< Yesaya 43 >

1 Koma tsopano, Yehova amene anakulenga, iwe Yakobo, amene anakuwumba, iwe Israeli akuti, “Usaope, pakuti ndakuwombola; Ndinakuyitanitsa mokutchula dzina lako, ndiwe wanga.
Et nunc hæc dicit Dominus creans te Iacob, et formans te Israel: Noli timere, quia redemi te, et vocavi te nomine tuo: meus es tu.
2 Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe; ndipo pamene ukuwoloka mitsinje, sidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto, sudzapsa; lawi la moto silidzakutentha.
Cum transieris per aquas, tecum ero, et flumina non operient te: cum ambulaveris in igne, non combureris, et flamma non ardebit in te:
3 Chifukwa Ine Yehova, Mulungu wako, Woyera wa Israeli, ndine Mpulumutsi wako. Ndinapereka Igupto pofuna kuti ndiwombole iwe, ndinapereka Kusi ndi Seba mʼmalo mwa iwe.
Quia ego Dominus Deus tuus sanctus Israel salvator tuus, dedi propitiationem tuam Ægyptum, Æthopiam, et Saba pro te.
4 Popeza kuti ndiwe wamtengowapatali wolemekezeka ndi wapamtima panga, ndipo chifukwa ndimakukonda, ndidzapereka anthu mʼmalo mwa iwe, ndidzapereka mitundu ya anthu pofuna kuwombola moyo wako.
Ex quo honorabilis factus es in oculis meis, et gloriosus: ego dilexi te, et dabo homines pro te, et populos pro anima tua.
5 Usachite mantha, pakuti Ine ndili nawe; ndidzabweretsa ana ako kuchokera kummawa, ndipo ndidzakusonkhanitsani kuchokera kumadzulo.
Noli timere, quia ego tecum sum: ab Oriente adducam semen tuum, et ab Occidente congregabo te.
6 Ndidzawuza a kumpoto kuti, ‘Amasuleni,’ ndidzawuza akummwera kuti, ‘Musawagwire.’ Bweretsani ana anga aamuna kuchokera ku mayiko akutali, ana anga a akazi kuchokera kumalekezero a dziko lapansi;
Dicam Aquiloni: Da: et Austro: Noli prohibere: affer filios meos de longinquo, et filias meas ab extremis terræ.
7 onsewo amadziwika ndi dzina langa; ndinawalenga chifukwa cha ulemerero wanga, ndinawawumba, inde ndinawapanga.”
Et omnem, qui invocat nomen meum, in gloriam meam creavi eum, formavi eum, et feci eum.
8 Tulutsa anthu amene ali nawo maso koma sakupenya, anthu amene ali nawo makutu koma sakumva.
Educ foras populum cæcum, et oculos habentem: surdum, et aures ei sunt.
9 Mitundu yonse ya anthu isonkhane pamodzi, anthu a mitundu ina akhale pamodzi pabwalo la milandu. Ndani wa iwo amene ananeneratu zimenezi? Ndani wa iwo anatifotokozerapo zinthu zakalekale? Abweretu ndi mboni zawo kuti adzatsimikizire kuti ananena zoona, kuti anthu ena amve ndi kunena kuti, “Ndi zoona.”
Omnes gentes congregatæ sunt simul, et collectæ sunt tribus: quis in vobis annunciet istud, et quæ prima sunt audire nos faciet? dent testes eorum, iustificentur, et audiant, et dicant: Vere.
10 Yehova akunena kuti, “Inu Aisraeli ndinu mboni zanga, ndi mtumiki wanga amene ndinakusankha, kuti mundidziwe ndi kundikhulupirira, ndipo mudzamvetsa kuti Mulungu ndine ndekha. Patsogolo panga sipanapangidwepo mulungu wina, ngakhale pambuyo panga sipadzakhalaponso wina.”
Vos testes mei, dicit Dominus, et servus meus, quem elegi: ut sciatis, et credatis mihi, et intelligatis quia ego ipse sum. Ante me non est formatus Deus, et post me non erit.
11 Akutero Yehova, “Ine, Inetu ndine Yehova, ndipo palibe Mpulumutsi wina koma Ine ndekha.
Ego sum, ego sum Dominus, et non est absque me salvator.
12 Ndine amene ndinaneneratu, amene ndinakupulumutsa; ndine, osati mulungu wina wachilendo pakati panu amene ndinalengezeratu. Inu ndinu mboni zanga, kuti Ine ndine Mulungu,” akutero Yehova.
Ego annunciavi, et salvavi: auditum feci, et non fuit in vobis alienus: vos testes mei, dicit Dominus, et ego Deus.
13 “Ine ndine Mulungu kuyambira nthawi yamakedzana, ndipo ndidzakhalabe Mulungu ku nthawi zonse. Palibe amene angathe kuthawa mʼmanja mwanga, ndipo chimene ndachita palibe angathe kuchisintha.”
Et ab initio ego ipse, et non est qui de manu mea eruat: operabor, et quis avertet illud?
14 Yehova akuti, Mpulumutsi wanu, Woyerayo wa Israeli akuti, “Chifukwa cha inu ndidzatuma gulu lankhondo kukalimbana ndi Babuloni ndi kukupulumutsani. Ndidzagwetsa zitseko zonse za mzindawo, ndipo kukondwa kwa anthu ake kudzasanduka kulira.
Hæc dicit Dominus redemptor vester, sanctus Israel: Propter vos misi in Babylonem, et detraxi vectes universos, et Chaldæos in navibus suis gloriantes.
15 Ine ndine Yehova, Woyera wanu uja, Mlengi wa Israeli. Ine ndine Mfumu yanu.”
Ego Dominus sanctus vester, creans Israel rex vester.
16 Yehova anapanga njira pa nyanja, anapanga njira pakati pa madzi amphamvu.
Hæc dicit Dominus, qui dedit in mari viam, et in aquis torrentibus semitam.
17 Iye anasonkhanitsa magaleta, akavalo, gulu lankhondo ndi asilikali amphamvu, ndipo onse anagwa pamenepo, osadzukanso anazimitsidwa kutheratu ngati chingwe cha nyale. Yehova ameneyu akuti,
Qui eduxit quadrigam et equum: agmen et robustum, simul obdormierunt, nec resurgent: contriti sunt quasi linum, et extincti sunt.
18 “Iwalani zinthu zakale; ndipo musaganizirenso zinthu zimene zinachitika kale.
Ne memineritis priorum, et antiqua ne intueamini.
19 Taonani, Ine ndikuchita zinthu zatsopano! Tsopano zayamba kale kuoneka; kodi simukuziona? Ine ndikulambula msewu mʼchipululu ndi kupanga mitsinje mʼdziko lowuma.
Ecce ego facio nova, et nunc orientur, utique cognoscetis ea: ponam in deserto viam, et in invio flumina.
20 Nyama zakuthengo, nkhandwe ndi akadzidzi zinandilemekeza. Ndidzayendetsa mitsinje mʼdziko lowuma kuti ndiwapatse madzi anthu anga osankhidwa.
Glorificabit me bestia agri, dracones et struthiones: quia dedi in deserto aquas, flumina in invio, ut darem potum populo meo, electo meo.
21 Anthu amene ndinadziwumbira ndekha kuti aziyimba nyimbo yotamanda Ine.
Populum istum formavi mihi, laudem meam narrabit.
22 “Komatu simunapemphera kwa Ine, Inu a mʼbanja la Yakobo, munatopa nane, Inu Aisraeli.
Non me invocasti Iacob, nec laborasti in me Israel.
23 Simunabweretse kwa Ine nkhosa za nsembe zopsereza, kapena kundilemekeza ndi nsembe zanu. Ine sindinakulemetseni pomakupemphani zopereka za chakudya kapena kukutopetsani pomakupemphani nsembe zofukiza.
Non obtulisti mihi arietem holocausti tui, et victimis tuis non glorificasti me: non te servire feci in oblatione, nec laborem tibi præbui in thure.
24 Simunandigulire bango lonunkhira kapena kundipatsa Ine mafuta okwanira a nsembe zanu. Koma inu mwandilemetsa Ine ndi machimo anu ndipo mwanditopetsa Ine ndi zolakwa zanu.
Non emisti mihi argento calamum, et adipe victimarum tuarum non inebriasti me. Verumtamen servire me fecisti in peccatis tuis, præbuisti mihi laborem in iniquitatibus tuis.
25 “Ine, Inetu, ndi amene ndimafafaniza zolakwa zanu, chifukwa cha Ine mwini, ndipo sindidzakumbukiranso machimo anu.
Ego sum, ego sum ipse qui deleo iniquitates tuas propter me, et peccatorum tuorum non recordabor.
26 Mundikumbutse zakale, ndipo titsutsane nkhaniyi pamodzi; fotokozani mlandu wanu kuti muonetse kuti ndinu osalakwa.
Reduc me in memoriam, et iudicemur simul: narra si quid habes ut iustificeris.
27 Kholo lanu loyamba linachimwa; ndipo Atsogoleri anu achipembedzo anandiwukira.
Pater tuus primus peccavit, et interpretes tui prævaricati sunt in me.
28 Chifukwa chake Ine ndidzanyazitsa akuluakulu a Nyumba yanu ya mapemphero, ndipo ndidzapereka Yakobo kuti awonongedwe ndi Israeli kuti achitidwe chipongwe.”
Et contaminavi principes sanctos, dedi ad internecionem Iacob, et Israel in blasphemiam.

< Yesaya 43 >