< Yesaya 42 >

1 “Nayu mtumiki wanga, amene ndimamuchirikiza, amene ndamusankha, amenenso ndimakondwera naye. Ndayika Mzimu wanga mwa Iyeyo, ndipo adzaweruza anthu a mitundu yonse mwachilungamo.
Behold, my servant, whom I uphold; my chosen one, in him I take delight. I have put my Spirit upon him; he will bring justice to the nations.
2 Iye sadzafuwula, sadzamveka mawu, kapena mawu ake kumveka mʼmisewu.
He will not cry out nor shout, nor make his voice heard in the streets.
3 Bango lophwanyika sadzalithyola, ndipo moto wozilala sadzawuzimitsa. Motero adzaonetsa kuti chilungamo ndicho choonadi;
A crushed reed he will not break, and a dimly burning wick he will not quench: he will faithfully execute justice.
4 sadzafowoka kapena kukhumudwa mpaka atakhazikitsa chilungamo pa dziko lapansi, ndi mpaka mayiko a mʼmbali mwa nyanja atafika poyembekezera malangizo ake.”
He will not grow faint nor be discouraged until he has established justice on the earth; and the coastlands wait for his law.
5 Yehova Mulungu amene analenga zamlengalenga ndi kuziyalika, amene analenga dziko lapansi ndi zonse zimene zimabereka, amenenso amapereka mpweya kwa anthu ake okhala mʼdzikomo, ndi moyo kwa onse oyendamo, akuti,
This is what God Yahweh says— the one who created the heavens and stretched them out, the one who made the earth and all that it produces, the one who gives breath to the people on it and life to those who live on it:
6 “Ine Yehova, ndakuyitana chifukwa Ine ndine wolungama; ndikugwira dzanja ndipo ndidzakuteteza. Ndakupereka kukhala pangano langa kwa anthu ndi kuwunika kwa anthu a mitundu ina.
“I, Yahweh, have called you in righteousness and will hold your hand. I will keep you and set you as a covenant for the people, as a light for the Gentiles,
7 Udzatsekula maso a anthu osaona, udzamasula anthu a mʼndende ndi kutulutsa mʼndende anthu okhala mu mdima.
to open the eyes of the blind, to release the prisoners from the dungeon, and from the house of confinement those who sit in darkness.
8 “Ine ndine Yehova: dzina langa ndi limenelo! Sindidzapereka ulemerero wanga kwa wina aliyense kapena matamando anga kwa mafano.
I am Yahweh, that is my name; and my glory I will not share with another nor my praise with carved idols.
9 Taonani, zinthu zimene ndinalosera kale zachitikadi, ndipo ndikuwuzani zinthu zatsopano; zinthuzo zisanaonekere Ine ndakudziwitsani.”
See, the previous things came to pass, now I am about to declare new events. Before they begin to occur I will tell you about them.”
10 Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, mutamandeni inu okhala mʼdziko lonse lapansi, inu amene mumayenda pa nyanja, nyanja ikokome ndi zonse zili mʼmenemo. Inu okhala pa zilumba tamandani Yehova.
Sing to Yahweh a new song, and his praise from the end of the earth; you who go down to the sea, and all that is in it, the coastlands, and those who live there.
11 Chipululu ndi mizinda yake zikweze mawu awo; midzi ya Akedara ikondwere. Anthu a ku Sela ayimbe mwachimwemwe; afuwule kuchokera pamwamba pa mapiri.
Let the desert and the cities cry out, the villages where Kedar lives, shout for joy! Let the inhabitants of Sela sing; let them shout from the mountaintops.
12 Atamande Yehova ndipo alalike matamando ake kwa anthu apazilumba zonse.
Let them give glory to Yahweh and declare his praise in the coastlands.
13 Yehova adzapita ku nkhondo ngati munthu wamphamvu, adzawutsa ukali wake ngati munthu wankhondo; akukuwa ndiponso akufuwula mfuwu wankhondo ndipo adzagonjetsa adani ake.
Yahweh will go out as a warrior; as a man of war he will stir up his zeal. He will shout, yes, he will roar his battle cries; he will show his enemies his power.
14 Yehova akuti, “Ndakhala ndili chete kwa nthawi yayitali, ndakhala ndili phee osachita kanthu. Koma tsopano, ngati mayi pa nthawi yochira, ndi kubuwula ndi kupuma modukizadukiza ndipo ndili wefuwefu.
I have kept quiet for a long time; I have been still and restrained myself; now I will cry out like a woman in labor; I will gasp and pant.
15 Ndidzawononga mapiri ndi zitunda ndipo ndidzawumitsa zomera zawo zonse; ndidzasandutsa mitsinje kukhala zilumba ndipo ndidzawumitsa maiwe.
I will lay waste mountains and hills and dry up all their vegetation; and I will turn the rivers into islands and will dry up the marshes.
16 Ndidzatsogolera anthu osaona mʼmisewu imene sanayidziwe, ndidzawatsogolera mʼnjira zimene sanayendepo; ndidzasandutsa mdima wa kutsogolo kwawo kuti ukhale kuwala ndipo ndidzasalaza malo osalala. Zimenezi ndizo ndidzachite; sindidzawataya.
I will bring the blind by a way that they do not know; in paths that they do not know I will lead them. I will turn the darkness into light before them, and make the crooked places straight. These things I will do, and I will not abandon them.
17 Koma onse amene amadalira mafano amene amanena kwa mafanowo kuti, ‘ndinu milungu yathu,’ ndidzawachititsa manyazi kotheratu.
They will be turned back, they will be completely put to shame, those who trust in carved figures, who say to cast metal figures, “You are our gods.”
18 “Imvani, agonthi inu; yangʼanani osaona inu, kuti muone!
Listen, you deaf; and look, you blind, that you may see.
19 Ali wosaona ndani, si mtumiki wanga kodi? Ndipo ndani ali wosamva ngati mthenga amene ndamutuma? Kodi ndani ali wosaona ngati uja ndinachita naye pangano, kapena wosaona ndani ngati mtumiki wa Yehova?
Who is blind but my servant? Or deaf like my messenger I send? Who is as blind as my covenant partner, or blind as Yahweh's servant?
20 Iwe waona zinthu zambiri, koma sunazisamale; makutu ako ndi otsekuka koma sumva kanthu.”
You see many things, but do not comprehend; ears are open, but no one hears.
21 Chinamukomera Yehova chifukwa cha chilungamo chake, kapena lamulo lake kukhala lalikulu ndi lopambana.
It pleased Yahweh to praise his justice and to make his law glorious.
22 Koma awa ndi anthu amene afunkhidwa ndi kuwalanda zinthu zawo, onsewa anawakola mʼmaenje kapena akuwabisa mʼndende. Tsono asanduka chofunkha popanda wina wowapulumutsa kapena kunena kuti, “Abwezeni kwawo.”
But this is a people robbed and plundered; they are all trapped in pits, held captive in prisons; they have become a plunder with no one to rescue them, and no one says, “Bring them back!”
23 Kodi ndani wa inu amene adzamvetsera zimenezi kapena kutchera khutu ndi kumva za mʼtsogolomo?
Who among you will listen to this? Who will listen and hear in the future?
24 Ndani anapereka Yakobo kwa ofunkha, ndi Israeli kwa anthu akuba? Kodi si Yehova, amene ife tamuchimwirayu? Pakuti sanathe kutsatira njira zake; ndipo sanamvere malangizo ake.
Who gave Jacob over to the robber, and Israel to the looters? Was it not Yahweh, against whom we have sinned, in whose ways they refused to walk, and whose law they refused to obey?
25 Motero anawakwiyira kwambiri, nawavutitsa ndi nkhondo. Anayatsa moto ponseponse mowazungulira komabe iwo sanamvetse; motowo unawapsereza, koma iwo sanatengepo phunziro ayi.
Therefore he poured out on them his fierce anger and the violence of war, Its flames encircled them, yet they did not understand; it consumed them, but they did not take it to heart.

< Yesaya 42 >