< Yesaya 44 >

1 Yehova akuti, “Mvera tsopano, iwe Yakobo, mtumiki wanga, Israeli, amene ndinakusankha.
ועתה שמע יעקב עבדי וישראל בחרתי בו׃
2 Yehova amene anakupanga iwe, anakuwumba iwe mʼmimba ya amayi ako, ndi amene adzakuthandiza iwe. Iye akuti, Usachite mantha, iwe Yakobo, mtumiki wanga, Yesuruni, amene ndinakusankha.
כה אמר יהוה עשך ויצרך מבטן יעזרך אל תירא עבדי יעקב וישרון בחרתי בו׃
3 Pakuti ndidzathira madzi pa nthaka yowuma, ndi kuyendetsa mitsinje mʼdziko lowuma; ndidzatumiza Mzimu wanga pa ana anu, ndi kutsitsa madalitso anga pa zidzukulu zanu.
כי אצק מים על צמא ונזלים על יבשה אצק רוחי על זרעך וברכתי על צאצאיך׃
4 Iwo adzakula ngati udzu wothirira bwino ndi ngati bango lomera mʼmbali mwa mitsinje ya madzi oyenda.
וצמחו בבין חציר כערבים על יבלי מים׃
5 Wina adzanena kuti, ‘Ine ndine wa Yehova;’ wina adzadzitcha yekha wa banja la Yakobo; winanso adzalemba pa dzanja lake, ‘Wa Yehova’ ndipo adzadzitcha wa banja la Israeli.
זה יאמר ליהוה אני וזה יקרא בשם יעקב וזה יכתב ידו ליהוה ובשם ישראל יכנה׃
6 “Yehova Mfumu ndi Mpulumutsi wa Israeli, Yehova Wamphamvuzonse akuti: Ine ndine woyamba ndi wotsiriza; palibenso Mulungu wina koma Ine ndekha.
כה אמר יהוה מלך ישראל וגאלו יהוה צבאות אני ראשון ואני אחרון ומבלעדי אין אלהים׃
7 Ndani nanga angafanane ndi Ine? Muloleni kuti ayankhule. Muloleni andifotokozere ndi kundiyalira bwino lomwe zimene zinachitika kuyambira pamene ndinkakhazikitsa anthu anga akalekale, ndi ziti zimene zidzachitike; inde, muloleni alosere zimene zikubwera.
ומי כמוני יקרא ויגידה ויערכה לי משומי עם עולם ואתיות ואשר תבאנה יגידו למו׃
8 Musanjenjemere, musachite mantha. Kodi sindinakuwuzeni zimenezi ndi kuzilosera kalekale lomwe? Inu ndinu mboni zanga. Kodi aliponso Mulungu wina kupatula Ine? Ayi, palibe Thanthwe linanso limene sindikulidziwa.”
אל תפחדו ואל תרהו הלא מאז השמעתיך והגדתי ואתם עדי היש אלוה מבלעדי ואין צור בל ידעתי׃
9 Onse amene amapanga mafano ngachabe, ndipo milungu imene amayilemekeza ndi yopanda phindu. Iwo amene amapembedza mafano ndi wosaona; ndipo sazindikira kanthu. Choncho adzawachititsa manyazi.
יצרי פסל כלם תהו וחמודיהם בל יועילו ועדיהם המה בל יראו ובל ידעו למען יבשו׃
10 Ndani amasema mulungu ndi kuwumba fano, limene silingamupindulire?
מי יצר אל ופסל נסך לבלתי הועיל׃
11 Iye pamodzi ndi anzake onse adzawachititsa manyazi; amisiri a mafano ndi anthu chabe. Aloleni onse asonkhane ndi kuyima pabwalo la milandu; onse adzaopsedwa ndipo adzachita manyazi.
הן כל חבריו יבשו וחרשים המה מאדם יתקבצו כלם יעמדו יפחדו יבשו יחד׃
12 Mmisiri wa zitsulo amatenga chitsulo ndipo amachiyika pa makala amoto; ndi dzanja lake lamphamvu amachisula pochimenya ndi nyundo. Pambuyo pake mʼmisiri uja amamva njala natha mphamvu; iye samwa madzi, ndipo amalefuka.
חרש ברזל מעצד ופעל בפחם ובמקבות יצרהו ויפעלהו בזרוע כחו גם רעב ואין כח לא שתה מים וייעף׃
13 Mmisiri wa matabwa nayenso amayeza mtengo ndi chingwe ndipo amajambula chithunzi ndi cholembera; amasema bwinobwino ndi chipangizo chake ndipo amachiwongola bwino ndi chida chake. Amachipanga ngati munthu, munthu wake wokongola kuti aliyike mʼnyumba yake yachipembedzo.
חרש עצים נטה קו יתארהו בשרד יעשהו במקצעות ובמחוגה יתארהו ויעשהו כתבנית איש כתפארת אדם לשבת בית׃
14 Amagwetsa mitengo ya mkungudza, mwinanso amatenga mtengo wa payini kapena wa thundu nʼkudzisankhira mtengo wabwino pakati pa mitengo ya mʼnkhalango, ndipo amadzala mtengo wa payini ndi kuwuleka kuti ukule ndi mvula.
לכרת לו ארזים ויקח תרזה ואלון ויאמץ לו בעצי יער נטע ארן וגשם יגדל׃
15 Mitengoyo munthu amachitako nkhuni; nthambi zina amasonkhera moto wowotha, amakolezera moto wophikira buledi ndi mbali ina ya mtengowo amapangira mulungu ndipo amapembedza; iye amapanga fano ndi kumaligwadira.
והיה לאדם לבער ויקח מהם ויחם אף ישיק ואפה לחם אף יפעל אל וישתחו עשהו פסל ויסגד למו׃
16 Chigawo china cha mtengowo amasonkhera moto wowotcherapo nyama imene amadya, nakhuta. Iye amawotha motowo ndipo amanena kuti, “Aa! Ndikumva kutentha; pano pali moto.”
חציו שרף במו אש על חציו בשר יאכל יצלה צלי וישבע אף יחם ויאמר האח חמותי ראיתי אור׃
17 Chigawo chotsala amapanga kamulungu, fano lake limenelo; amaligwadira ndi kulipembedza. Amapemphera kwa fanolo ndipo amanena kuti, “Iwe ndiwe mulungu wanga, ndipulumutse.”
ושאריתו לאל עשה לפסלו יסגוד לו וישתחו ויתפלל אליו ויאמר הצילני כי אלי אתה׃
18 Anthu otere sadziwa kanthu, samvetsa kanthu kalikonse; maso awo ndi omatirira ndipo sangathe kuona, ndipo mitu yawo ndi yogontha kotero sangathe kumvetsa.
לא ידעו ולא יבינו כי טח מראות עיניהם מהשכיל לבתם׃
19 Palibe amene amayima nʼkulingalira. Palibe wanzeru kapena womvetsa zinthu bwino woti nʼkunena kuti, chigawo china cha mtengowo ndinasonkhera moto; pa makala ake ndinaphikira buledi, ndinawotchapo nyama ndipo ndinadya. Chigawo chotsalachi ndipangire chinthu chonyansachi. Kodi ndidzagwadira mtengo?
ולא ישיב אל לבו ולא דעת ולא תבונה לאמר חציו שרפתי במו אש ואף אפיתי על גחליו לחם אצלה בשר ואכל ויתרו לתועבה אעשה לבול עץ אסגוד׃
20 Munthu wotere ali ngati wodya phulusa, maganizo ake opusa amusocheretsa; motero kuti sangathe kudzipulumutsa yekha kapena kudzifunsa kuti, “Kodi chinthu chili mʼmanja mwangachi si chabodza?”
רעה אפר לב הותל הטהו ולא יציל את נפשו ולא יאמר הלוא שקר בימיני׃
21 Yehova akuti, “Iwe Yakobo, kumbukira zinthu izi popeza kuti ndiwe mtumiki wanga, iwe Israeli. Ine ndinakupanga iwe, ndiwe mtumiki wanga; iwe Israeli, sindidzakuyiwala.
זכר אלה יעקב וישראל כי עבדי אתה יצרתיך עבד לי אתה ישראל לא תנשני׃
22 Ndachotsa zolakwa zako ngati mitambo, ndi machimo ako ngati nkhungu ya mmawa. Bwerera kwa Ine, popeza ndakupulumutsa.”
מחיתי כעב פשעיך וכענן חטאותיך שובה אלי כי גאלתיך׃
23 Imbani mwachimwemwe, inu zolengedwa zamlengalenga, pakuti Yehova wachita zimenezi; fuwula, iwe dziko lapansi. Imbani nyimbo, inu mapiri, inu nkhalango ndi mitengo yonse, chifukwa Yehova wawombola Yakobo, waonetsa ulemerero wake mwa Israeli.
רנו שמים כי עשה יהוה הריעו תחתיות ארץ פצחו הרים רנה יער וכל עץ בו כי גאל יהוה יעקב ובישראל יתפאר׃
24 Yehova Mpulumutsi wanu, amene anakuwumbani mʼmimba ya amayi anu akuti: “Ine ndine Yehova, amene anapanga zinthu zonse, ndinatambasula ndekha zinthu zakuthambo, ndinayala ndekha dziko lapansi.
כה אמר יהוה גאלך ויצרך מבטן אנכי יהוה עשה כל נטה שמים לבדי רקע הארץ מי אתי׃
25 Ndine amene ndinalepheretsa mipingo ya anthu onyenga, ndipo ndimapusitsa owombeza mawula. Ndimasokoneza anthu a nzeru, ndi kuonetsa kuti nzeru zawo nʼzopusa.
מפר אתות בדים וקסמים יהולל משיב חכמים אחור ודעתם ישכל׃
26 Ndine amene ndimatsimikiza mawu a atumiki ake ndi kukwaniritsa zimene analosera amithenga ake. “Ndine amene ndinanena za Yerusalemu kuti mudzakhalanso anthu. Ndinanenanso za mizinda ya Yuda kuti idzamangidwanso. Za mabwinja awo ndinanena kuti ndidzawawutsanso.
מקים דבר עבדו ועצת מלאכיו ישלים האמר לירושלם תושב ולערי יהודה תבנינה וחרבותיה אקומם׃
27 Ndine amene ndinawuza nyanga yayikulu kuti, ‘Uma’ ndipo ndidzawumitsa mitsinje yako.
האמר לצולה חרבי ונהרתיך אוביש׃
28 Ndine amene ndinanena kwa Koresi kuti, ‘Iye ndiye mʼbusa wanga,’ ndipo adzachita zonse zimene ndikufuna; iye adzalamula kuti, ‘Yerusalemu amangidwenso’ ndi kuti, ‘Maziko a Nyumba ya Mulungu ayikidwenso.’”
האמר לכורש רעי וכל חפצי ישלם ולאמר לירושלם תבנה והיכל תוסד׃

< Yesaya 44 >