< Yesaya 3 >

1 Taonani tsopano, Ambuye Yehova Wamphamvuzonse, ali pafupi kuchotsa mu Yerusalemu ndi mu Yuda zinthu pamodzi ndi thandizo; adzachotsa chakudya chonse ndi madzi onse,
כי הנה האדון יהוה צבאות מסיר מירושלם ומיהודה משען ומשענה כל משען לחם וכל משען מים
2 anthu amphamvu ndi asilikali ankhondo, oweruza ndi aneneri, anthu olosera ndi akuluakulu,
גבור ואיש מלחמה שופט ונביא וקסם וזקן
3 atsogoleri a ankhondo makumi asanu ndi anthu olemekezeka, aphungu ndi anthu amatsenga ndi akatswiri pa za kulosera.
שר חמשים ונשוא פנים ויועץ וחכם חרשים ונבון לחש
4 Ndidzawayikira anyamata kuti akhale mafumu awo; ana akhanda ndiwo adzawalamulire.
ונתתי נערים שריהם ותעלולים ימשלו בם
5 Anthu adzazunzana, munthu ndi munthu mnzake, mnansi ndi mnansi wake. Anthu wamba adzanyoza akuluakulu.
ונגש העם איש באיש ואיש ברעהו ירהבו הנער בזקן והנקלה בנכבד
6 Munthu adzagwira mʼbale wake mʼnyumba ya abambo awo, ndipo adzati, “Iwe uli nawo mwinjiro, ndiye ukhale mtsogoleri wathu; lamulira malo opasuka ano!”
כי יתפש איש באחיו בית אביו שמלה לכה קצין תהיה לנו והמכשלה הזאת תחת ידך
7 Koma tsiku limenelo mʼbale wakeyo adzafuwula kuti, “Ayi, mavuto oterewa ndilibe mankhwala ake. Ndilibe chakudya kapena chovala mʼnyumba mwanga; musasankhe ine kukhala mtsogoleri wa anthu.”
ישא ביום ההוא לאמר לא אהיה חבש ובביתי אין לחם ואין שמלה לא תשימני קצין עם
8 Yerusalemu akudzandira, Yuda akugwa; zokamba zawo ndi ntchito zawo nʼzotsutsana ndi Yehova, sakulabadira ulemerero wa Mulungu.
כי כשלה ירושלם ויהודה נפל כי לשונם ומעלליהם אל יהוה למרות עני כבודו
9 Maonekedwe a nkhope zawo amawatsutsa; amaonetsera poyera tchimo lawo ngati Sodomu; salibisa tchimo lawolo. Tsoka kwa iwo odziputira okha mavuto.
הכרת פניהם ענתה בם וחטאתם כסדם הגידו לא כחדו אוי לנפשם כי גמלו להם רעה
10 Nena kwa olungama kuti zonse zidzawayendera bwino, pakuti adzakondwera ndi phindu la ntchito zawo.
אמרו צדיק כי טוב כי פרי מעלליהם יאכלו
11 Tsoka kwa anthu oyipa! Mavuto ali pa iwo! Adzalandira malipiro a zimene manja awo anachita.
אוי לרשע רע כי גמול ידיו יעשה לו
12 Achinyamata akupondereza anthu anga, ndipo amene akuwalamulira ndi akazi. Aa, anthu anga, atsogoleri anu akukusocheretsani; akukuchotsani pa njira yanu.
עמי נגשיו מעולל ונשים משלו בו עמי מאשריך מתעים ודרך ארחתיך בלעו
13 Yehova wakhala pamalo pake mʼbwalo la milandu; wakonzeka kuti aweruze anthu ake.
נצב לריב יהוה ועמד לדין עמים
14 Yehova akuwazenga milandu akuluakulu ndi atsogoleri a anthu ake: “Ndinu amene mwawononga munda wanga wa mpesa; nyumba zanu zadzaza ndi zolanda kwa amphawi.
יהוה במשפט יבוא עם זקני עמו ושריו ואתם בערתם הכרם גזלת העני בבתיכם
15 Nʼchifukwa chiyani inu mukupsinja anthu anga, nʼkudyera masuku pamutu amphawi?” Akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse.
מלכם (מה לכם) תדכאו עמי ופני עניים תטחנו נאם אדני יהוה צבאות
16 Yehova akunena kuti, “Akazi a ku Ziyoni ngodzikuza kwambiri, akuyenda atakweza makosi awo, akukopa amuna ndi maso awo akuyenda monyangʼama akuliza zigwinjiri za mʼmiyendo yawo
ויאמר יהוה יען כי גבהו בנות ציון ותלכנה נטוות (נטויות) גרון ומשקרות עינים הלוך וטפף תלכנה וברגליהם תעכסנה
17 Nʼchifukwa chake Ambuye, adzatulutsa zipere pa mitu ya akazi a ku Ziyoniwo; Yehova adzachititsa dazi mitu yawo.”
ושפח אדני קדקד בנות ציון ויהוה פתהן יערה
18 Tsiku limenelo Ambuye adzawachotsera zodzikongoletsera zawo: za mʼmiyendo, za ku mutu za mʼkhosi,
ביום ההוא יסיר אדני את תפארת העכסים והשביסים--והשהרנים
19 ndolo ndi zibangiri, nsalu zophimba pa nkhope,
הנטפות והשירות והרעלות
20 maduku, zigwinjiri za mʼmiyendo ndi malamba, mabotolo a zonunkhira ndi zithumwa,
הפארים והצעדות והקשרים ובתי הנפש והלחשים
21 mphete ndi zipini,
הטבעות ונזמי האף
22 zovala za pa mphwando, zipewa ndi mwinjiro, zikwama,
המחלצות והמעטפות והמטפחות והחריטים
23 magalasi oyangʼanira, zovala zosalala, nduwira ndiponso nsalu za mʼmapewa.
והגלינים והסדינים והצניפות והרדידים
24 Mʼmalo mwa kununkhira azidzanunkha, mʼmalo mwa lamba, adzavala chingwe; mʼmalo mwa tsitsi lopesa bwino, adzakhala ndi dazi; mʼmalo mwa zovala zabwino, adzavala chiguduli; mʼmalo mwa kunyadira kukongola adzachita manyazi.
והיה תחת בשם מק יהיה ותחת חגורה נקפה ותחת מעשה מקשה קרחה ותחת פתיגיל מחגרת שק כי תחת יפי
25 Iwe Yerusalemu anthu ako aamuna adzaphedwa ndi lupanga, asilikali ako adzafera ku nkhondo.
מתיך בחרב יפלו וגבורתך במלחמה
26 Pa zipata za Ziyoni padzakhala kubuma ndi kulira; Iweyo udzasakazidwa nʼkukhala pansi, ukugubuduzika pa fumbi.
ואנו ואבלו פתחיה ונקתה לארץ תשב

< Yesaya 3 >