< Yesaya 22 >
1 Uthenga wonena za Chigwa cha Masomphenya: Kodi chachitika nʼchiyani, kuti nonsenu mukwere pa madenga?
論異象谷的默示: 有甚麼事使你這滿城的人都上房頂呢?
2 Iwe mzinda wodzaza ndi chisangalalo chodzaza tsaya, iwe mzinda waphokoso ndi wosokonekera? Anthu ako ophedwa aja sanaphedwe ndi lupanga, kapena kufera pa nkhondo.
你這滿處吶喊、大有喧嘩的城, 歡樂的邑啊, 你中間被殺的並不是被刀殺, 也不是因打仗死亡。
3 Atsogoleri ako onse ngakhale anathawa limodzi; koma anagwidwa osadziteteza nʼkomwe. Inu munapezeka ndipo nonse pamodzi munatengedwa ukapolo, ngakhale munathawa pamene mdani akanali patali.
你所有的官長一同逃跑, 都為弓箭手所捆綁。 你中間一切被找到的都一同被捆綁; 他們本是逃往遠方的。
4 Nʼchifukwa chake Ine ndinati, “Chokani pamaso panga; ndilekeni ndilire ndi mtima wowawa. Musayesere kunditonthoza chifukwa cha kuwonongeka kwa anthu anga.”
所以我說:你們轉眼不看我, 我要痛哭。 不要因我眾民的毀滅, 就竭力安慰我。
5 Lero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse walola kuti tione mavuto ndi kugonjetsedwa ndiponso chisokonezo mʼChigwa cha Masomphenya. Malinga agumuka, komanso anthu akanalira mofuwula ku mapiri.
因為主-萬軍之耶和華使「異象谷」 有潰亂、踐踏、煩擾的日子。 城被攻破, 哀聲達到山間。
6 Ankhondo a ku Elamu anadza pa magaleta ndi akavalo ali ndi mivi mʼmanja. Ankhondo a ku Kiri anakonzeka ndi zishango.
以攔帶着箭袋, 還有坐戰車的和馬兵; 吉珥揭開盾牌。
7 Zigwa zanu zachonde ndi zodzaza ndi magaleta, ndipo asilikali okwera pa akavalo ayikidwa pa zipata za mzinda;
你嘉美的谷遍滿戰車, 也有馬兵在城門前排列。
8 zonse zoteteza Yuda zachotsedwa. Ndipo tsiku limenelo munayangʼanayangʼana zida zankhondo zomwe zinali mʼnyumba yaufumu ya nkhalango;
他去掉猶大的遮蓋。 那日,你就仰望林庫內的軍器。
9 inu munaona kuti makoma ambiri a mzinda wa Davide anali ndi malo ambiri ogumuka; munasunga madzi mu chidziwe chakumunsi.
你們看見大衛城的破口很多,便聚積下池的水,
10 Munawerenga nyumba zonse za mu Yerusalemu ndipo munagwetsa nyumba zina kuti mulimbitse linga logumuka lija.
又數點耶路撒冷的房屋,將房屋拆毀,修補城牆,
11 Pakati pa makoma awiri munamanga chitsime chosungiramo madzi ochokera ku dziwe lakale, koma inu simunadalire Mulungu amene anapanga zimenezi, kapena kusamalako za Iye amene anazilenga kale lomwe.
又在兩道城牆中間挖一個聚水池可盛舊池的水,卻不仰望做這事的主,也不顧念從古定這事的。
12 Pa tsiku limenelo, Ambuye Yehova Wamphamvuzonse anakuyitanani kuti mulire ndi kukhetsa misozi; kumeta mutu wanu mpala ndi kuvala ziguduli.
當那日,主-萬軍之耶和華叫人哭泣哀號, 頭上光禿,身披麻布。
13 Koma mʼmalo mwake inu munakondwa ndi kusangalala; munapha ngʼombe ndi nkhosa; munadya nyama ndi kumwa vinyo. Inu mumati, “Tiyeni tidye ndi kumwa pakuti mawa tifa!”
誰知,人倒歡喜快樂, 宰牛殺羊,吃肉喝酒,說: 我們吃喝吧!因為明天要死了。
14 Yehova Wamphamvuzonse wandiwululira mondinongʼoneza kuti, “Tchimo limeneli sindidzakhululuka mpaka tsiku la kufa kwanu,” akutero Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse.
萬軍之耶和華親自默示我說: 這罪孽直到你們死,斷不得赦免! 這是主-萬軍之耶和華說的。
15 Chimene Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Pita, ukanene kwa Sabina kapitawo, amene amayangʼanira nyumba yaufumu:
主-萬軍之耶和華這樣說:「你去見掌銀庫的,就是家宰舍伯那,對他說:
16 Kodi ukuchita chiyani kuno, nanga ndani anakupatsa chilolezo kuti udzikumbire manda kuno, kudzikumbira manda pa phiri ndi kudzisemera malo opumulira mʼthanthwe?
『你在這裏做甚麼呢?有甚麼人竟在這裏鑿墳墓,就是在高處為自己鑿墳墓,在磐石中為自己鑿出安身之所?
17 “Samalira, Yehova watsala pangʼono kukugwira zolimba ndi kukuponya mwamphamvu, iwe munthu wamphamvu.
看哪,耶和華必像大有力的人,將你緊緊纏裹,竭力拋去。
18 Iye adzakukulunga kwambiri ngati mpira ndipo adzakuponyera mʼdziko lalikulu. Kumeneko ndiko ukafere ndipo kumeneko ndiko kudzatsalire magaleta ako. Ndipo udzasanduka wochititsa manyazi nyumba ya mbuye wako.
他必將你滾成一團,拋在寬闊之地,好像拋球一樣。你這主人家的羞辱,必在那裏坐你榮耀的車,也必在那裏死亡。
19 Ine ndidzakuchotsa pa ukapitawo wako ndipo ndidzakutsitsa pa udindo wako.
我必趕逐你離開官職;你必從你的原位撤下。』
20 “Tsiku limenelo ndidzayitanitsa mtumiki wanga, Eliyakimu mwana wa Hilikiya.
「到那日,我必召我僕人希勒家的兒子以利亞敬來,
21 Ndidzamuveka mkanjo wako ndi kumangira lamba wako mʼchiwuno mwake ndi kumupatsa ulamuliro wako. Iye adzakhala kholo la amene amakhala mu Yerusalemu ndiponso a fuko la Yuda.
將你的外袍給他穿上,將你的腰帶給他繫緊,將你的政權交在他手中。他必作耶路撒冷居民和猶大家的父。
22 Ndidzamupatsa ulamuliro wa banja la Davide. Adzatsekula ndipo palibe adzatseke, adzatseka popanda wina kutsekula.
我必將大衛家的鑰匙放在他肩頭上。他開,無人能關;他關,無人能開。
23 Ufumu wake udzakhala wokhazikika ngati chikhomo chokhomedwa pa malo olimba. Anthu adzalemekeza nyumba ya abale ake chifukwa cha iye.
我必將他安穩,像釘子釘在堅固處;他必作為他父家榮耀的寶座。
24 Ana ndi abale a nyumba ya abambo ake adzakhala ngati katundu pa iye ngati ziwiya zopanda ntchito zimene zapachikidwa pa chikhomo.
他父家所有的榮耀,連兒女帶子孫,都掛在他身上,好像一切小器皿,從杯子到酒瓶掛上一樣。
25 “Yehova Wamphamvuzonse akunena kuti, ‘Tsiku limeneli chikhomo chokhomedwa kwambiri chija sichidzalimbanso; chidzazuka ndipo chidzagwa ndipo zonse zopachikidwa zidzawonongedwa.’” Yehova wayankhula chomwechi.
萬軍之耶和華說:當那日,釘在堅固處的釘子必壓斜,被砍斷落地;掛在其上的重擔必被剪斷。因為這是耶和華說的。」