< Yesaya 31 >
1 Tsoka kwa amene amapita ku Igupto kukapempha chithandizo, amene amadalira akavalo, nakhulupirira kuchuluka kwa magaleta awo ankhondo ndiponso mphamvu za asilikali awo okwera pa akavalo, koma sakhulupirira Woyerayo wa Israeli, kapena kupempha chithandizo kwa Yehova.
2 Komatu Yehovayo ndi wanzeru ndipo angathe kuwononga, ndipo sasintha chimene wanena. Adzalimbana ndi anthu ochita zoyipa, komanso ndi amene amathandiza anthu ochita zoyipa.
3 Aigupto ndi anthu chabe osati Mulungu; akavalo awo ndi nyama chabe osati mizimu. Yehova akangotambasula dzanja lake, amene amapereka chithandizo adzapunthwa, amene amalandira chithandizocho adzagwa; onsewo adzathera limodzi.
4 Zimene Yehova akunena kwa ine ndi izi: “Monga mkango kapena msona wamkango umabangula ukagwira nyama yake, ndipo suopsedwa kapena kusokonezeka ndi kufuwula kwa abusa amene akulimbana nayo, momwemonso palibe chingaletse Yehova Wamphamvuzonse kubwera kudzatchinjiriza phiri la Ziyoni ndi zitunda zake.
5 Monga mbalame zowuluka pamwamba pa zisa zake, Yehova Wamphamvuzonse adzatchinjiriza Yerusalemu; ndi kumupulumutsa, iye adzawupitirira ndi kuwulanditsa.”
6 Inu Aisraeli, bwererani kwa Iye amene munamuwukira kwakukulu.
7 Pakuti tsiku limenelo nonsenu mudzataya mafano anu a siliva ndi golide amene mumapanga ndi manja anu auchimo.
8 “Aasiriya adzaphedwa ku nkhondo ndi mphamvu osati za munthu. Lupanga, osati la munthu, lidzawawononga. Adzathawa ku nkhondo ndipo anyamata awo adzagwira ntchito yathangata.
9 Mfumu yawo idzamwalira ndi mantha, ndipo atsogoleri awo ankhondo adzathawa ndi mantha kusiya pambuyo mbendera yawo ya nkhondo.” Akutero Yehova, amene moto wake uli mu Ziyoni, ndipo ngʼanjo yake ili mu Yerusalemu.