< Yesaya 41 >

1 “Khalani chete pamaso panga, inu mayiko a mʼmbali mwa nyanja! Alekeni ayandikire ndi kuyankhula; tiyeni tikhale pamodzi kuti atiweruze.
החרישו אלי איים ולאמים יחליפו כח יגשו אז ידברו יחדו למשפט נקרבה
2 “Ndani anadzutsa wochokera kummawa uja amene ananka napambana kulikonse kumene ankapita? Iye amapereka anthu a mitundu ina mʼmanja mwake ndipo ndi lupanga lake anagonjetsa ndi kusandutsa mafumu kukhala ngati fumbi nawamwaza ngati mankhusu ndi uta wake.
מי העיר ממזרח צדק יקראהו לרגלו יתן לפניו גוים ומלכים ירד--יתן כעפר חרבו כקש נדף קשתו
3 Amawalondola namayenda mosavutika, mʼnjira imene mapazi ake sanayendemo kale.
ירדפם יעבור שלום ארח ברגליו לא יבוא
4 Ndani anachita zimenezi ndi kuzitsiriza, si uja amene anayambitsa mitundu ya anthu? Ine Yehova, ndine chiyambi ndipo potsiriza pake ndidzakhalapo.”
מי פעל ועשה קרא הדרות מראש אני יהוה ראשון ואת אחרנים אני הוא
5 Mayiko amʼmbali mwa nyanja aona zimenezi ndipo akuopa; anthu a ku mathero a dziko lapansi akunjenjemera. Akuyandikira pafupi, akubwera;
ראו איים ויראו קצות הארץ יחרדו קרבו ויאתיון
6 aliyense akuthandiza mnzake ndipo akuwuza mʼbale wake kuti, “Limba mtima!”
איש את רעהו יעזרו ולאחיו יאמר חזק
7 Mʼmisiri wa matabwa amalimbikitsa mʼmisiri wa golide, ndipo iye amene amasalaza fano ndi nyundo amalimbikitsa amene amalisanja pa chipala. Ponena za kuwotcherera iye amati, “Zili bwino.” Iye amalikhomerera fanolo ndi misomali kuti lisagwe.
ויחזק חרש את צרף מחליק פטיש את הולם פעם אמר לדבק טוב הוא ויחזקהו במסמרים לא ימוט
8 “Koma Iwe Israeli mtumiki wanga, Yakobo amene ndakusankha, Ndiwe chidzukulu cha Abrahamu bwenzi langa.
ואתה ישראל עבדי יעקב אשר בחרתיך זרע אברהם אהבי
9 Ndinakutengani kuchokera ku mapeto a dziko lapansi, ndinakuyitanani kuchokera ku mbali za kutali za dziko lapansi. Ine ndinati, ‘Iwe ndiwe mtumiki wanga;’ Ndinakusankha ndipo sindinakutaye.
אשר החזקתיך מקצות הארץ ומאציליה קראתיך ואמר לך עבדי אתה בחרתיך ולא מאסתיך
10 Tsono usaope, pakuti Ine ndili nawe; usataye mtima chifukwa Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu ndipo ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
אל תירא כי עמך אני אל תשתע כי אני אלהיך אמצתיך אף עזרתיך--אף תמכתיך בימין צדקי
11 “Onse amene akupsera mtima adzachita manyazi ndithu ndi kunyazitsidwa; onse amene akukangana nawe sadzakhalanso kanthu, adzawonongeka.
הן יבשו ויכלמו כל הנחרים בך יהיו כאין ויאבדו אנשי ריבך
12 Udzafunafuna adani ako, koma sadzapezeka. Iwo amene akuchita nawe nkhondo sadzakhalanso kanthu.
תבקשם ולא תמצאם אנשי מצתך יהיו כאין וכאפס אנשי מלחמתך
13 Pakuti Ine Yehova, ndine Mulungu wako, amene ndikukugwira dzanja lako lamanja ndipo ndikuti, usaope; ndidzakuthandiza.
כי אני יהוה אלהיך--מחזיק ימינך האמר לך אל תירא אני עזרתיך
14 Usachite mantha, iwe Yakobo wofowoka ngati nyongolotsi, iwe wochepa mphamvu Israeli, chifukwa Ine ndidzakuthandiza,” akutero Yehova Mpulumutsi wako, Woyerayo wa Israeli.
אל תיראי תולעת יעקב מתי ישראל אני עזרתיך נאם יהוה וגאלך קדוש ישראל
15 “Taona, ndidzakusandutsa ngati chipangizo chopunthira tirigu chatsopano, chakunthwa ndi cha mano ambiri. Udzanyenya mapiri ndi kuwaphwanyaphwanya, ndipo zitunda adzazisandutsa ngati mankhusu.
הנה שמתיך למורג חרוץ חדש--בעל פיפיות תדוש הרים ותדק וגבעות כמץ תשים
16 Udzawapeta ndipo adzawuluka ndi mphepo komanso adzamwazika ndi kamvuluvulu. Koma iwe udzakondwera chifukwa Ine ndine Mulungu wako, ndipo udzanyadira chifukwa cha Ine Woyerayo wa Israeli:
תזרם ורוח תשאם וסערה תפיץ אותם ואתה תגיל ביהוה בקדוש ישראל תתהלל
17 “Pamene amphawi ndi osauka akufunafuna madzi, koma sakuwapeza; ndipo kummero kwawo kwawuma ndi ludzu. Ine Yehova ndidzayankha pemphero lawo; Ine, Mulungu wa Israeli, sindidzawasiya.
העניים והאביונים מבקשים מים ואין--לשונם בצמא נשתה אני יהוה אענם אלהי ישראל לא אעזבם
18 Ndidzayendetsa mitsinje mʼmalo owuma, ndi akasupe adzatumphuka mu zigwa. Ndidzasandutsa chipululu kukhala dziwe la madzi ndipo dziko lowuma kukhala akasupe a madzi.
אפתח על שפיים נהרות ובתוך בקעות מעינות אשים מדבר לאגם מים וארץ ציה למוצאי מים
19 Mʼchipululu ndidzameretsa mkungudza, kasiya mchisu ndi mtengo wa Olivi. Mʼdziko lowuma ndidzaza mitengo ya payini, ya mkuyu ndi ya mlombwa,
אתן במדבר ארז שטה והדס ועץ שמן אשים בערבה ברוש תדהר ותאשור--יחדו
20 kuti anthu aone ndi kudziwa; inde, alingalire ndi kumvetsa, kuti Yehova ndiye wachita zimenezi; kuti Woyera wa Israeli ndiye anakonza zimenezi.
למען יראו וידעו וישימו וישכילו יחדו--כי יד יהוה עשתה זאת וקדוש ישראל בראה
21 “Yehova akuwuza milungu ina kuti, ‘Fotokozani mlandu wanu.’ Mfumu ya Yakobo ikuti, ‘Perekani umboni wanu.’
קרבו ריבכם יאמר יהוה הגישו עצמותיכם יאמר מלך יעקב
22 Bwerani ndi milungu yanu kuti idzatiwuze zomwe zidzachitike mʼtsogolo. Tifotokozereni zinthu zamakedzana tiziganizire ndi kudziwa zotsatira zake. Kapena tiwuzeni zimene zidzachitike mʼtsogolo,
יגישו ויגידו לנו את אשר תקרינה הראשנות מה הנה הגידו ונשימה לבנו ונדעה אחריתן או הבאות השמיענו
23 tiwuzeni kuti kutsogolo kuli zotani, ndipo ife tidziwa kuti ndinu milungu. Chitani chinthu chabwino kapena choyipa, ndipo mutidabwitsa ndi kutichititsa mantha.
הגידו האתיות לאחור ונדעה כי אלהים אתם אף תיטיבו ותרעו ונשתעה ונרא (ונראה) יחדו
24 Koma inu sindinu kanthu ndipo zochita zanu nʼzopandapake; amene amapembedza inu ali ngati chinthu chokanidwa chifukwa ndi choyipa.
הן אתם מאין ופעלכם מאפע תועבה יבחר בכם
25 “Ndinawutsa munthu wina kumpoto ndipo anabwera, munthu wochokera kummawa amene ndinamuyitana. Amapondaponda olamulira ngati matope, ngati ndi wowumba mbiya amene akuponda dongo.
העירותי מצפון ויאת ממזרח שמש יקרא בשמי ויבא סגנים כמו חמר וכמו יוצר ירמס טיט
26 Ndani anawululiratu zimenezi poyamba pomwe, kuti ife tidziwe, kapena kutiwuziratu zisanachitike kuti ife tinene kuti, ‘Analondola?’ Palibe amene ananena, palibe analengeza zimenezi, palibe anamva mawu anu.
מי הגיד מראש ונדעה ומלפנים ונאמר צדיק אף אין מגיד אף אין משמיע--אף אין שמע אמריכם
27 Ine ndinali woyamba kumuwuza Ziyoni kuti, ‘Taona, si awa akubwera apawa!’ Ndinatumiza mthenga wa nkhani yabwino ku Yerusalemu.
ראשון לציון הנה הנם ולירושלם מבשר אתן
28 Koma ndikayangʼana palibe ndi mmodzi yemwe, palibe ndi mmodzi yemwe pakati pawo wotha kupereka uphungu, palibe woti ayankhe pamene ine ndawafunsa.
וארא ואין איש ומאלה ואין יועץ ואשאלם וישיבו דבר
29 Taonani, milungu yonseyi ndi yachinyengo! Zochita zawo si kanthu konse; mafano awo ali ngati mphepo yachabechabe.
הן כלם און אפס מעשיהם רוח ותהו נסכיהם

< Yesaya 41 >