< Yesaya 27 >
1 Tsiku limenelo, Yehova ndi lupanga lake lakuthwa, lalikulu ndi lamphamvu, adzalanga Leviyatani chinjoka chothawa chija, Leviyatani chinjoka chodzikulunga; adzapha chirombo choopsa cha mʼnyanja.
2 Tsiku limenelo Yehova adzati, “Tidzayimba nyimbo ya munda wamphesa wobereka bwino:
3 Ine, Yehova, ndimawuyangʼanira; ndimawuthirira nthawi zonse. Ndimawulondera usana ndi usiku kuti wina angawononge.
4 Ine sindinakwiye. Ngati mkandankhuku ndi minga zikanaoneka ndikanalimbana nazo! Ndikachita nazo nkhondo; ndikanazitentha zonse ndi moto.
5 Koma ngati apo ayi, abweretu kwa Ine adani angawo kuti ndidzawateteze; apangane nane za mtendere, ndithu, apangane nane za mtendere.”
6 Masiku akubwerawo Yakobo adzazika mizu, Israeli adzaphukira ndi kuchita maluwa, ndipo adzadzaza dziko lonse lapansi ndi zipatso.
7 Kodi Yehova anakantha Israeli ngati momwe anakanthira anthu amene anazunza Israeli? Kapena kodi Yehova anapha Israeli ngati mmene anthu ena anaphera Israeli?
8 Yehova mwawalanga powapirikitsa ndi kuwatumiza ku ukapolo, mwawachotsa ndi mpweya wanu woopsa, monga zimachitikira pa tsiku la mkuntho wochokera kummawa.
9 Yehova adzakhululuka kulakwa kwa Yakobo. Iwo adzaonetsa kuti alapadi pamene adzaphwanya miyala yonse ya guwa lachikunja, ngati mmene anthu amaphwanyira miyala yanjereza mpaka kukhala ngati fumbi lokhalokha. Sipadzapezekanso mafano a Asera kapena maguwa ofukiza lubani.
10 Mzinda wamalinga uja wasanduka bwinja, wasanduka malo osiyidwa, ndi kutayidwa ngati chipululu; kumeneko amadyetselako ana angʼombe kumeneko zimapumulako ziweto ndi kumwetula nthambi za mitengo kotheratu.
11 Pamene nthambi za mitengoyo zauma, zimathyoka ndipo amayi amabwera nazitola ndi kuzisandutsa nkhuni. Pakuti awa ndi anthu opanda nzeru; kotero Mulungu amene anawapanga sadzachitira chisoni, ndipo Mlengi wawo sawakomera mtima.
12 Tsiku limenelo Yehova adzasonkhanitsa pamodzi anthu ake mmodzimmodzi kumalo opunthira tirigu, kuchokera ku mtsinje wa Yufurate mpaka ku mtsinje wa ku Igupto.
13 Ndipo tsiku limenelo lipenga lalikulu lidzalira. Amene akuzunzika ku Asiriya iwo amene ali ku ukapolo ku Igupto adzabwera ndi kudzalambira Yehova pa phiri lopatulika mu Yerusalemu.