< Yesaya 14 >

1 Yehova adzachitira chifundo Yakobo; adzasankhanso Israeli ndi kuwalola kuti akhalenso mʼdziko lawo. Alendo adzabwera kudzakhala nawo ndi kudziphatika okha kukhala ngati a mʼnyumba ya Yakobo.
For the LORD will have compassion on Jacob, and will yet choose Israel, and set them in their own land. The foreigner will join himself with them, and they will unite with the house of Jacob.
2 Anthu a mitundu ina adzaperekeza a Israeli ku dziko lawo. Tsono Aisraeli adzasandutsa anthu a mitundu ina aja kukhala antchito awo aamuna ndi aakazi mʼdziko la Yehova. Ndiye kuti Aisraeli adzasandutsa akapolo anthu amene kale anali ambuye awo. Iwo adzasandutsa akapolo anthu amene kale ankawalamulira ndi kuwazunza.
The peoples will take them, and bring them to their place. The house of Israel will possess them in the LORD's land for servants and for handmaids. They will take as captives those whose captives they were; and they shall rule over their oppressors.
3 Yehova akadzakupumitsani ku zowawa ndi mavuto, ndiponso kuntchito yakalavulagaga imene ankakugwiritsani,
It will happen in the day that the LORD will give you rest from your sorrow, from your trouble, and from the hard service in which you were made to serve,
4 mudzayankhula monyogodola mfumu ya Babuloni kuti, Wopsinja uja watha! Ukali wake uja watha!
that you will take up this parable against the king of Babylon, and say, "How the oppressor has ceased. How the attacker has ceased."
5 Yehova wathyola chikwapu cha anthu oyipa, Iye waphwanya ndodo ya olamulira.
The LORD has broken the staff of the wicked, the scepter of the rulers,
6 Mfumu ya ku Babuloni inkakantha mitundu ya anthu mwaukali powamenya kosalekeza, Iyo inkagonjetsa anthu a mitundu ina mwaukali ndikuwazunza kosalekeza.
who struck the peoples in wrath with a continual stroke, who ruled the nations in anger, with a persecution that none restrained.
7 Koma tsopano mayiko onse ali pa mpumulo ndi pa mtendere; ndipo akuyimba mokondwa.
The whole earth is at rest, and is quiet. They break out song.
8 Ngakhale mitengo ya payini ndi mikungudza ya ku Lebanoni ikuyimba za iwe mokondwa ndipo ikuti, “Chigwetsedwere chako pansi, palibe wina anabwera kudzatigwetsa.”
Yes, the fir trees rejoice with you, with the cedars of Lebanon, saying, "Since you are humbled, no lumberjack has come up against us."
9 Ku manda kwatekeseka kuti akulandire ukamabwera; mizimu ya anthu akufa, aja amene anali atsogoleri a dziko lapansi, yadzutsidwa. Onse amene anali mafumu a mitundu ya anthu ayimiritsidwa pa mipando yawo. (Sheol h7585)
Sheol from beneath has moved for you to meet you at your coming. It stirs up the dead for you, even all the rulers of the earth. It has raised up from their thrones all the kings of the nations. (Sheol h7585)
10 Onse adzayankha; adzanena kwa iwe kuti, “Iwenso watheratu mphamvu ngati ife; Iwe wafanana ndi ife.”
They all will answer and ask you, "Have you also become as weak as we are? Have you become like us?"
11 Ulemerero wako wonse walowa mʼmanda, pamodzi ndi nyimbo za azeze ako; mphutsi zayalana pogona pako ndipo chofunda chako ndi nyongolotsi. (Sheol h7585)
Your pomp is brought down to Sheol, with the sound of your stringed instruments. Maggots are spread out under you, and worms cover you. (Sheol h7585)
12 Wagwa pansi bwanji kuchoka kumwamba, iwe nthanda, mwana wa mʼbandakucha! Wagwetsedwa pansi pa dziko lapansi, Iwe amene unagonjetsapo mitundu ya anthu!
How you have fallen from heaven, morning star, son of the dawn. How you are cut down to the ground, who laid the nations low.
13 Mu mtima mwako unkanena kuti, “Ndidzakwera mpaka kumwamba; ndidzakhazika mpando wanga waufumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu; ndidzakhala pa mpando waufumu pa phiri losonkhanirako, pamwamba penipeni pa phiri la kumpoto.
You said in your heart, "I will ascend into heaven. I will exalt my throne above the stars of God. I will sit on the mountain of assembly, in the far north.
14 Ndidzakwera pamwamba pa mitambo; ndidzafanana ndi Wammwambamwamba.”
I will ascend above the heights of the clouds. I will make myself like the Most High."
15 Koma watsitsidwa mʼmanda pansi penipeni pa dzenje. (Sheol h7585)
Yet you shall be brought down to Sheol, to the depths of the Pit. (Sheol h7585)
16 Anthu akufa adzakupenyetsetsa nadzamalingalira za iwe nʼkumati, “Kodi uyu ndi munthu uja anagwedeza dziko lapansi ndi kunjenjemeretsa maufumu,
Those who see you will stare at you. They will ponder you, saying, "Is this the man who made the earth to tremble, who shook kingdoms;
17 munthu amene anasandutsa dziko lonse chipululu, amene anagwetsa mizinda yake ndipo sankalola kuti anthu ogwidwa abwerere kwawo?”
who made the world like a wilderness, and overthrew its cities; who did not release his prisoners to their home?"
18 Mafumu onse a mitundu ya anthu akugona mwaulemu aliyense mʼmanda akeake.
All the kings of the nations lie in splendor, everyone in his own house.
19 Koma iwe watayidwa kunja kwa manda ako, ngati nthambi yowola ndi yonyansa. Mtembo wako waphimbidwa ndi anthu ophedwa; amene anabayidwa ndi lupanga, anatsikira mʼdzenje lamiyala ngati mtembo woponderezedwa.
But you are cast away from your tomb like an abominable branch, clothed with the slain, who are thrust through with the sword, who go down to the stones of the pit; like a dead body trodden under foot.
20 Sudzayikidwa nawo mʼmanda mwaulemu, chifukwa unawononga dziko lako ndi kupha anthu ako. Zidzukulu za anthu oyipa sizidzakumbukika nʼpangʼono pomwe.
You will not join them in burial, because you have destroyed your land. You have killed your people. The offspring of evildoers will not be mentioned forever.
21 Konzani malo woti muphere ana ake aamuna chifukwa cha machimo a makolo awo; kuti angadzuke ndi kulanda dziko lapansi ndi kulidzaza dziko lonselo ndi mizinda yawo.
Prepare for slaughter of his children because of the iniquity of their fathers, that they not rise up and possess the earth, and fill the surface of the world with cities.
22 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ine ndidzathira nkhondo mzinda wa Babuloni. Ndidzachotseratu mu Babuloni dzina lake ndi onse otsaliramo. Ndiye kuti sipadzakhala ana kapena zidzukulu,” akutero Yehova.
"I will rise up against them," says the LORD of hosts, "and cut off from Babylon name and remnant, and son and son's son," says the LORD.
23 “Ndidzawusandutsa mzindawo malo okhalamo anungu ndiponso dambo lamatope; ndidzawusesa ndi tsache lowononga,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.
"I will also make it a possession for the porcupine, and pools of water. I will sweep it with the broom of destruction," says the LORD of hosts.
24 Yehova Wamphamvuzonse walumbira kuti, “Ndithudi, monga ndaganizira ndidzachitadi choncho, ndipo monga momwe ndatsimikizira zidzakhala momwemo ndithu.
The LORD of hosts has sworn, saying, "Surely, as I have thought, so shall it happen; and as I have purposed, so shall it stand:
25 Ndidzawawononga Asiriya mʼdziko langa; ndidzawapondereza ndi mapazi pa mapiri anga; ndidzachotsa goli lawo pa anthu anga, ndipo ndidzachotsa katundu wawo pa mapewa awo.”
that I will break the Assyrian in my land, and tread him under foot on my mountains. Then his yoke will leave them, and his burden leave their shoulders.
26 Izi ndizo ndakonza kuti zichitike pa dziko lonse lapansi, ndatambasula dzanja pa anthu a mitundu yonse.
This is the plan that is determined for the whole earth. This is the hand that is stretched out over all the nations.
27 Pakuti Yehova Wamphamvuzonse watsimikiza, ndipo ndani angamuletse? Dzanja lake latambasulidwa ndipo ndani angalibweze?
For the LORD of hosts has planned, and who can stop it? His hand is stretched out, and who can turn it back?"
28 Uthenga uwu unabwera chaka chimene mfumu Ahazi anamwalira:
This burden was in the year that king Ahaz died.
29 Musakondwere inu Afilisti nonse kuti Asiriya amene anali ngati ndodo yokukanthani anathedwa; chifukwa kuchokera ku njoka yomweyi (mfumu ya Aasiriya) mudzatuluka mphiri, ndipo chipatso chake chidzakhala njoka yaliwiro ndiponso yaululu.
Do not rejoice, O Philistia, all of you, because the rod that struck you is broken; for out of the serpent's root an adder will emerge, and his fruit will be a fiery flying serpent.
30 Osaukitsitsa adzapeza chakudya ndipo amphawi adzakhala mwamtendere. Koma anthu ako ndidzawawononga ndi njala, ndipo njalayo idzapha ngakhale opulumuka ako.
The firstborn of the poor will eat, and the needy will lie down in safety; and I will kill your root with famine, and your remnant will be killed.
31 Lirani kwambiri, anthu a pa chipata! Fuwulani kwambiri, anthu a mu mzinda! Njenjemerani ndi mantha, inu Afilisti nonse! Mtambo wa utsi ukuchokera kumpoto, ndipo palibe wamantha pakati pa ankhondo ake.
Howl, gate. Cry, city. You are melted away, Philistia, all of you; for smoke comes out of the north, and there is no straggler in his ranks.
32 Kodi tidzawayankha chiyani amithenga a ku Filisitiya? “Yehova wakhazikitsa Ziyoni, ndipo mu mzinda wakewu, anthu ozunzika apeza populumukira.”
What then is one to answer the messengers of this nation? That the LORD has founded Zion, and in her the afflicted of his people will take refuge.

< Yesaya 14 >