< Yesaya 38 >

1 Nthawi imeneyo Mfumu Hezekiya anadwala ndipo anali pafupi kufa. Mneneri Yesaya mwana wa Amozi anapita kukamuona ndipo anati “Yehova akuti: Konza bwino nyumba yako, pakuti ukufa; suchira.”
U ono se vrijeme Ezekija razbolje nasmrt. Prorok Izaija, sin Amosov, dođe mu i reče: “Ovako veli Jahve: 'Uredi kuću svoju, jer ćeš umrijeti, nećeš ozdraviti.'”
2 Hezekiya anatembenuka nayangʼana kukhoma, napemphera kwa Yehova kuti,
Ezekija se okrenu zidu i ovako se pomoli Jahvi:
3 “Inu Yehova, kumbukirani momwe ndayendera pamaso panu mokhulupirika ndi modzipereka ndipo ndakhala ndikuchita zabwino pamaso panu.” Ndipo Hezekiya analira mosweka mtima.
“Ah, Jahve, sjeti se da sam pred tobom hodio vjerno i poštena srca i učinio što je dobro u tvojim očima.” I Ezekija briznu u gorak plač.
4 Ndipo Yehova analamula Yesaya kuti:
Tada dođe riječ Jahvina Izaiji:
5 “Pita kwa Hezekiya ndipo ukamuwuze kuti, ‘Yehova, Mulungu wa kholo lake Davide akuti: Ndamva pemphero lako ndipo misozi yako ndayiona; ndidzakuwonjezera zaka 15 pa moyo wako.
“Idi i reci Ezekiji: Ovako kaže Jahve, Bog oca tvoga Davida: 'Uslišao sam tvoju molitvu, vidio tvoje suze. Izliječit ću te; za tri dana uzići ćeš u Dom Jahvin. Dodat ću tvome vijeku petnaest godina.
6 Ndipo ndidzakupulumutsa, iwe pamodzi ndi mzindawu mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya, Ine ndidzawuteteza mzindawu.
Izbavit ću tebe i ovaj grad iz ruku asirskoga kralja. Jest, zakrilit ću ovaj grad!'”
7 “‘Ichi ndi chizindikiro cha Yehova kwa iwe kutsimikiza kuti Yehova adzachita zimene walonjeza:
Izaija odgovori: “Evo ti znaka od Jahve da će učiniti što je rekao:
8 Chithunzithunzi chimene dzuwa likuchititsa pa makwerero a Ahazi ndidzachibweza mʼmbuyo makwerero khumi.’” Ndipo chithunzithunzi chinabwerera mʼmbuyo makwerero khumi.
sjenu koja je sišla po stupnjevima Ahazova sunčanika vratit ću za deset stupnjeva natrag.” I vrati se sunce deset stupnjeva natrag po stupnjevima po kojima bijaše već sišlo.
9 Ndakatulo ya Hezekiya mfumu ya ku Yuda imene analemba atadwala ndi kuchira:
Pjesan Ezekije, kralja judejskoga, kada se razbolio pa ozdravio od svoje bolesti:
10 Ine ndinaganiza kuti ndidzapita ku dziko la akufa pamene moyo ukukoma. (Sheol h7585)
“Govorio sam: U podne dana svojih ja moram otići. Na vratima Podzemlja mjesto mi je dano za ostatak mojih ljeta. (Sheol h7585)
11 Ndinaganiza kuti, “Sindidzaonanso Yehova, mʼdziko la anthu amoyo, sindidzaonanso mtundu wa anthu kapena kukhala pamodzi ndi amene amakhala pa dziko lapansi lino.
Govorio sam: Vidjet više neću Jahve na zemlji živih, vidjet više neću nikoga od stanovnika ovog svijeta.
12 Nyumba yanga yasasuka ndipo yachotsedwa. Ngati tenti ya mʼbusa mwapindapinda moyo wanga, ngati munthu wowomba nsalu; kuyambira usana mpaka usiku mwakhala mukundisiya.
Stan je moj razvrgnut, bačen daleko, kao šator pastirski; poput tkalca moj si život namotao da bi me otkinuo od osnove. Od jutra do noći skončat ćeš me,
13 Ndinkalira kupempha chithandizo usiku wonse mpaka mmawa; koma Inu Yehova munaphwanya mafupa anga ngati mkango, ndipo mwakhala mukundisiya.
vičem sve do jutra; kao što lav mrska kosti moje, od jutra do noći skončat ćeš me.
14 Ndinkalira ngati namzeze kapena chumba, ndinkabuwula ngati nkhunda yodandaula. Maso anga anatopa nʼkuyangʼana mlengalenga. Inu Ambuye, ine ndili mʼmavuto bwerani mudzandithandize!”
Poput laste ja pijučem, zapomažem kao golubica, uzgor mi se okreću oči, zauzmi se, jamči za me.
15 Koma ine ndinganene chiyani? Yehova wayankhula nane, ndipo Iye ndiye wachita zimenezi. Chifukwa cha kuwawa kwa mtima wanga, ine ndidzayenda modzichepetsa masiku amoyo wanga onse.
Kako ću mu govoriti i što ću mu reći? TÓa on je koji djeluje. Slavit ću te sva ljeta svoja, premda s gorčinom u duši.
16 Ambuye, masiku anga ali mʼmanja mwanu. Mzimu wanga upeza moyo mwa Inu. Munandichiritsa ndi kundikhalitsa ndi moyo.
Gospodine, za tebe živjet će srce moje i živjet će moj duh. Ti ćeš me izliječiti i vratiti mi život,
17 Ndithudi, ine ndinamva zowawa zotere kuti ndikhale ndi moyo; Inu munandisunga kuti ndisapite ku dzenje la chiwonongeko chifukwa mwakhululukira machimo anga onse.
bolest će mi se pretvorit' u zdravlje. Ti si spasio dušu moju od jame uništenja, za leđa si bacio sve moje grijehe.
18 Pakuti akumanda sangathe kukutamandani, akufa sangayimbe nyimbo yokutamandani. Iwo amene akutsikira ku dzenje sangakukhulupirireni. (Sheol h7585)
Jer Podzemlje ne slavi te, ne hvali te Smrt; oni koji padnu u rupu u tvoju se vjernost više ne uzdaju. (Sheol h7585)
19 Amoyo, amoyo okha ndiwo amakutamandani, monga mmene ndikuchitira ine lero lino; abambo amawuza ana awo za kukhulupirika kwanu.
Živi, živi, jedino on te slavi kao ja danas. Otac naučava sinovima tvoju vjernost.
20 Yehova watipulumutsa. Tiyeni tiyimbe ndi zoyimbira za zingwe masiku onse a moyo wathu mʼNyumba ya Yehova.
U pomoć mi, Jahve priteci, i mi ćemo pjevati uz harfe sve dane svojega života pred Hramom Jahvinim.”
21 Yesaya anati, “Anthu atenge mʼbulu wankhunyu ndipo apake pa chithupsacho ndipo Hezekiya adzachira.”
Izaija naloži: “Donesite oblog od smokava, privijte mu ga na čir i on će ozdraviti.”
22 Hezekiya nʼkuti atafunsa kuti, “Kodi chizindikiro chako nʼchiyani chotsimikiza kuti ndidzapita ku Nyumba ya Yehova?”
Ezekija upita: “Po kojem ću znaku prepoznati da ću uzići u Dom Jahvin?”

< Yesaya 38 >