< Yesaya 33 >

1 Tsoka kwa iwe, iwe wowonongawe, amene sunawonongedwepo! Tsoka kwa iwe, iwe mthirakuwiri, iwe amene sunanyengedwepo! Iwe ukadzaleka kuwononga, udzawonongedwa, ukadzasiya umʼthirakuwiri, adzakuwononga, ndipo ukadzaleka kuchita zachinyengo adzakunyenga.
禍哉,你這不受侵害而侵害人,不受劫掠而劫掠人的人!當你侵害完了,你將遭受別人的侵害;當你劫掠完了,你將遭受別人的劫掠。
2 Inu Yehova, mutikomere mtima ife; tikulakalaka Inu. Tsiku ndi tsiku mutitchinjirize ndi mkono wanu, ndipo mutipulumutse pa nthawi ya masautso.
上主啊!憐恤我們罷!我們仰望你,每日清晨,請作我們的臂膊!在窘迫時,請作我們的救援!
3 Mukatulutsa liwu lanu longa bingu mitundu ya anthu imathawa; pamene Inu mwadzambatuka mitundu ya anthu imabalalika.
叫囂的聲音一響,民眾遂即逃遁;你一奮起,萬民便都潰散。
4 Zofunkha za ku nkhondo za mitundu ina Aisraeli adzazisonkhanitsa ngati mmene limachitira dzombe. Iwo adzalumphira zofunkhazo monga mmene limachitira dzombe.
人們收集掠物,有如拾取蚱蜢;急於劫掠,有如蝗蟲疾跳。
5 Yehova wakwezeka kwambiri pakuti amakhala pamwamba pa zonse adzadzaza Ziyoni ndi chilungamo ndi chipulumutso.
上主是崇高的,因為他居於高處;他以正義和公平充盈了熙雍。
6 Iye adzakupatsani mtendere pa nthawi yanu, adzakupatsani chipulumutso chochuluka, nzeru zambiri ndi chidziwitso chochuluka; kuopa Yehova ngati madalitso.
他是你命運的保障,得救的府庫、智慧和明智;敬畏上主, 將是你的寶藏。
7 Taonani, anthu awo amphamvu akulira mofuwula mʼmisewu; akazembe okhazikitsa mtendere akulira kwambiri.
看哪!傳信的的人在外號叫,和平使者悲痛啼哭。
8 Mʼmisewu yayikulu mulibe anthu, mʼmisewu mulibe anthu a paulendo. Mdaniyo ndi wosasunga pangano. Iye amanyoza mboni. Palibe kulemekezana.
大路已經荒廢,行旅已經絕跡。他撕毀了盟約,藐視了證人,不顧及任何人。
9 Dziko likulira ndipo likunka likutha. Nkhalango ya Lebanoni ikuchita manyazi, yafota. Chigwa cha chonde cha Saroni chasanduka chachidalala. Masamba a mitengo ya ku Basani ndi Karimeli akuyoyoka.
地域悽慘頹廢,黎巴嫩慚赧憔悴,沙龍變成荒野,巴商和加爾默耳搖曳凋零。
10 Yehova akunena kuti, “Tsopano ndidzadzambatuka ndipo ndidzaonetsa mphamvu zanga, ndipo ndidzakwezedwa.
上主說:「現在我要起來,現在我要奮發,現在我要受尊崇!
11 Zolingalira zanu nʼzachabechabe ngati udzu wamanyowa. Mpweya wamoto udzakupserezani.
你們所懷的是枯草,所生的是碎湝;我的氣息有如火燄,必將你們焚盡!
12 Anthu a mitundu ina adzatenthedwa ngati miyala ya njereza; ndi ngati minga yodulidwa.”
萬民將被焚燒,有如石灰,又如斬斷的荊棘燬於火中。
13 Inu amene muli kutali, imvani zimene ndachita; inu amene muli pafupi, dziwani mphamvu zanga
遠方的人要聽到我的作為,近處的人要嘗試我的能力!」
14 Mu mzinda wa Ziyoni anthu ochimwa agwidwa ndi mantha; anthu osapembedza Mulungu akunjenjemera: Iwo akunena kuti, “Ndani wa ife angathe kukhala mʼmoto wonyeketsa? Ndani wa ife angathe kukhala moto wosatha?”
熙雍的罪人戰兢害怕,不法之徒為恐懼所攫:「我們中誰能與吞噬的烈火同居﹖我們中誰能與不滅的烈燄共處﹖」
15 Angathe kuti ndi amene amachita zolungama ndi kuyankhula zoona, amene amakana phindu lolipeza monyenga ndipo salola manja ake kulandira ziphuphu, amene amatseka makutu ake kuti angamve mawu opangana kupha anzawo ndipo amatsinzina kuti angaone zoyipa.
那行走正道,出言真誠的,鄙棄欺詐入息的,搖手不受賄賂的,充耳不聞流血陰謀的,閉眼不看邪惡的:
16 Munthu wotere ndiye adzakhale pa nsanja, kothawira kwake kudzakhala mʼmalinga a mʼmapiri. Azidzalandira chakudya chake ndipo madzi sadzamusowa.
這樣的人要居高處,巖石上的保壘將作他的保障,他的食物有人供應,他的水可得保全。
17 Nthawi imeneyo maso a ana adzaona mfumu ya maonekedwe wokongola ndi kuona dziko lotambasukira kutali.
你必要舉目瞻仰具有華美的君王,要遙望幅員廣闊的地帶。
18 Mu mtima mwanu muzidzalingalira zoopsa zinachitika kale zija: “Ali kuti mkulu wa Asilikali uja? Ali kuti wokhometsa misonkho uja? Ali kuti mkulu woyangʼanira nsanja?”
你的心追憶起已往的恐怖時,要說:「登記的人員在那裏呢﹖量銀的人員在那裏呢﹖數點城堡的人又在那裏呢﹖」
19 Simudzawaonanso anthu odzikuza aja, anthu aja achiyankhulo chosadziwika, chachilendo ndi chosamveka.
你再見不到那野蠻的民族,即言語深邃而難以領悟,說話口吃而不易理喻的民族。
20 Taonani Ziyoni, mzinda wa zikondwerero zachipembedzo chathu; maso anu adzaona Yerusalemu, mzinda wamtendere, tenti imene sidzachotsedwa, zikhomo zake sizidzazulidwa, kapena zingwe zake kuduka.
你將觀看熙雍,我們集會的城邑;你的眼將見到耶路撒冷,安全的寓所,不動搖的帳幕;她的木樁永不能拔出,她所有的繩索也不能拉斷。
21 Kumeneko Yehova adzaonetsa ulemerero wake ndipo mzindawo udzakhala kasupe wa mitsinje yayikulu. Ngalawa za zopalasa sizidzapitamo, sitima zapamadzi zikuluzikulu sizidzayendamo.
榮耀的上主在那裏將作我們的巨川大河,沒有舟楫往來其間,也沒有遊艇划過。
22 Pakuti Yehova ndi woweruza wathu, Yehova ndiye wotilamulira, Yehova ndiye mfumu yathu; ndipo ndiye amene adzatipulumutse.
它的繩索鬆弛了,沒有穩固桅杆的力量,也沒有扯起船帆的力量。
23 Zingwe za sitima zapamadzi za adani athu zamasuka, sizikutha kulimbitsa mlongoti wake, matanga ake sakutheka kutambasuka. Ngakhale tidzagawana zofunkha zochuluka kwambiri ndipo ngakhale olumala adzatenga zofunkhazo.
因為上主是我們的判官,上主是我們的立法者,上主是我們的君王,他必拯救我們。
24 Palibe ndi mmodzi yemwe wokhala mʼZiyoni adzanene kuti, “Ndikudwala” ndipo anthu onse okhala mʼmenemo machimo awo adzakhululukidwa.
那時,瞎子要分得許多戰利品,瘸子要取得擄獲物。 沒有一個居民再會說:「我病了。」住在那裏的人必將獲得罪赦。

< Yesaya 33 >