< Yesaya 19 >

1 Uthenga onena za Igupto: Taonani, Yehova wakwera pa mtambo waliwiro, ndipo akupita ku Igupto. Mafano a ku Igupto akunjenjemera pamaso pake, ndipo mitima ya Aigupto yachokamo ndi mantha.
משא מצרים הנה יהוה רכב על עב קל ובא מצרים ונעו אלילי מצרים מפניו ולבב מצרים ימס בקרבו
2 “Ine ndidzadzutsa Aigupto kuti amenyane okhaokha; mʼbale adzamenyana ndi mʼbale wake, mnansi ndi mnansi wake, mzinda ndi mzinda unzake, ndiponso ufumu ndi ufumu unzake.
וסכסכתי מצרים במצרים ונלחמו איש באחיו ואיש ברעהו עיר בעיר ממלכה בממלכה
3 Aigupto adzataya mtima popeza ndidzalepheretsa zolinga zawo; adzapempha nzeru kwa mafano awo ndiponso kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa, kwa amawula ndi kwa oyankhula ndi mizimu.
ונבקה רוח מצרים בקרבו ועצתו אבלע ודרשו אל האלילים ואל האטים ואל האבות ואל הידענים
4 Ndidzawapereka Aigupto kwa olamulira ankhanza, ndipo mfumu yoopsa idzawalamulira,” akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse.
וסכרתי את מצרים ביד אדנים קשה ומלך עז ימשל בם נאם האדון יהוה צבאות
5 Madzi a mu mtsinje wa Nailo adzaphwa, ndipo mʼmbali mwa mtsinje mudzangʼaluka ndi kuwuma.
ונשתו מים מהים ונהר יחרב ויבש
6 Ngalande zake zidzanunkha; ndipo mitsinje ya Igupto idzayamba kuchepa ndi kuwuma. Bango ndi dulu zidzafota,
והאזניחו נהרות דללו וחרבו יארי מצור קנה וסוף קמלו
7 ndiponso zomera za mʼmphepete mwa Nailo ndi ku mathiriro a mtsinjewo. Zonse zodzalidwa mʼmbali mwa Nailo zidzawuma, zidzawuluzika ndipo sizidzaonekanso.
ערות על יאור על פי יאור וכל מזרע יאור ייבש נדף ואיננו
8 Asodzi adzabuwula ndi kudandaula, onse amene amaponya mbedza mu Nailo; onse amene amaponya makoka mʼmadzi adzalira.
ואנו הדיגים ואבלו כל משליכי ביאור חכה ופרשי מכמרת על פני מים אמללו
9 Amene amagwira ntchito yopota thonje adzataya mtima, anthu oluka nsalu zofewa zabafuta adzataya chiyembekezo.
ובשו עבדי פשתים שריקות וארגים חורי
10 Akatswiri opanga nsalu adzangoti kakasi, ndipo anthu onse ogwira ntchito yolipidwa adzatheratu mphamvu.
והיו שתתיה מדכאים כל עשי שכר אגמי נפש
11 Akuluakulu a ku Zowani ndi zitsiru; aphungu a nzeru a Farao amalangiza zopusa. Kodi mungathe kunena bwanji kwa Farao kuti, “Ine ndine mmodzi mwa anthu anzeru, wophunzira wa mafumu akale?”
אך אולים שרי צען חכמי יעצי פרעה עצה נבערה איך תאמרו אל פרעה בן חכמים אני בן מלכי קדם
12 Iwe Farao, anthu ako anzeru ali kuti? Abweretu kuti akuwuze ndi kukudziwitsa zimene Yehova Wamphamvuzonse wakonza kuchitira dziko la Igupto.
אים אפוא חכמיך ויגידו נא לך וידעו מה יעץ יהוה צבאות על מצרים
13 Akuluakulu a ku Zowani asanduka zitsiru, atsogoleri a ku Mefisi anamizidwa; atsogoleri a dziko la Igupto asocheretsa anthu a dzikolo.
נואלו שרי צען נשאו שרי נף התעו את מצרים פנת שבטיה
14 Yehova wasocheretsa anthu a ku Igupto. Iwo akuchita kudzandira pa zonse zimene akuchita, ngati chidakwa choterereka pa masanzi ake.
יהוה מסך בקרבה רוח עועים והתעו את מצרים בכל מעשהו כהתעות שכור בקיאו
15 Palibe chimene munthu wa mu Igupto angachite, mtsogoleri kapena wotsatira, nthambi ya kanjedza kapena bango.
ולא יהיה למצרים מעשה אשר יעשה ראש וזנב כפה ואגמון
16 Tsiku limenelo Aigupto adzakhala ngati amayi. Adzanjenjemera ndi kuchita mantha akadzaona Yehova Wamphamvuzonse, atakweza dzanja lake kufuna kuwalanga.
ביום ההוא יהיה מצרים כנשים וחרד ופחד מפני תנופת יד יהוה צבאות אשר הוא מניף עליו
17 Ndipo dziko la Yuda lidzaopsa dziko la Aigupto. Aliyense amene adzamve dzina la Yuda adzaopsedwa chifukwa cha zimene Yehova Wamphamvuzonse wakonzekera kuchitira dziko la Igupto.
והיתה אדמת יהודה למצרים לחגא כל אשר יזכיר אתה אליו יפחד--מפני עצת יהוה צבאות אשר הוא יועץ עליו
18 Tsiku limenelo ku dziko la Igupto kudzakhala mizinda isanu yoyankhula chiyankhulo cha Akanaani, ndipo anthu ake adzalumbira kwa Yehova Wamphamvuzonse kuti adzamutumikira. Umodzi mwa mizindayo udzatchedwa Mzinda Wachilungamo.
ביום ההוא יהיו חמש ערים בארץ מצרים מדברות שפת כנען ונשבעות ליהוה צבאות עיר ההרס יאמר לאחת
19 Tsiku limenelo mʼkati mwa dziko la Igupto mudzakhala guwa lansembe la Yehova, ndipo mʼmalire mwake adzayikira Yehova mwala wachikumbutso.
ביום ההוא יהיה מזבח ליהוה בתוך ארץ מצרים ומצבה אצל גבולה ליהוה
20 Zimenezo zidzakhala umboni wozindikiritsa kuti Yehova Wamphamvuzonse alimo mʼdziko la Igupto. Pamene Aigupto adzalirira Yehova chifukwa cha owapondereza, Iye adzawatumizira mpulumutsi ndi mtetezi ndipo adzawalanditsa.
והיה לאות ולעד ליהוה צבאות בארץ מצרים כי יצעקו אל יהוה מפני לחצים וישלח להם מושיע ורב והצילם
21 Kotero Yehova adzadziulula yekha kwa Aigupto, ndipo tsiku limenelo adzadziwa Yehova. Adzapembedza Yehova popereka nsembe ndi popereka zopereka zachakudya; Adzalumbira kwa Yehova ndipo adzachita zimene alumbirazo.
ונודע יהוה למצרים וידעו מצרים את יהוה ביום ההוא ועבדו זבח ומנחה ונדרו נדר ליהוה ושלמו
22 Yehova adzakantha Aigupto ndi mliri. Iye adzawakanthadi ndipo kenaka adzawachiritsa. Aigupto adzatembenukira kwa Yehova ndipo Iye adzamva madandawulo awo ndi kuwachiritsa.
ונגף יהוה את מצרים נגף ורפוא ושבו עד יהוה ונעתר להם ורפאם
23 Tsiku limenelo kudzakhala msewu waukulu wochoka ku Igupto kupita ku Asiriya. Aasiriya adzapita ku Igupto ndi Aigupto ku Asiriya. Aigupto ndi Aasiriya adzapembedza pamodzi.
ביום ההוא תהיה מסלה ממצרים אשורה ובא אשור במצרים ומצרים באשור ועבדו מצרים את אשור
24 Tsiku limenelo Israeli adzakhala pamodzi ndi Igupto ndi Asiriya, mayiko atatuwa adzakhala dalitso pa dziko lapansi.
ביום ההוא יהיה ישראל שלישיה למצרים ולאשור ברכה בקרב הארץ
25 Yehova Wamphamvuzonse adzawadalitsa, ndi mawu awa, “Adalitsike anthu anga Aigupto, Aasiriya, ntchito ya manja anga, ndi Aisraeli osankhidwa anga.”
אשר ברכו יהוה צבאות לאמר ברוך עמי מצרים ומעשה ידי אשור ונחלתי ישראל

< Yesaya 19 >