< Yesaya 10 >

1 Tsoka kwa anthu amene amapanga malamulo opanda chilungamo, kwa iwo amene amalemba zongovutitsa anzawo,
Ole wao wawekao sheria zisizo za haki, kwa wale watoao amri za kuonea,
2 kuwalanda anthu osauka ufulu wawo ndi kumana chilungamo osautsidwa pakati pa anthu anga, amalanda zinthu za akazi amasiye ndi kubera ana amasiye.
kuwanyima maskini haki zao na kuzuilia haki za watu wangu walioonewa, kuwafanya wajane mawindo yao na kuwanyangʼanya yatima.
3 Kodi mudzatani pa tsiku la chilango, pofika chiwonongeko chochokera kutali? Kodi mudzathawira kwa yani kuti akuthandizeni? Nanga chuma chanu mudzachisiya kuti?
Mtafanya nini siku ya kutoa hesabu, wakati maafa yatakapokuja kutoka mbali? Mtamkimbilia nani awape msaada? Mtaacha wapi mali zenu?
4 Kudzatsala nʼkungozolika mwamanyazi pakati pa anthu ogwidwa kapena kufa pamodzi ndi ophedwa. Komabe pa zonsezi mkwiyo wake sunawachokere, mkono wake uli chitambasulire.
Hakutasalia kitu chochote, isipokuwa kujikunyata miongoni mwa mateka, au kuanguka miongoni mwa waliouawa. Hata kwa haya yote, hasira yake haijageukia mbali, mkono wake bado umeinuliwa juu.
5 “Tsoka kwa mfumu ya ku Asiriya, chikwapu cha mkwiyo wanga, iye ndiye ndodo ya mkwiyo wanga!
“Ole kwa Ashuru, fimbo ya hasira yangu, ambaye mkononi mwake ana rungu ya ghadhabu yangu!
6 Ndidzamutuma kukalimbana ndi mtundu wosapembedza Mulungu, ndidzamutumiza kukalimbana ndi anthu amene amandikwiyitsa Ine, kukafunkha ndi kulanda chuma, ndi kuwapondereza pansi ngati matope a mʼmisewu.
Ninamtuma dhidi ya taifa lisilomjua Mungu, ninamtuma dhidi ya taifa linalonikasirisha, kukamata mateka na kunyakua nyara, pia kuwakanyaga chini kama matope ya barabarani.
7 Koma izi si zimene akufuna kukachita, izi si zimene zili mʼmaganizo mwake; cholinga chake ndi kukawononga, kukapulula mitundu yambiri ya anthu.
Lakini hili silo analokusudia, hili silo alilo nalo akilini; kusudi lake ni kuangamiza, kuyakomesha mataifa mengi.
8 Iye akuti, ‘Kodi atsogoleri anga ankhondo si mafumu okhaokha?’
Maana asema, ‘Je, wafalme wote si majemadari wangu?
9 ‘Kodi Kalino sanagonjetsedwe monga Karikemesi? Kodi Hamati sali ngati Aripadi, nanga Samariya sali ngati Damasiko?
Je, Kalno hakutendwa kama Karkemishi? Hamathi si kama Arpadi, nayo Samaria si kama Dameski?
10 Dzanja langa linakantha maufumu a anthu opembedza mafano, mafumu amene mafano awo ndi aakulu kupambana Yerusalemu ndi Samariya;
Kama vile mkono wangu ulivyotwaa falme za sanamu, falme ambazo vinyago vyao vilizidi vile vya Yerusalemu na Samaria:
11 nanga Ine nʼkulephera kodi kuwononga Yerusalemu pamodzi ndi mafano ake monga ndinakanthira Samariya pamodzi ndi mafano ake?’”
je, nisiishughulikie Yerusalemu na sanamu zake kama nilivyoshughulikia Samaria na vinyago vyake?’”
12 Ambuye akadzamaliza ntchito yonse yolanga phiri la Ziyoni ndi Yerusalemu adzalanganso mfumu ya ku Asiriya chifukwa cha kudzitama ndi kunyada kwake.
Bwana atakapokuwa amemaliza kazi yake yote dhidi ya Mlima Sayuni na Yerusalemu, atasema, “Nitamwadhibu mfalme wa Ashuru kwa ajili ya majivuno ya ukaidi wa moyo wake na kutazama kwa macho yenye dharau.”
13 Pakuti mfumuyo ikuti, “‘Ndachita zimenezi ndi dzanja langa, ndiponso ndi nzeru zanga, chifukwa ndine wozindikira zinthu. Ndinachotsa malire a mitundu ya anthu, ndinafunkha chuma chawo; ndinagonjetsa mafumu awo monga munthu wamphamvu.
Kwa kuwa anasema: “‘Kwa nguvu za mkono wangu nimefanya hili, kwa hekima yangu, kwa sababu nina ufahamu. Niliondoa mipaka ya mataifa, niliteka nyara hazina zao, kama yeye aliye shujaa niliwatiisha wafalme wao.
14 Dzanja langa lagwira chuma cha mitundu ya anthu ngati momwe munthu amagwirira chisa cha mbalame, ngati momwe anthu amatolera mazira osiyidwa, motero inenso ndinasonkhanitsa mayiko onse; palibe mbalame imene inakupiza mapiko ake, kapena kuyasama kukamwa kuti ilire.’”
Kama mtu atiavyo mkono kwenye kiota, ndivyo mkono wangu ulivyochukua utajiri wa mataifa; kama watu wakusanyavyo mayai yaliyoachwa, ndivyo nilivyokusanya nchi zote; wala hakuna hata mmoja aliyepiga bawa au kufungua kinywa chake kutoa mlio.’”
15 Kodi nkhwangwa ingathe kudzikuza kupambana woyigwiritsa ntchito, kapena macheka angathe kudzikuza kupambana wowagwiritsa ntchito? Ndiye kukhala ngati kuti chikwapu chikuzunguza munthu amene wachinyamula, kapena ngati kuti ndodo ikuopseza amene wayinyamula!
Je, shoka laweza kujigamba kuwa na nguvu zaidi kuliko yule anayelitumia, au msumeno kujisifu dhidi ya yule anayeutumia? Ni kana kwamba fimbo ingeweza kumwinua yeye aichukuaye, au mkongojo ungemwinua mwenye kuutumia!
16 Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova Wamphamvuzonse adzatumiza matenda owondetsa kwa ankhondo amphamvu; kunyada kwa mfumuyo kudzapsa ndi moto wosazima.
Kwa hiyo Bwana, Bwana Mwenye Nguvu Zote, atatuma ugonjwa wa kudhoofisha kwa askari wake walio hodari, katika fahari yake moto utawaka kama mwali wa moto.
17 Mulungu, Kuwala kwa Israeli, adzakhala ngati moto, Woyera uja wa Israeli adzakhala ngati malawi a moto. Motowo udzawatentha ndi kuwapsereza ngati minga ndi mkandankhuku pa tsiku limodzi.
Nuru ya Israeli itakuwa moto, Aliye Mtakatifu wao mwali wa moto; katika siku moja utaunguza na kuteketeza miiba na michongoma yake.
18 Ankhondo ake adzawonongedwa ngati nkhalango yayikulu ndi ngati nthaka yachonde.
Fahari ya misitu yake na mashamba yenye rutuba utateketeza kabisa, kama vile mtu mgonjwa adhoofikavyo.
19 Mitengo yotsalira ya mʼnkhalango zake idzakhala yochepa kwambiri, yoti ndi mwana yemwe ndi kuyiwerenga.
Nayo miti inayobaki katika misitu yake itakuwa michache sana hata mtoto mdogo angeweza kuihesabu.
20 Tsiku limenelo otsalira a ku Israeli, opulumuka a nyumba ya Yakobo, sadzadaliranso anthu amene anawakantha, koma adzadalira Yehova, Woyerayo wa Israeli.
Katika siku ile, mabaki ya Israeli, walionusurika wa nyumba ya Yakobo, hawatamtegemea tena yeye aliyewapiga, lakini watamtegemea kwa kweli Bwana Aliye Mtakatifu wa Israeli.
21 Otsalira adzabwerera, otsalira a Yakobo adzabwerera kwa Mulungu Wamphamvu.
Mabaki watarudi, mabaki wa Yakobo watamrudia Mungu Mwenye Nguvu.
22 Iwe Israeli, ngakhale anthu ako achuluke ngati mchenga wa ku nyanja, otsala okha ndiwo adzabwerere. Chiwonongeko chalamulidwa, chidzaonetsa chilungamo chosefukira.
Ingawa watu wako, ee Israeli, ni wengi kama mchanga wa pwani, ni mabaki yao tu watakaorudi. Maangamizi yamekwisha amriwa, ni mengi tena ni haki.
23 Ambuye Yehova Wamphamvuzonse adzawononga ndithu dziko lonse monga momwe analamulira.
Bwana, Bwana Mwenye Nguvu Zote, atatekeleza maangamizi yaliyoamriwa juu ya nchi yote.
24 Nʼchifukwa chake, Ambuye Yehova Wamphamvuzonse akunena kuti, “Inu anthu anga okhala mu Ziyoni, musawaope Asiriya, amene amakukanthani ndi ndodo nakumenyani ndi zibonga monga mmene Igupto anachitira.
Kwa hiyo, hili ndilo Bwana, Bwana Mwenye Nguvu Zote asemalo: “Enyi watu wangu mkaao Sayuni, msiwaogope Waashuru, wanaowapiga ninyi kwa fimbo na kuinua rungu dhidi yenu, kama Misri ilivyofanya.
25 Patsala pangʼonongʼono kuti mkwiyo wanga uchoke pa inu ndipo ndidzaonetsa ukali wanga pa iwo mpaka kuwawononga.”
Bado kitambo kidogo sana hasira yangu dhidi yenu itakoma, na ghadhabu yangu itaelekezwa kwenye maangamizi yao.”
26 Yehova Wamphamvuzonse adzawakwapula ndi chikwapu, monga momwe anakwapulira Amidiyani ku thanthwe la Orebu; ndipo adzatukula ndodo yake pa madzi ndikuwalanga monga analangira Igupto pa nyanja.
Bwana Mwenye Nguvu Zote atawachapa kwa mjeledi, kama alivyowapiga Wamidiani katika mwamba wa Orebu, naye atainua fimbo yake juu ya maji, kama alivyofanya huko Misri.
27 Tsiku limenelo katundu wawo adzachotsedwa pa mapewa anu, goli lawo lidzachoka mʼkhosi mwanu; golilo lidzathyoka chifukwa cha kunenepa kwambiri.
Katika siku hiyo mzigo wao utainuliwa kutoka mabegani mwenu, na nira yao kutoka shingoni mwenu; nira itavunjwa kwa sababu ya kutiwa mafuta.
28 Adani alowa mu Ayati apyola ku Migironi; asunga katundu wawo ku Mikimasi.
Wanaingia Ayathi, wanapita katikati ya Migroni, wanahifadhi mahitaji huko Mikmashi.
29 Adutsa pa mpata uja, ndipo akuti, “Tikagona ku Geba” Rama akunjenjemera; Gibeya, mzinda wa Saulo ukuthawa.
Wanavuka kivukoni, nao wanasema, “Tutapiga kambi huko Geba usiku kucha.” Rama inatetemeka; Gibea ya Sauli inakimbia.
30 Lilani mokweza, inu anthu a ku Galimu! Tchera khutu, iwe Laisa! Iwe Anatoti wosauka!
Piga kelele, ee Binti Galimu! Sikiliza, ee Laisha! Maskini Anathothi!
31 Anthu a ku Madimena akuthawa; anthu a ku Gebimu bisalani.
Madmena inakimbia; watu wa Gebimu wanajificha.
32 Lero lomwe lino adaniwo adzayima ku Nobu; adzagwedeza mikono yawo, kuopseza anthu a ku Ziyoni, pa phiri la Yerusalemu.
Siku hii ya leo watasimama Nobu; watatikisa ngumi zao kwa mlima wa Binti Sayuni, kwa kilima cha Yerusalemu.
33 Taonani, Ambuye Yehova Wamphamvuzonse, adzadula mwamphamvu nthambi za mitengo, mitengo yodzikweza idzadulidwa, mitengo yayitali idzagwetsedwa.
Tazama, Bwana, Bwana Mwenye Nguvu Zote, atayakata matawi kwa nguvu kuu. Miti mirefu sana itaangushwa, ile mirefu itashushwa chini.
34 Yehova adzadula ndi nkhwangwa mitengo ya mʼnkhalango yowirira; Lebanoni adzagwa pamaso pa Wamphamvu.
Atakata vichaka vya msitu kwa shoka; Lebanoni itaanguka mbele zake yeye Mwenye Nguvu.

< Yesaya 10 >