< Yesaya 21 >
1 Uthenga wonena za chipululu cha mʼmbali mwa Nyanja. Ankhondo a ku Elamu ndi Mediya adzabwera ngati kamvuluvulu amene akuwomba modutsa mʼmbali ya nyanja, kuchokera ku chipululu, dziko lochititsa mantha.
2 Ine ndaona zinthu zoopsa mʼmasomphenya: Wonyenga akunyenga, wofunkha akufunkha komanso owononga akuwononga. Elamu, yambani nkhondo! Mediya, zingani mzinda! Ine ndidzathetsa mavuto onse amene anayambitsa Ababuloni.
3 Chifukwa cha zimenezi thupi langa likunjenjemera ndi mantha, ndikumva ululu ngati wa mayi amene akubereka; ndikuvutika kwambiri ndi zimene ndikumva, ndathedwa nzeru ndi zimene ndikuziona.
4 Mtima wanga ukugunda, ndipo ndikunjenjemera ndi mantha; chisisira chimene ndakhala ndikuchifuna chasanduka chinthu choopsa kwa ine.
5 Ankhondo a ku Elamu ndi Mediya akukonza matebulo, akuyala mphasa, akudya komanso kumwa! Mwadzidzidzi anamva mawu akuti, “Dzukani inu ankhondo, pakani mafuta zishango zanu!”
6 Zimene Ambuye akunena kwa ine ndi izi; “Pita, kayike mlonda kuti azinena zimene akuziona.
7 Taonani, anthu akubwera ali pa akavalo ndipo akuyenda awiriawiri, okwera pa bulu kapena okwera pa ngamira, mlondayo akhale tcheru kwambiri.”
8 Ndipo mlondayo anafuwula kuti, “Ambuye anga, tsiku ndi tsiku ndimakhala pa nsanja yolondera; Usiku uliwonse ndimakhala pa malo anga olondera.
9 Taonani, uyo munthu akubwera atakwera pa galeta ali ndi gulu la akavalo. Mmodzi wa iwo akuti, ‘Babuloni wagwa, wagwa! Mafano onse a milungu yake agwa pansi ndipo aphwanyika!’”
10 Inu anthu anga opunthidwa ndi kupetedwa ngati tirigu, ine ndikukuwuzani zimene ndamva ndikukuwuzani Uthenga wochokera kwa Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli.
11 Uthenga wonena za Duma: Munthu wina akundiyitana kuchokera ku Seiri kuti, “Iwe mlonda, usikuwu utha liti? Iwe mlonda, utha liti kodi usikuwu?”
12 Mlonda akuyankha kuti, “Kukucha, koma kudanso. Ngati ukufuna kufunsa, funsa tsopano; ndipo ubwerenso udzafunse.”
13 Uthenga wonena za Arabiya: Inu anthu amalonda a ku Dedani, amene usiku mumagona mʼzithukuluzi za ku Arabiya,
14 perekani madzi kwa anthu aludzu. Inu anthu a ku Tema perekani chakudya kwa anthu othawa nkhondo.
15 Iwo akuthawa malupanga, lupanga losololedwa, akuthawa uta wokokakoka ndiponso nkhondo yoopsa.
16 Zimene Ambuye akunena kwa ine ndi izi: “Chaka chimodzi chisanathe, potsata mmene amawerengera munthu waganyu, ulemerero wonse wa Kedara udzatheratu.
17 Mwa anthu okoka uta, ankhondo a ku Kedara opulumuka adzakhala owerengeka.” Wayankhula ndi Yehova Mulungu wa Israeli.