< Yesaya 23 >

1 Uthenga wonena za Turo: Lirani mofuwula, inu oyendetsa sitima za pa madzi za ku Tarisisi: pakuti mzinda wa Turo wawonongedwa ndipo mulibe nyumba kapena dooko. Zimenezi anazimva pochokera ku Kitimu.
משא צר הילילו אניות תרשיש כי שדד מבית מבוא מארץ כתים נגלה למו׃
2 Khalani chete inu anthu okhala mʼmbali mwa nyanja, inu amalonda a ku Sidoni, iwe amene unalemera ndi anthu oyenda pa nyanja.
דמו ישבי אי סחר צידון עבר ים מלאוך׃
3 Pa nyanja zazikulu panabwera tirigu wa ku Sihori; zokolola za ku Nailo, ndipo munachita malonda ndi anthu a mitundu ina.
ובמים רבים זרע שחר קציר יאור תבואתה ותהי סחר גוים׃
4 Chita manyazi, iwe Sidimu pakuti nyanja yayankhula, linga la ku nyanja (Turo) layankhula kuti, “Sindinamvepo zowawa za kubereka kapena kuberekapo mwana; sindinalerepo ana aamuna kapena kulera ana aakazi.”
בושי צידון כי אמר ים מעוז הים לאמר לא חלתי ולא ילדתי ולא גדלתי בחורים רוממתי בתולות׃
5 Mawuwa akadzamveka ku Igupto, iwo adzachita mantha akadzamva kuti Turo wawonongeka.
כאשר שמע למצרים יחילו כשמע צר׃
6 Wolokerani ku Tarisisi, lirani mofuwula, inu anthu okhala mʼmbali mwa nyanja.
עברו תרשישה הילילו ישבי אי׃
7 Kodi uwu si mzinda wachisangalalo uja, mzinda wakalekale, umene anthu ake ankapita kukakhala ku mayiko akutali?
הזאת לכם עליזה מימי קדם קדמתה יבלוה רגליה מרחוק לגור׃
8 Kodi ndani anakonza zimenezi kuti zigwere Turo, mzinda umene unakhazikitsa mizinda ina, mzinda umene amalonda ake ndi akalonga ndi otchuka pa dziko lapansi?
מי יעץ זאת על צר המעטירה אשר סחריה שרים כנעניה נכבדי ארץ׃
9 Yehova Wamphamvuzonse anakonza zimenezi kuti athetse kunyada kwawo ndi kutsitsa anthu otchuka a pa dziko lapansi.
יהוה צבאות יעצה לחלל גאון כל צבי להקל כל נכבדי ארץ׃
10 Mubalalike mʼdziko mwanu ngati mtsinje wa Nailo inu anthu a ku Tarisisi, pakuti mulibenso chokutetezani.
עברי ארצך כיאר בת תרשיש אין מזח עוד׃
11 Yehova watambasula dzanja lake kuloza ku nyanja ndipo wagwedeza maufumu ake. Iye walamula kuti Kanaani agwetse malinga ake.
ידו נטה על הים הרגיז ממלכות יהוה צוה אל כנען לשמד מעזניה׃
12 Iye anati, “Simudzakondwanso konse, inu anthu opanikizidwa a ku Sidoni, tsopano wamphwanyidwa! “Ngakhale muwolokere ku Kitimu, kumeneko simukapezako mpumulo.”
ויאמר לא תוסיפי עוד לעלוז המעשקה בתולת בת צידון כתיים קומי עברי גם שם לא ינוח לך׃
13 Onani dziko la Ababuloni, anthu amenewa tsopano atheratu! Asiriya asandutsa Turo kukhala malo a zirombo za ku chipululu; anamanga nsanja zawo za nkhondo, anagumula malinga ake ndipo anawasandutsa bwinja.
הן ארץ כשדים זה העם לא היה אשור יסדה לציים הקימו בחיניו עררו ארמנותיה שמה למפלה׃
14 Lirani mofuwula, inu anthu oyendetsa sitima za pa madzi za ku Tarisisi; chifukwa malinga ako agwetsedwa!
הילילו אניות תרשיש כי שדד מעזכן׃
15 Pa nthawi imeneyo Turo adzayiwalika pa zaka 70, amene ndi masiku a moyo wa mfumu. Koma potsiriza pa zaka 70 zimenezi, Turo adzakhala ngati mkazi wachiwerewere woyimbidwa mu nyimbo:
והיה ביום ההוא ונשכחת צר שבעים שנה כימי מלך אחד מקץ שבעים שנה יהיה לצר כשירת הזונה׃
16 “Tenga zeze wako uzungulire mzinda, iwe mkazi wachiwerewere woyiwalika; imba zeze mokometsera, imba nyimbo zambiri, kuti anthu akukumbukire.”
קחי כנור סבי עיר זונה נשכחה היטיבי נגן הרבי שיר למען תזכרי׃
17 Pakutha pa zaka 70, Yehova adzachitapo kanthu pa Turo. Iye adzabwerera ku ntchito yake yakale monga mkazi wachiwerewere ndipo adzachita zachiwerewere ndi maufumu onse a dziko lapansi.
והיה מקץ שבעים שנה יפקד יהוה את צר ושבה לאתננה וזנתה את כל ממלכות הארץ על פני האדמה׃
18 Koma phindu lake ndi malipiro ake adzazipereka kwa Yehova; sadzazikundika kapena kuzisunga. Phindu lake lidzapita kwa mtumiki wa Yehova kuti agule zakudya zambiri ndi zovala zokongola.
והיה סחרה ואתננה קדש ליהוה לא יאצר ולא יחסן כי לישבים לפני יהוה יהיה סחרה לאכל לשבעה ולמכסה עתיק׃

< Yesaya 23 >