< Yesaya 13 >

1 Uthenga onena za Babuloni umene Yesaya mwana wa Amozi anawulandira:
מַשָּׂא בָּבֶל אֲשֶׁר חָזָה יְשַֽׁעְיָהוּ בֶּן־אָמֽוֹץ׃
2 Kwezani mbendera yankhondo pa phiri loti see, muwafuwulire ankhondo; muwakodole kuti adzalowe pa zipata za anthu olemekezeka.
עַל הַר־נִשְׁפֶּה שְֽׂאוּ־נֵס הָרִימוּ קוֹל לָהֶם הָנִיפוּ יָד וְיָבֹאוּ פִּתְחֵי נְדִיבִֽים׃
3 Ine Yehova, ndalamulira ankhondo anga; ndasonkhanitsa ankhondo anga kuti akhale zida zanga zolangira amene amadzikuza ndi chipambano changa.
אֲנִי צִוֵּיתִי לִמְקֻדָּשָׁי גַּם קָרָאתִי גִבּוֹרַי לְאַפִּי עַלִּיזֵי גַּֽאֲוָתִֽי׃
4 Tamvani phokoso ku mapiri, likumveka ngati phokoso la gulu lalikulu la anthu! Tamvani phokoso pakati pa maufumu, ngati kuti mitundu ya anthu ikusonkhana pamodzi! Yehova Wamphamvuzonse akukhazika asilikali ake mokonzekera kuchita nkhondo.
קוֹל הָמוֹן בֶּהָרִים דְּמוּת עַם־רָב קוֹל שְׁאוֹן מַמְלְכוֹת גּוֹיִם נֶֽאֱסָפִים יְהֹוָה צְבָאוֹת מְפַקֵּד צְבָא מִלְחָמָֽה׃
5 Iwo akuchokera ku mayiko akutali, kuchokera kumalekezero a dziko Yehova ali ndi zida zake za nkhondo kuti adzawononge dziko la Babuloni.
בָּאִים מֵאֶרֶץ מֶרְחָק מִקְצֵה הַשָּׁמָיִם יְהֹוָה וּכְלֵי זַעְמוֹ לְחַבֵּל כׇּל־הָאָֽרֶץ׃
6 Lirani mofuwula, pakuti tsiku la Yehova layandikira; lidzabwera ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuzonse.
הֵילִילוּ כִּי קָרוֹב יוֹם יְהֹוָה כְּשֹׁד מִשַּׁדַּי יָבֽוֹא׃
7 Zimenezi zinafowoketsa manja onse, mtima wa munthu aliyense udzachokamo.
עַל־כֵּן כׇּל־יָדַיִם תִּרְפֶּינָה וְכׇל־לְבַב אֱנוֹשׁ יִמָּֽס׃
8 Anthu adzagwidwa ndi mantha aakulu, zowawa ndi masautso zidzawagwera; adzamva zowawa zonga amamva mayi pobereka. Adzayangʼanana mwamantha, nkhope zawo zikufiira ngati malawi amoto.
וְֽנִבְהָלוּ ׀ צִירִים וַֽחֲבָלִים יֹֽאחֵזוּן כַּיּוֹלֵדָה יְחִילוּן אִישׁ אֶל־רֵעֵהוּ יִתְמָהוּ פְּנֵי לְהָבִים פְּנֵיהֶֽם׃
9 Taonani, tsiku la Yehova likubwera, tsiku lopanda chisoni, lawukali ndi lamkwiyo; kudzasandutsa dziko kuti likhale chipululu ndi kuwononga anthu ochimwa a mʼmenemo.
הִנֵּה יוֹם־יְהֹוָה בָּא אַכְזָרִי וְעֶבְרָה וַחֲרוֹן אָף לָשׂוּם הָאָרֶץ לְשַׁמָּה וְחַטָּאֶיהָ יַשְׁמִיד מִמֶּֽנָּה׃
10 Nyenyezi zakumwamba ndiponso zonse zamlengalenga sizidzaonetsa kuwala kwawo. Dzuwa lidzada potuluka, ndipo mwezi sudzawala konse.
כִּֽי־כוֹכְבֵי הַשָּׁמַיִם וּכְסִילֵיהֶם לֹא יָהֵלּוּ אוֹרָם חָשַׁךְ הַשֶּׁמֶשׁ בְּצֵאתוֹ וְיָרֵחַ לֹֽא־יַגִּיהַּ אוֹרֽוֹ׃
11 Ndidzalanga dziko lonse chifukwa cha zolakwa zake, anthu oyipa ndidzawalanga chifukwa cha machimo awo. Ndidzathetsa kunyada kwa odzikuza, ndipo ndidzatsitsa kudzitukumula kwa anthu ankhanza.
וּפָקַדְתִּי עַל־תֵּבֵל רָעָה וְעַל־רְשָׁעִים עֲוֺנָם וְהִשְׁבַּתִּי גְּאוֹן זֵדִים וְגַאֲוַת עָרִיצִים אַשְׁפִּֽיל׃
12 Ndidzasandutsa anthu kukhala ovuta kupeza kuposa mmene amasowera golide wabwino. Iwo sazidzapezekapezeka kuposa mmene amasowera golide wa ku Ofiri.
אוֹקִיר אֱנוֹשׁ מִפָּז וְאָדָם מִכֶּתֶם אוֹפִֽיר׃
13 Tsono ndidzagwedeza miyamba ndipo dziko lapansi lidzachoka pa maziko ake. Izi zidzachitika chifukwa cha ukali wa Wamphamvuzonse pa tsiku la mkwiyo wake woopsa.
עַל־כֵּן שָׁמַיִם אַרְגִּיז וְתִרְעַשׁ הָאָרֶץ מִמְּקוֹמָהּ בְּעֶבְרַת יְהֹוָה צְבָאוֹת וּבְיוֹם חֲרוֹן אַפּֽוֹ׃
14 Ngati mbawala zosakidwa, ngati nkhosa zopanda wozikusa, munthu aliyense adzabwerera kwa anthu akwawo, aliyense adzathawira ku dziko lake.
וְהָיָה כִּצְבִי מֻדָּח וּכְצֹאן וְאֵין מְקַבֵּץ אִישׁ אֶל־עַמּוֹ יִפְנוּ וְאִישׁ אֶל־אַרְצוֹ יָנֽוּסוּ׃
15 Aliyense amene atadzapezeke ndi kugwidwa adzaphedwa momubaya ndi lupanga.
כׇּל־הַנִּמְצָא יִדָּקֵר וְכׇל־הַנִּסְפֶּה יִפּוֹל בֶּחָֽרֶב׃
16 Ana awo akhanda adzaphwanyidwa iwo akuona; nyumba zawo zidzafunkhidwa ndipo akazi awo adzagwiriridwa.
וְעֹלְלֵיהֶם יְרֻטְּשׁוּ לְעֵינֵיהֶם יִשַּׁסּוּ בָּתֵּיהֶם וּנְשֵׁיהֶם (תשגלנה) [תִּשָּׁכַֽבְנָה]׃
17 Taona, Ine ndidzadzutsa Amedi amene safuna siliva ndipo sasangalatsidwa ndi golide, kuti amenyane ndi Ababuloni.
הִנְנִי מֵעִיר עֲלֵיהֶם אֶת־מָדָי אֲשֶׁר־כֶּסֶף לֹא יַחְשֹׁבוּ וְזָהָב לֹא יַחְפְּצוּ־בֽוֹ׃
18 Adzapha anyamata ndi mauta awo; sadzachitira chifundo ana ngakhale kumvera chisoni ana akhanda.
וּקְשָׁתוֹת נְעָרִים תְּרַטַּשְׁנָה וּפְרִי־בֶטֶן לֹא יְרַחֵמוּ עַל־בָּנִים לֹא־תָחוּס עֵינָֽם׃
19 Babuloni, ufumu wake ndi waulemerero kuposa mafumu onse. Anthu ake amawunyadira. Koma Yehova adzawuwononga ngati mmene anawonongera Sodomu ndi Gomora.
וְהָיְתָה בָבֶל צְבִי מַמְלָכוֹת תִּפְאֶרֶת גְּאוֹן כַּשְׂדִּים כְּמַהְפֵּכַת אֱלֹהִים אֶת־סְדֹם וְאֶת־עֲמֹרָֽה׃
20 Anthu sadzakhalamonso kapena kukhazikikamo pa mibado yonse; palibe Mwarabu amene adzayimike tenti yake, palibe mʼbusa amene adzawetamo ziweto zake.
לֹא־תֵשֵׁב לָנֶצַח וְלֹא תִשְׁכֹּן עַד־דּוֹר וָדוֹר וְלֹא־יַהֵל שָׁם עֲרָבִי וְרֹעִים לֹא־יַרְבִּצוּ שָֽׁם׃
21 Koma nyama zakuthengo ndizo zidzakhale kumeneko, nyumba zake zidzadzaza ndi nkhandwe; mu mzindamo muzidzakhala akadzidzi, ndipo atonde akuthengo azidzalumphalumphamo.
וְרָבְצוּ־שָׁם צִיִּים וּמָלְאוּ בָתֵּיהֶם אֹחִים וְשָׁכְנוּ שָׁם בְּנוֹת יַעֲנָה וּשְׂעִירִים יְרַקְּדוּ־שָֽׁם׃
22 Mu nsanja zake muzidzalira afisi, mʼnyumba zake zokongola muzidzalira nkhandwe. Nthawi yake yayandikira ndipo masiku ake ali pafupi kutha.
וְעָנָה אִיִּים בְּאַלְמְנוֹתָיו וְתַנִּים בְּהֵיכְלֵי עֹנֶג וְקָרוֹב לָבוֹא עִתָּהּ וְיָמֶיהָ לֹא יִמָּשֵֽׁכוּ׃

< Yesaya 13 >