< Yesaya 16 >

1 Anthu a ku Mowabu atumiza mphatso za ana ankhosa onenepa, kuchokera ku Sela kudutsa chipululu mpaka kukafika ku phiri la Ziyoni.
שִׁלְחוּ־כַ֥ר מֹשֵֽׁל־אֶ֖רֶץ מִסֶּ֣לַע מִדְבָּ֑רָה אֶל־הַ֖ר בַּת־צִיּֽוֹן׃
2 Monga momwe mbalame zimawulukira uku ndi uku akazimwaza mʼchisa, momwemonso akazi a ku Mowabu akuyendayenda ku madooko a Arinoni.
וְהָיָ֥ה כְעוֹף־נוֹדֵ֖ד קֵ֣ן מְשֻׁלָּ֑ח תִּֽהְיֶ֙ינָה֙ בְּנ֣וֹת מוֹאָ֔ב מַעְבָּרֹ֖ת לְאַרְנֽוֹן׃
3 Amowabu aja anawuza a ku Yuda kuti, “Tiwuzeni chochita, gamulani zoti tichite. Inu mutiteteze kwa adani anthu. Mukhale ngati mthunzi wathu dzuwa lili pa liwombo. Mutibise, musatipereke ife othawa nkhondo kwa adani athu.
הָבִ֤יאִי עֵצָה֙ עֲשׂ֣וּ פְלִילָ֔ה שִׁ֧יתִי כַלַּ֛יִל צִלֵּ֖ךְ בְּת֣וֹךְ צָהֳרָ֑יִם סַתְּרִי֙ נִדָּחִ֔ים נֹדֵ֖ד אַל־תְּגַלִּֽי׃
4 Lolani kuti anthu othawa nkhondo a ku Mowabu azikhala pakati panu; mukhale populumukira pawo kwa wowonongayo.” Nthawi idzafika ndipo wozunzayo sadzakhalaponso, kuwononga kudzaleka; waukaliyo adzachoka mʼdzikomo.
יָג֤וּרוּ בָךְ֙ נִדָּחַ֔י מוֹאָ֛ב הֱוִי־סֵ֥תֶר לָ֖מוֹ מִפְּנֵ֣י שׁוֹדֵ֑ד כִּֽי־אָפֵ֤ס הַמֵּץ֙ כָּ֣לָה שֹׁ֔ד תַּ֥מּוּ רֹמֵ֖ס מִן־הָאָֽרֶץ׃
5 Mpando waufumu udzakhazikitsidwa mwachikondi; mmodzi mwa zidzukulu za Davide adzakhalapo mokhulupirika. Iyeyo poweruza adzatsata chilungamo ndipo adzalimbikitsa kuchita zachilungamo.
וְהוּכַ֤ן בַּחֶ֙סֶד֙ כִּסֵּ֔א וְיָשַׁ֥ב עָלָ֛יו בֶּאֱמֶ֖ת בְּאֹ֣הֶל דָּוִ֑ד שֹׁפֵ֛ט וְדֹרֵ֥שׁ מִשְׁפָּ֖ט וּמְהִ֥ר צֶֽדֶק׃
6 Tinamva kuti Mowabu anadzikuza kwambiri. Kunyada kwawo ndi kunyogodola kwawo ndi kudzitama kwawo, zonse ndi zopanda phindu.
שָׁמַ֥עְנוּ גְאוֹן־מוֹאָ֖ב גֵּ֣א מְאֹ֑ד גַּאֲוָת֧וֹ וּגְאוֹנ֛וֹ וְעֶבְרָת֖וֹ לֹא־כֵ֥ן בַּדָּֽיו׃ ס
7 Nʼchifukwa chake Amowabu akulira kwambiri; iwo akulirira dziko lawo. Akubuma momvetsa chisoni chifukwa cha makeke a mphesa a ku Kiri Hareseti.
לָכֵ֗ן יְיֵלִ֥יל מוֹאָ֛ב לְמוֹאָ֖ב כֻּלֹּ֣ה יְיֵלִ֑יל לַאֲשִׁישֵׁ֧י קִיר־חֲרֶ֛שֶׂת תֶּהְגּ֖וּ אַךְ־נְכָאִֽים׃
8 Minda ya ku Hesiboni yauma, minda ya mpesa ya ku Sibina yaguga. Atsogoleri a mitundu ina anapondaponda minda ya mpesa wabwino, imene nthambi zake zinakafika ku Yazeri, mpaka kutambalalira ku chipululu. Mizu yake inakafika mpaka ku tsidya la nyanja.
כִּ֣י שַׁדְמוֹת֩ חֶשְׁבּ֨וֹן אֻמְלָ֜ל גֶּ֣פֶן שִׂבְמָ֗ה בַּעֲלֵ֤י גוֹיִם֙ הָלְמ֣וּ שְׂרוּקֶּ֔יהָ עַד־יַעְזֵ֥ר נָגָ֖עוּ תָּ֣עוּ מִדְבָּ֑ר שְׁלֻ֣חוֹתֶ֔יהָ נִטְּשׁ֖וּ עָ֥בְרוּ יָֽם׃
9 Kotero Ine ndikulira, monga mmene akulirira anthu a ku Yazeri, chifukwa cha minda ya mpesa ya ku Sibima. Inu anthu a ku Hesiboni, inu anthu a ku Eleali, ndikukunyowetsani ndi misozi! Mwalephera kupeza zokolola, chifukwa cha nkhondo imene inawononga zokolola zonse.
עַל־כֵּ֡ן אֶבְכֶּ֞ה בִּבְכִ֤י יַעְזֵר֙ גֶּ֣פֶן שִׂבְמָ֔ה אֲרַיָּ֙וֶךְ֙ דִּמְעָתִ֔י חֶשְׁבּ֖וֹן וְאֶלְעָלֵ֑ה כִּ֧י עַל־קֵיצֵ֛ךְ וְעַל־קְצִירֵ֖ךְ הֵידָ֥ד נָפָֽל׃
10 Chimwemwe ndi chisangalalo zalekeka ku minda yanu ya zipatso; palibe amene akuyimba kapena kufuwula mʼminda ya mpesa; palibe amene akupsinya vinyo ku malo opsinyira mphesa, pakuti ndathetsa kufuwula.
וְנֶאֱסַ֨ף שִׂמְחָ֤ה וָגִיל֙ מִן־הַכַּרְמֶ֔ל וּבַכְּרָמִ֥ים לֹֽא־יְרֻנָּ֖ן לֹ֣א יְרֹעָ֑ע יַ֗יִן בַּיְקָבִ֛ים לֹֽא־יִדְרֹ֥ךְ הַדֹּרֵ֖ךְ הֵידָ֥ד הִשְׁבַּֽתִּי׃
11 Chifukwa chake moyo wanga ukulira ngati pangwe kulirira Mowabu, mtima wanga ukubuwula chifukwa cha Kiri Hareseti.
עַל־כֵּן֙ מֵעַ֣י לְמוֹאָ֔ב כַּכִּנּ֖וֹר יֶֽהֱמ֑וּ וְקִרְבִּ֖י לְקִ֥יר חָֽרֶשׂ׃
12 Ngakhale anthu a ku Mowabu apite ku malo awo achipembedzo koma amangodzitopetsa ndi kutaya nthawi chabe chifukwa sizidzatheka.
וְהָיָ֧ה כִֽי־נִרְאָ֛ה כִּֽי־נִלְאָ֥ה מוֹאָ֖ב עַל־הַבָּמָ֑ה וּבָ֧א אֶל־מִקְדָּשׁ֛וֹ לְהִתְפַּלֵּ֖ל וְלֹ֥א יוּכָֽל׃
13 Awa ndi mawu amene Yehova wayankhula kale zokhudza Mowabu.
זֶ֣ה הַדָּבָ֗ר אֲשֶׁ֨ר דִּבֶּ֧ר יְהוָ֛ה אֶל־מוֹאָ֖ב מֵאָֽז׃
14 Koma tsopano Yehova akuti, “Zisanathe zaka zitatu, potsata mʼmene munthu waganyu amawerengera, ulemerero wa Mowabu udzakhala utatheratu ndipo anthu ake ambiri adzakhala atawonongeka, ndipo opulumuka ake adzakhala ochepa ndi ofowoka.”
וְעַתָּ֗ה דִּבֶּ֣ר יְהוָה֮ לֵאמֹר֒ בְּשָׁלֹ֤שׁ שָׁנִים֙ כִּשְׁנֵ֣י שָׂכִ֔יר וְנִקְלָה֙ כְּב֣וֹד מוֹאָ֔ב בְּכֹ֖ל הֶהָמ֣וֹן הָרָ֑ב וּשְׁאָ֥ר מְעַ֛ט מִזְעָ֖ר ל֥וֹא כַבִּֽיר׃ ס

< Yesaya 16 >