< Yesaya 29 >
1 Tsoka kwa iwe, Arieli, Arieli, mzinda umene Davide anakhazikitsamo zithando za nkhondo! Papite chaka chimodzi kapena ziwiri ndipo masiku a zikondwerero zanu azipitirirabe ndithu.
Væ Ariel, Ariel civitas, quam expugnavit David: additus est annus ad annum: sollemnitates evolutæ sunt.
2 Komatu Ine ndidzathira nkhondo Arieli ndipo kudzakhala kulira ndi kudandaula, mzindawo udzasanduka ngati ngʼanjo ya guwa lansembe.
Et circumvallabo Ariel, et erit tristis et mœrens, et erit mihi quasi Ariel.
3 Ine ndidzamanga misasa ya nkhondo kulimbana ndi mzindawo; ndidzakuzungulira ndi nsanja za nkhondo ndi kumanga mitumbira yanga ya nkhondo kulimbana nawe.
Et circumdabo quasi sphæram in circuitu tuo, et iaciam contra te aggerem, et munimenta ponam in obsidionem tuam.
4 Utagwetsedwa pansi, iwe udzayankhula kuchokera mʼnthaka, mawu ako adzatuluka uli mʼfumbi, adzamveka ngati a mzukwa. Mawu ako adzamveka ngati onongʼona kuchokera mʼfumbi.
Humiliaberis, de terra loqueris, et de humo audietur eloquium tuum: et erit quasi pythonis de terra vox tua, et de humo eloquium tuum mussitabit.
5 Koma chigulu cha adani ako chidzasanduka chifwirimbwiti. Chigulu cha ankhondo achilendo chidzabalalika ngati mungu wowuluzika ndi mphepo. Mwadzidzidzi ndi mosayembekezereka,
Et erit sicut pulvis tenuis multitudo ventilantium te: et sicut favilla pertransiens multitudo eorum, qui contra te prævaluerunt:
6 Yehova Wamphamvuzonse adzabwera ndi mabingu ndi chivomerezi ndi phokoso lalikulu, kamvuluvulu ndi namondwe ndi malawi a moto wonyeketsa.
eritque repente confestim. A Domino exercituum visitabitur in tonitruo, et commotione terræ, et voce magna turbinis et tempestatis, et flammæ ignis devorantis.
7 Tsono chigulu chankhondo cha mitundu ina yonse chimene chikulimbana ndi mzinda wa Arieli nʼkumathira nkhondo mzindawo, malinga ake ndi kuwuzinga, chigulu chonsecho chidzazimirira ngati maloto, gati zinthu zoziona mʼmasomphenya usiku.
Et erit sicut somnium visionis nocturnæ multitudo omnium Gentium, quæ dimicaverunt contra Ariel, et omnes qui militaverunt, et obsederunt, et prævaluerunt adversus eam.
8 Chidzakhala ngati munthu wanjala wolota akudya, koma podzuka ali nayobe njala; kapena ngati munthu waludzu wolota akumwa, koma podzuka, ali nalobe ludzu, kummero kwake kuli gwaa. Izi zidzachitika pamene chigulu cha nkhondo cha mitundu ina yonse chikunthira nkhondo Phiri la Ziyoni.
Et sicut somniat esuriens, et comedit, cum autem fuerit expergefactus, vacua est anima eius: et sicut somniat sitiens, et bibit, et postquam fuerit expergefactus, lassus adhuc sitit, et anima eius vacua est: sic erit multitudo omnium Gentium, quæ dimicaverunt contra montem Sion.
9 Pitirizani kuledzera ndipo mudzakhala opusa. Dzitsekeni mʼmaso ndipo mukhale osapenya, ledzerani, koma osati ndi vinyo, dzandirani, koma osati ndi mowa.
Obstupescite, et admiramini, fluctuate, et vacillate: inebriamini, et non a vino: movemini, et non ab ebrietate.
10 Yehova wakugonetsani tulo tofa nato. Watseka maso anu, inu aneneri; waphimba mitu yanu, inu alosi.
Quoniam miscuit vobis Dominus spiritum soporis, claudet oculos vestros, prophetas et principes vestros, qui vident visiones, operiet.
11 Kwa inu mawu onsewa ali ngati buku lotsekedwa, ndipo ngati lipatsidwa kwa wina wodziwa kuwerenga ndi kunena kuti, “Chonde tawerengani bukuli,” iye adzati, “Sindingathe popeza ndi lomatidwa.”
Et erit vobis visio omnium sicut verba libri signati, quem cum dederint scienti litteras, dicent: Lege istum: et respondebit: Non possum, signatus est enim:
12 Kapena ngati lipatsidwa kwa amene sadziwa kuwerenga ndi kunena kuti, “Chonde werenga bukuli,” iye adzayankha kuti, “Ine sindidziwa kuwerenga.”
Et dabitur liber nescienti litteras, diceturque ei: Lege: et respondebit: Nescio litteras.
13 Ambuye akuti, “Anthu awa amandipembedza Ine ndi pakamwa pawo, ndi kundilemekeza Ine ndi milomo yawo, koma mitima yawo ili kutali ndi Ine. Kundipembedza kwawo ndi kwa chiphamaso. Amandipembedza motsata malamulo a anthu amene anaphunzitsidwa.
Et dixit Dominus: Eo quod appropinquat populus iste ore suo, et labiis suis glorificat me, cor autem eius longe est a me, et timuerunt me mandato hominum et doctrinis:
14 Nʼchifukwa chakenso Ine ndidzapitirira kuwachitira ntchito zodabwitsa; nzeru za anthu anzeru zidzatha, luntha la anthu aluntha Ine ndidzalinyoza.”
Ideo ecce ego addam ut admirationem faciam populo huic miraculo grandi et stupendo: peribit enim sapientia a sapientibus eius, et intellectus prudentium eius abscondetur.
15 Tsoka kwa amene amayesetsa kubisira Yehova maganizo awo, amene amachita ntchito zawo mu mdima nʼkumanena kuti, “Ndani amene akundiona kapena ndani akudziwa zimene ndikuchita?”
Væ qui profundi estis corde, ut a Domino abscondatis consilium: quorum sunt in tenebris opera, et dicunt: Quis videt nos, et quis novit nos?
16 Inu mumazondotsa zinthu ngati kuti dothi lasanduka wowumba mbiya. Kodi chinthu chopangidwa chingawuze wochipanga kuti “Sunandipange ndi iwe?” Kapena mʼphika kunena kwa amene anawuwumba kuti, “Iwe sudziwa chilichonse?”
Perversa est hæc vestra cogitatio: quasi si lutum contra figulum cogitet, et dicat opus factori suo: Non fecisti me: et figmentum dicat fictori suo: Non intelligis.
17 Kodi Lebanoni posachedwapa sadzasanduka munda wachonde, ndipo kodi munda wachondewo ngati nkhalango?
Nonne adhuc in modico et in brevi convertetur Libanus in charmel, et charmel in saltum reputabitur?
18 Tsiku limenelo anthu osamva adzamva mawu a mʼbuku, ndipo anthu osaona amene ankakhala mu mdima adzapenya.
Et audient in die illa surdi verba libri, et de tenebris et caligine oculi cæcorum videbunt.
19 Anthu odzichepetsa adzakhalanso ndi chimwemwe mwa Yehova; ndipo anthu osowa adzakondwa chifukwa cha Woyerayo wa Israeli.
Et addent mites in Domino lætitiam, et pauperes homines in sancto Israel exultabunt:
20 Koma anthu ankhanza adzazimirira, oseka anzawo sadzaonekanso, ndipo onse okopeka ndi zoyipa adzawonongedwa.
quoniam defecit qui prævalebat, consummatus est illusor, et succisi sunt omnes qui vigilabant super iniquitatem:
21 Yehova adzalanga amene amasinjirira munthu kuti apezeke wolakwa, kapena kuphophonyetsa anthu ozenga mlandu ndi umboni wonama kuti osalakwa asaweruzidwe mwachilungamo.
qui peccare faciebant homines in verbo, et arguentem in porta supplantabant, et declinaverunt frustra a iusto.
22 Choncho Yehova amene anawombola Abrahamu, akunena kwa zidzukulu za Yakobo kuti, “Anthu anga sadzachitanso manyazi; nkhope zawo sizidzagwanso ndi manyazi.
Propter hoc, hæc dicit Dominus ad domum Iacob, qui redemit Abraham: Non modo confundetur Iacob, nec modo vultus eius erubescet:
23 Akadzaona ana awo ndi ntchito ya manja anga pakati pawo, adzatamanda dzina langa loyera; adzazindikira kuyera kwa Woyerayo wa Yakobo, ndipo adzachita naye mantha Mulungu wa Israeli.
sed cum viderit filios suos, opera manuum mearum in medio sui sanctificantes nomen meum, et sanctificabunt sanctum Iacob, et Deum Israel prædicabunt,
24 Anthu opusa adzapeza nzeru; onyinyirika adzalandira malangizo.”
et scient errantes spiritu intellectum, et mussitatores discent legem.