< Yesaya 2 >
1 Nazi zinthu zokhudza Yuda ndi Yerusalemu, zimene Yesaya mwana wa Amozi anaziona mʼmasomphenya:
Esta es la visión que Isaías, hijo de Amoz, vio sobre Judá y Jerusalén.
2 Mʼmasiku otsiriza, phiri la Nyumba ya Yehova adzalikhazikitsa kukhala lalitali kuposa mapiri ena onse, lidzaonekera pamwamba pa mapiri ena onse, ndipo mayiko onse adzathamangira kumeneko.
En los últimos días, la montaña donde se levanta el Templo del Señor será conocida como la más alta de todas las montañas, elevándose por encima de otras colinas. Muchos vendrán de otras naciones para visitarla.
3 Anthu ambiri adzabwera ndikunena kuti, “Tiyeni tikwere ku phiri la Yehova, ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo. Iye adzatiphunzitsa njira zake, ndipo tidzayenda mʼnjira zakezo.” Malangizo adzachokera ku Ziyoni, mawu a Yehova adzachokera ku Yerusalemu.
La gente vendrá y dirá: “Subamos al monte del Señor, al Templo del Dios de Jacob. Allí Dios nos enseñará sus caminos y seguiremos sus indicaciones. Las enseñanzas de Dios se extenderán desde Sión, y su palabra desde Jerusalén”.
4 Iye adzaweruza pakati pa mayiko, ndipo adzathetsa kusamvana pakati pa anthu ambiri. Anthuwo adzasandutsa malupanga awo kukhala makasu ndiponso mikondo yawo kukhala zomwetera. Mtundu wina sudzatenganso lupanga kumenyana ndi mtundu wina, kapena kuphunziranso za nkhondo.
El Señor decidirá los casos de las naciones; resolverá las discusiones entre ellas. Martillarán sus espadas y las convertirán en hojas de arado, y sus lanzas en podaderas. Las naciones ya no lucharán entre sí; ya no aprenderán métodos de guerra.
5 Inu nyumba ya Yakobo, bwerani, tiyeni tiyende mʼkuwala kwa Yehova.
Vengan, israelitas, caminemos a la luz del Señor.
6 Inu Yehova mwawakana anthu anu, nyumba ya Yakobo. Iwo adzaza ndi zamatsenga zochokera Kummawa; amawombeza mawula ngati Afilisti, ndipo amayanjana ndi anthu osapembedza Mulungu.
Porque tú, Señor, has renunciado a tu pueblo, los israelitas, porque han adoptado prácticas paganas de Oriente, usan hechizos como los filisteos y se hacen amigos de los extranjeros.
7 Dziko lawo ndi lodzaza ndi siliva ndi golide; ndipo chuma chawo ndi chosatha. Dziko lawo ndi lodzaza ndi akavalo; ndipo magaleta awo ankhondo ngosawerengeka.
Su país está lleno de plata y oro, y de una riqueza infinita. Su tierra está llena de caballos; y tienen una cantidad interminable de carros.
8 Dziko lawo ndi lodzaza ndi mafano; iwo amapembedza ntchito ya manja awo, amagwadira zomwe anapanga ndi zala zawo.
Su país está lleno de ídolos; se inclinan y adoran lo que han hecho ellos mismos, producido por sus propias manos.
9 Tsono munthu aliyense adzachepetsedwa ndi kutsitsidwa. Inu Yehova musawakhululukire.
Este pueblo será abatido y humillado: ¡Señor, no los perdones!
10 Lowani mʼmatanthwe, bisalani mʼmaenje, kuthawa kuopsa kwa Yehova ndi ulemerero wa ufumu wake!
Huyan a las cuevas de las rocas, escóndanse bajo tierra de la presencia aterradora del Señor, de la gloria de su majestad.
11 Kudzikuza kwa anthu kudzatha, ndipo kudzitama kwa anthu kudzawonongedwa; Yehova yekha ndiye adzapatsidwe ulemu pa tsiku limenelo.
Los que miran con arrogancia serán abatidos; los soberbios serán humillados. En ese día sólo el Señor será exaltado.
12 Yehova Wamphamvuzonse wakonzeratu tsiku limene adzatsitse onse onyada ndi odzitama, ndipo adzagonjetsa onse amphamvu,
El Señor ha reservado un día en el que se ocupará de los orgullosos y arrogantes. Acabará con toda la altivez, y los derribará.
13 tsiku la mikungudza yonse ya ku Lebanoni, yayitali ndi yoonekera patali, ndiponso la mitengo yonse ya thundu ya ku Basani,
Derribará los cedros del Líbano, altos y elevados, y todos los grandes robles de Basán,
14 tsiku la mapiri onse ataliatali ndiponso la zitunda zonse zazitali,
Derribará los altos montes y las altas colinas.
15 tsiku la nsanja zonse zazitali ndiponso malinga onse olimba,
Derribará toda torre alta y todo muro defensivo.
16 tsiku la sitima zapamadzi zonse za ku Tarisisi ndiponso la mabwato onse okongola.
Aniquilará a todos los barcos comerciales de Tarsis, así como las embarcaciones comerciales.
17 Kudzikuza kwa munthu kudzatha ndipo kudzitama kwa anthu kudzawonongedwa, Yehova yekha ndiye adzapatsidwe ulemu tsiku limenelo,
Los arrogantes serán abatidos, y los orgullosos serán humillados. En ese día sólo el Señor será exaltado.
18 ndipo mafano onse adzatheratu.
Los ídolos desaparecerán por completo.
19 Anthu adzathawira mʼmapanga a matanthwe ndi mʼmaenje a nthaka, kuthawa mkwiyo wa Yehova, ndiponso ulemerero wa ufumu wake, pamene Iye adzuka kugwedeza dziko lapansi.
La gente huirá a las cuevas de las rocas y a los agujeros de la tierra para tratar de esconderse de la presencia aterradora del Señor, de la gloria de su majestad, cuando llegue a sacudir la tierra.
20 Tsiku limenelo anthu adzatayira mfuko ndi mileme mafano awo asiliva ndi mafano awo agolide, amene anawapanga kuti aziwapembedza.
Ese día la gente tomará los ídolos de plata y oro que construyeron para adorar y los arrojarán a las ratas y a los murciélagos.
21 Adzathawira mʼmapanga a matanthwe ndiponso mʼmingʼalu ya nthaka kuthawa mkwiyo wa Yehova ndiponso ulemerero wa ufumu wake, pamene Iye adzuka kugwedeza dziko lapansi.
Correrán a las grietas de las rocas y a las brechas de los acantilados para tratar de esconderse de la aterradora presencia del Señor, de la gloria de su majestad, cuando llegue a sacudir la tierra.
22 Lekani kudalira munthu, amene moyo wake sukhalira kutha. Iye angathandize bwanji wina aliyense?
No se molesten en confiar en los seres humanos que sólo viven por un corto tiempo. ¿Acaso qué valor tienen?