< Yesaya 35 >
1 Chipululu ndi dziko lopanda madzi zidzasangalala; dziko lowuma lidzakondwa ndi kuchita maluwa.
2 Dzikolo lidzakhala ndi maluwa ochuluka lidzasangalala kwambiri ndi kufuwula mwachimwemwe. Lidzakhala ndi ulemerero monga wa ku mapiri a ku Lebanoni, maonekedwe ake wokongola adzakhala ngati a ku Karimeli ndi a ku Saroni. Aliyense adzaona ulemerero wa Yehova, ukulu wa Mulungu wathu.
3 Limbitsani manja ofowoka, limbitsani mawondo agwedegwede;
4 nenani kwa a mitima yamantha kuti; “Limbani mtima, musachite mantha; Mulungu wanu akubwera, akubwera kudzalipsira; ndi kudzabwezera chilango adani anu; akubwera kudzakupulumutsani.”
5 Pamenepo maso a anthu osaona adzapenyanso ndipo makutu a anthu osamva adzatsekuka.
6 Anthu olumala adzalumpha ngati mbawala, ndipo osayankhula adzayimba mokondwera. Akasupe adzatumphuka mʼchipululu ndipo mitsinje idzayenda mʼdziko lowuma,
7 mchenga wotentha udzasanduka dziwe, nthaka yowuma idzasanduka ya akasupe. Pamene panali mbuto ya ankhandwe padzamera udzu ndi bango.
8 Ndipo kumeneko kudzakhala msewu waukulu; ndipo udzatchedwa Msewu Wopatulika. Anthu odetsedwa sadzayendamo mʼmenemo; zitsiru sizidzasochera mʼmenemo.
9 Kumeneko sikudzakhala mkango, ngakhale nyama yolusa sidzafikako; sidzapezeka konse kumeneko. Koma okhawo amene Yehova anawapulumutsa adzayenda mu msewu umenewu.
10 Iwo amene Yehova anawawombola adzabwerera. Adzalowa mu mzinda wa Ziyoni akuyimba; kumeneko adzakondwa mpaka muyaya. Adzakutidwa ndi chisangalalo ndi chimwemwe, ndipo chisoni ndi kudandaula zidzatheratu.