< Yesaya 32 >

1 Taonani, kudzakhala mfumu ina imene idzalamulira mwachilungamo, ndipo akalonga ake adzaweruza molungama.
הן לצדק ימלך מלך ולשרים למשפט ישרו׃
2 Munthu aliyense adzakhala ngati pothawirapo mphepo ndi malo obisalirapo namondwe, adzakhala ngati mitsinje ya mʼchipululu, ngati mthunzi wa thanthwe lalikulu la mʼdziko lowuma.
והיה איש כמחבא רוח וסתר זרם כפלגי מים בציון כצל סלע כבד בארץ עיפה׃
3 Ndipo maso a anthu openya sadzakhalanso otseka, ndipo makutu a anthu akumva adzamvetsetsa.
ולא תשעינה עיני ראים ואזני שמעים תקשבנה׃
4 Anthu a mtima wopupuluma adzadziwa ndi kuchita zinthu mofatsa, ndipo anthu ovutika kuyankhula adzayankhula mosadodoma ndi momveka.
ולבב נמהרים יבין לדעת ולשון עלגים תמהר לדבר צחות׃
5 Chitsiru sichidzatchedwanso munthu waulemu wake ndipo munthu woyipa sadzalemekezedwa.
לא יקרא עוד לנבל נדיב ולכילי לא יאמר שוע׃
6 Pakuti munthu opusa amayankhula zauchitsiru, amaganiza kuchita zoyipa: Iye amachita zoyipira Mulungu, ndipo amafalitsa zolakwika zokhudza Yehova; anjala sawapatsa chakudya ndipo aludzu sawapatsa madzi.
כי נבל נבלה ידבר ולבו יעשה און לעשות חנף ולדבר אל יהוה תועה להריק נפש רעב ומשקה צמא יחסיר׃
7 Munthu woyipa njira zake ndi zoyipanso, iye kwake nʼkulingalira zinthu zoyipa. Amalingalira zakuti awononge anthu aumphawi ndi mabodza ake ngakhale kuti waumphawiyo akuyankhula zoona.
וכלי כליו רעים הוא זמות יעץ לחבל ענוים באמרי שקר ובדבר אביון משפט׃
8 Koma munthu wolemekezeka amalingaliranso kuchita zinthu zabwino, Iye amakhazikika pa zinthu zabwinozo.
ונדיב נדיבות יעץ והוא על נדיבות יקום׃
9 Khalani maso, inu akazi amene mukungokhala wopanda kulingalira kuti kunja kulinji ndipo imvani mawu anga. Inu akazi odzitama, imvani zimene ndikunena!
נשים שאננות קמנה שמענה קולי בנות בטחות האזנה אמרתי׃
10 Pakapita chaka ndi masiku pangʼono inu akazi amatama mudzanjenjemera; chifukwa mitengo ya mphesa idzakanika ndipo zipatso sizidzaoneka.
ימים על שנה תרגזנה בטחות כי כלה בציר אסף בלי יבוא׃
11 Nthunthumirani inu okhala mosatekesekanu; ndipo njenjemerani, inu akazi omadzikhulupirira nokhanu. Vulani zovala zanu, ndipo valani ziguduli mʼchiwuno mwanu.
חרדו שאננות רגזה בטחות פשטה וערה וחגורה על חלצים׃
12 Dzigugudeni pachifuwa mwachisoni chifukwa minda yachonde, ndi mphesa yawonongeka.
על שדים ספדים על שדי חמד על גפן פריה׃
13 Mʼdziko la anthu anga mwamera minga ndi mkandankhuku. Zoona, mulilire nyumba zonse zachikondwerero ndi mzinda uno umene unali wachisangalalo.
על אדמת עמי קוץ שמיר תעלה כי על כל בתי משוש קריה עליזה׃
14 Nyumba yaufumu idzasiyidwa, mzinda waphokoso udzakhala wopanda anthu; malinga ndi nsanja zidzasanduka chipululu mpaka muyaya. Abulu adzasangalalamo ndipo ziweto zidzapezamo msipu.
כי ארמון נטש המון עיר עזב עפל ובחן היה בעד מערות עד עולם משוש פראים מרעה עדרים׃
15 Yehova adzatipatsa mzimu wake, ndipo dziko lachipululu lidzasanduka munda wachonde, ndipo munda wachonde udzakhala ngati nkhalango.
עד יערה עלינו רוח ממרום והיה מדבר לכרמל וכרמל ליער יחשב׃
16 Tsono mʼchipululu mudzakhala chiweruzo cholungama ndipo mʼminda yachonde mudzakhala chilungamo.
ושכן במדבר משפט וצדקה בכרמל תשב׃
17 Mtendere udzakhala chipatso chachilungamo; zotsatira za chilungamo zidzakhala bata ndi kudzidalira mpaka muyaya.
והיה מעשה הצדקה שלום ועבדת הצדקה השקט ובטח עד עולם׃
18 Anthu anga adzakhala mʼmidzi yamtendere, mʼnyumba zodalirika, ndi malo osatekeseka a mpumulo.
וישב עמי בנוה שלום ובמשכנות מבטחים ובמנוחת שאננות׃
19 Ngakhale nkhalango idzawonongedwa ndi matalala ndipo mzinda udzagwetsedwa mpaka pansi,
וברד ברדת היער ובשפלה תשפל העיר׃
20 inutu mudzakhala odalitsika ndithu. Mudzadzala mbewu zanu mʼmbali mwa mtsinje uliwonse, ndipo ngʼombe zanu ndi abulu anu zidzadya paliponse.
אשריכם זרעי על כל מים משלחי רגל השור והחמור׃

< Yesaya 32 >