< Yesaya 17 >

1 Uthenga wonena za Damasiko: “Taonani, mzinda wa Damasiko sudzakhalanso mzinda, koma udzasanduka bwinja.
משא דמשק הנה דמשק מוסר מעיר והיתה מעי מפלה
2 Mizinda ya Aroeri idzakhala yopanda anthu ndipo idzakhala ya ziweto, zimene zidzagona pansi popanda wina woziopseza.
עזבות ערי ערער לעדרים תהיינה ורבצו ואין מחריד
3 Ku Efereimu sikudzakhalanso linga, ndipo ku Damasiko sikudzakhalanso ufumu; Otsalira a ku Siriya adzachotsedwa ulemu monga anthu a ku Israeli,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.
ונשבת מבצר מאפרים וממלכה מדמשק ושאר ארם ככבוד בני ישראל יהיו נאם יהוה צבאות
4 “Tsiku limenelo ulemerero wa Yakobo udzazimirira; ndipo chuma chake chidzasanduka umphawi.
והיה ביום ההוא ידל כבוד יעקב ומשמן בשרו ירזה
5 Israeli adzakhala ngati munda wa tirigu umene anatsiriza kukolola. Adzakhalanso ngati munda wa mʼchigwa cha Refaimu anthu atatha kukunkha ngala za tirigu.
והיה כאסף קציר קמה וזרעו שבלים יקצור והיה כמלקט שבלים בעמק רפאים
6 Komabe Aisraeli ochepa okha ndiwo ati adzatsale monga mʼmene zimatsalira zipatso ziwiri kapena zitatu pa nthambi ya pamwamba penipeni kapena zipatso zisanu pa nthambi za mʼmunsi mwa mtengo wa olivi akawugwedeza,” akutero Yehova, Mulungu wa Israeli.
ונשאר בו עוללת כנקף זית שנים שלשה גרגרים בראש אמיר ארבעה חמשה בסעפיה פריה--נאם יהוה אלהי ישראל
7 Tsiku limenelo anthu adzayangʼana Mlengi wawo ndipo adzatembenukira kwa Woyerayo wa Israeli.
ביום ההוא ישעה האדם על עשהו ועיניו אל קדוש ישראל תראינה
8 Iwo sadzakhulupiriranso maguwa ansembe, ntchito ya manja awo, ndipo sadzadaliranso mitengo ya mafano a Asera, ndiponso maguwa ofukizirapo lubani amene manja awo anapanga.
ולא ישעה אל המזבחות מעשה ידיו ואשר עשו אצבעתיו לא יראה והאשרים והחמנים
9 Tsiku limenelo mizinda yawo yamphamvu, imene anasiya chifukwa cha Aisraeli, idzakhala ngati malo osiyidwa kuti awirire ndi kumera ziyangoyango. Ndipo yonse idzakhala mabwinja.
ביום ההוא יהיו ערי מעוזו כעזובת החרש והאמיר אשר עזבו מפני בני ישראל והיתה שממה
10 Inu mwayiwalatu Mulungu Mpulumutsi wanu; simunakumbukire Thanthwe, linga lanu. Choncho, ngakhale munadzala mbewu zabwino, ndi kuyitanitsa kunja mitengo ya mpesa,
כי שכחת אלהי ישעך וצור מעזך לא זכרת על כן תטעי נטעי נעמנים וזמרת זר תזרענו
11 nimuyembekeza kuti zikule tsiku lomwelo ndi kuphukira maluwa mmawa mwake, komabe zimenezi sizidzakupindulirani pa tsiku la mavuto.
ביום נטעך תשגשגי ובבקר זרעך תפריחי נד קציר ביום נחלה וכאב אנוש
12 Aa, mkokomo wa anthu a mitundu yambiri, akusokosa ngati kukokoma kwa nyanja! Aa, phokoso la anthu a mitundu ina, akusokosa ngati mkokomo wa madzi amphamvu!
הוי המון עמים רבים כהמות ימים יהמיון ושאון לאמים כשאון מים כבירים ישאון
13 Ngakhale ankhondo a mitundu ina akubwera ndi mkokomo ngati wa madzi ambiri, koma adzathawira kutali Mulungu akadzawadzudzula. Yehova adzawapirikitsa ngati mankhusu owuluka ndi mphepo pa phiri, ndi ngati fumbi la kamvuluvulu asanayambe.
לאמים כשאון מים רבים ישאון וגער בו ונס ממרחק ורדף כמץ הרים לפני רוח וכגלגל לפני סופה
14 Pofika nthawi yamadzulo zoopsa zidzayamba kuchitika, ndipo zidzakhala zitatha pofika mmawa. Izi ndizo zidzachitikire anthu otilanda zinthu, gawo la amene amatibera zinthu zathu.
לעת ערב והנה בלהה בטרם בקר איננו זה חלק שוסינו וגורל לבזזינו

< Yesaya 17 >