: ego Dominus, et non est alter,
7 Ndimalenga kuwala ndi mdima, ndimabweretsa madalitso ndi tsoka; ndine Yehova, amene ndimachita zonsezi.
formans lucem, et creans tenebras, faciens pacem, et creans malum: ego Dominus faciens omnia hæc.
8 “Iwe thambo gwetsa mvula kuchokera kumwamba; mitambo ivumbwe mivumbi ya chilungamo. Dziko lapansi litsekuke, ndipo chipulumutso chiphuke kuti chilungamo chimereponso; Ine Yehova, ndine ndalenga zimenezi.
Rorate cæli desuper, et nubes pluant iustum: aperiatur terra, et germinet salvatorem: et iustitia oriatur simul: ego Dominus creavi eum.
9 “Tsoka kwa wokangana ndi mlengi wake, ngakhale kuti ali ngati phale chabe pakati pa mapale anzake. Kodi dongo lingafunse munthu wowumba kuti, ‘Kodi ukuwumba chiyani?’ Kodi ntchito yako inganene kuti, ‘Ulibe luso?’
Væ qui contradicit Fictori suo, testa de samiis terræ: numquid dicet lutum figulo suo: Quid facis, et opus tuum absque manibus est?
10 Tsoka kwa wofunsa abambo ake kuti, ‘Kodi munabereka chiyani?’ Kapena amayi ake kuti, ‘Kodi mufuna kubereka chiyani?’
Væ qui dicit patri: Quid generas? et mulieri: Quid parturis?
11 “Yehova Woyerayo wa Israeli, ndiponso Mlengi wake akunena, zokhudza zinthu zimene zikubwera ndi izi: Kodi iwe ukundifunsa za ana anga, kapena kundilamula pa zokhudza ntchito zanga?
Hæc dicit Dominus, Sanctus Israel, Plastes eius: Ventura interrogate me, super filios meos, et super opus manuum mearum mandate mihi.
12 Ndine amene ndinapanga dziko lapansi ndikulenga munthu kuti akhalemo. Ine ndi manja anga ndinayalika thambo; ndimalamulira zolengedwa zonse za mlengalenga.
Ego feci terram, et hominem super eam creavi ego: manus meæ tetenderunt cælos, et omni militiæ eorum mandavi.
13 Ndine amene ndidzawutsa Koresi kuti chilungamo changa chikwaniritsidwe: ndipo ndidzawongolera njira zake zonse. Iye adzamanganso mzinda wanga ndi kumasula anthu anga amene ali mu ukapolo, wopanda kupereka ndalama kapena mphotho, akutero Yehova Wamphamvuzonse.”
Ego suscitavi eum ad iustitiam, et omnes vias eius dirigam: ipse ædificabit civitatem meam, et captivitatem meam dimittet, non in pretio, neque in muneribus, dicit Dominus Deus exercituum.
14 Yehova akuti, “Chuma cha ku Igupto ndi chuma cha malonda cha Kusi chidzakhala chanu. Anthu amphamvu zawo ndi athanzi a ku Seba adzabwera kwa inu ndipo adzakhala anthu anu; iwo adzidzakutsatani pambuyo panu ali mʼmaunyolo. Adzakugwadirani ndi kukupemphani, ponena kuti, ‘Ndithudi Mulungu ali ndi inu, ndipo palibenso wina; palibenso mulungu wina.’”
Hæc dicit Dominus: Labor Ægypti, et negotiatio Æthiopiæ, et Sabaim viri sublimes, ad te transibunt, et tui erunt: Post te ambulabunt, vincti manicis pergent: et te adorabunt, teque deprecabuntur: Tantum in te est Deus, et non est absque te Deus.
15 Zoonadi inu muli ndi Mulungu wobisika amene ali Mulungu ndi Mpulumutsi wa Israeli.
Vere tu es Deus absconditus, Deus Israel Salvator.
16 Onse amene amapanga mafano adzawachititsa manyazi ndi kuwanyozetsa. Adzakhala osokonezeka maganizo.
Confusi sunt, et erubuerunt omnes: simul abierunt in confusionem fabricatores errorum.
17 Koma Yehova adzapulumutsa Israeli ndi chipulumutso chamuyaya; simudzachitanso manyazi kapena kunyozeka mpaka kalekale.
Israel salvatus est in Domino salute æterna: non confundemini, et non erubescetis usque in sæculum sæculi.
18 Yehova analenga zinthu zakumwamba, Iye ndiye Mulungu; amene akulenga dziko lapansi, ndi kulikhazikitsa, sanalipange kuti likhale lopanda kanthu, koma analipanga kuti anthu akhalemo. Iyeyu akunena kuti: Ine ndine Yehova, ndipo palibenso wina.
Quia hæc dicit Dominus creans cælos, ipse Deus formans terram, et faciens eam, ipse Plastes eius: non in vanum creavit eam: ut habitaretur, formavit eam. Ego Dominus, et non est alius.
19 Ine sindinayankhule mwachinsinsi, pamalo ena a mdima; Ine sindinaziwuze zidzukulu za Yakobo kuti, “Ndifunefuneni ku malo kopanda kanthu.” Ine Yehova, ndimayankhula zoona; ndikunena zolungama.
Non in abscondito locutus sum, in loco terræ tenebroso: non dixi semini Iacob: Frustra quærite me. Ego Dominus loquens iustitiam, annuncians recta.
20 Yehova akuti, “Sonkhanani pamodzi ndipo mubwere; yandikirani, inu amene munapulumuka pothawa nkhondo kwa anthu a mitundu ina. Ndinu opanda nzeru amene mumanyamula mafano a mitengo, amene mumapemphera kwa milungu imene singathe kupulumutsa.
Congregamini, et venite, et accedite simul qui salvati estis ex Gentibus: nescierunt qui levant lignum sculpturæ suæ, et rogant deum non salvantem.
21 Fotokozani mlandu wanu, mupatsane nzeru nonse pamodzi. Kodi ndani ananeneratu zimenezi kalekale? Ndani anazifotokozeratu zimenezi nthawi yamakedzana? Kodi si Ineyo Yehova? Ndipo palibenso Mulungu wina kupatula Ine, Mulungu wolungama ndi Wopulumutsa, palibenso wina kupatula Ine.
Annunciate, et venite, et consiliamini simul: Quis auditum fecit hoc ab initio, ex tunc prædixit illud? Numquid non ego Dominus, et non est ultra deus absque me? Deus iustus, et salvans non est præter me.
22 “Tembenukirani kwa Ine kuti mupulumuke, inu anthu onse a pa dziko lapansi, pakuti Ine ndine Mulungu ndipo palibenso wina.
Convertimini ad me, et salvi eritis omnes fines terræ: quia ego Deus, et non est alius.
23 Ndalumbira ndekha, pakamwa panga patulutsa mawu owona, mawu amene sadzasinthika konse akuti, bondo lililonse lidzagwada pamaso panga; anthu onse adzalumbira potchula dzina langa.
In memetipso iuravi, egredietur de ore meo iustitiæ verbum, et non revertetur: quia mihi curvabitur omne genu, et iurabit omnis lingua.
24 Iwo adzanene kwa Ine kuti, ‘Chilungamo ndi mphamvu zimapezeka mwa Yehova yekha.’” Onse amene anamuwukira Iye adzabwera kwa Iye ndipo adzachita manyazi.
Ergo in Domino, dicet, meæ sunt iustitiæ et imperium: ad eum venient, et confundentur omnes qui repugnant ei.
25 Koma mwa Yehova zidzukulu zonse za Israeli zidzapambana ndi kupeza ulemerero.
In Domino iustificabitur, et laudabitur omne semen Israel.

< Yesaya 45 >