< Yesaya 15 >

1 Uthenga wonena za Mowabu: Popeza kuti mu usiku umodzi wokha mzinda wa Ari wa ku Mowabu wawonongedwa, wawonongedwa pa usiku umodzi wokha. Mzinda wa Kiri wawonongedwa, wawonongedwa pa usiku umodzi wokha.
משא מואב כי בליל שדד ער מואב נדמה--כי בליל שדד קיר מואב נדמה
2 Anthu a ku Diboni akupita ku nyumba ya milungu yawo, akupita ku malo awo achipembedzo kukalira; anthu a ku Mowabu akulirira mofuwula mzinda wa Nebo ndi wa Medeba. Mutu uliwonse wametedwa mpala, ndipo ndevu zonse zametedwa.
עלה הבית ודיבן הבמות לבכי על נבו ועל מידבא מואב ייליל--בכל ראשיו קרחה כל זקן גרועה
3 Mʼmisewu akuvala ziguduli; pa madenga ndi mʼmabwalo aliyense akulira mofuwula, misozi ili pupupu.
בחוצתיו חגרו שק על גגותיה וברחבתיה כלה ייליל ירד בבכי
4 Anthu a ku Hesiboni ndi Eleali akulira mofuwula, mawu awo akumveka mpaka ku Yahazi. Kotero asilikali a ku Mowabu akulira mofuwula, ndipo ataya mtima.
ותזעק חשבון ואלעלה עד יהץ נשמע קולם על כן חלצי מואב יריעו--נפשו ירעה לו
5 Inenso ndikulirira Mowabu; chifukwa othawa nkhondo ake akupita akulira ku chikweza cha Luluti mpaka ku Zowari ndi Egilati-Selisiya akupita akulira ku chikweza cha Luhiti, Akulira mosweka mtima pa njira yopita ku Horonaimu; akulira mosweka mtima chifukwa cha chiwonongeko chawo.
לבי למואב יזעק בריחה עד צער עגלת שלשיה כי מעלה הלוחית בבכי יעלה בו--כי דרך חורנים זעקת שבר יעערו
6 Madzi a ku Nimurimu aphwa ndipo udzu wauma; zomera zawonongeka ndipo palibe chomera chobiriwira chatsala.
כי מי נמרים משמות יהיו כי יבש חציר כלה דשא ירק לא היה
7 Kotero kuti chuma chomwe anachipeza ndi kuchisunga, achitenga kuti awoloke nacho chigwembe cha Misondozi.
על כן יתרה עשה ופקדתם--על נחל הערבים ישאום
8 Kulira kwawo kukumveka mʼdziko lonse la Mowabu; kulira kwawo kosweka mtima kukumveka mpaka ku Egilaimu ndi Beeri-Elimu.
כי הקיפה הזעקה את גבול מואב עד אגלים יללתה ובאר אילים יללתה
9 Madzi a ku Dimoni afiira ndi magazi, komabe ndidzabweretsa zina zambiri pa Dimoni, mkango woti udzagwire aliyense othawa mu Mowabu ndi aliyense wotsala mʼdzikomo.
כי מי דימון מלאו דם כי אשית על דימון נוספות--לפליטת מואב אריה ולשארית אדמה

< Yesaya 15 >