< Hoseya 9 >
1 Iwe Israeli, usakondwere; monga imachitira mitundu ina. Pakuti wakhala wosakhulupirika kwa Mulungu wako; umakonda malipiro a chiwerewere pa malo aliwonse opunthira tirigu.
Noli lætari Israel, noli exultare sicut populi: quia fornicatus es a Deo tuo, dilexisti mercedem super omnes areas tritici.
2 Malo opunthira tirigu ndi malo opsinyira mphesa sadzadyetsa anthu; adzasowa vinyo watsopano.
Area et torcular non pascet eos, et vinum mentietur eis.
3 Sadzakhalanso mʼdziko la Yehova. Efereimu adzabwerera ku Igupto ndipo mudzadya chakudya chodetsedwa ku Asiriya.
Non habitabunt in terra Domini: reversus est Ephraim in Ægyptum, et in Assyriis pollutum comedit.
4 Iwo sadzaperekanso chopereka cha chakumwa kwa Yehova, kapena nsembe zawo kuti akondweretse Yehovayo. Nsembe zotere zidzakhala kwa iwo ngati chakudya cha anamfedwa; onse akudya chakudya chimenechi adzakhala odetsedwa. Chakudya ichi chidzakhala chodya okha, sichidzalowa mʼnyumba ya Yehova.
Non libabunt Domino vinum, et non placebunt ei: sacrificia eorum quasi panis lugentium. omnes, qui comedent eum, contaminabuntur: quia panis eorum animæ ipsorum, non intrabit in domum Domini.
5 Kodi mudzachita chiyani pa tsiku la maphwando anu oyikika; pa masiku a zikondwerero za Yehova?
Quid facietis in die sollemni, in die festivitatis Domini?
6 Ngakhale iwo atathawa chiwonongeko, Igupto adzawasonkhanitsa, ndipo Mefisi adzawayika mʼmanda. Khwisa adzamera pa ziwiya zawo zasiliva, ndipo minga idzamera mʼmatenti awo.
Ecce enim profecti sunt a vastitate: Ægyptus congregabit eos, Memphis sepeliet eos: desiderabile argentum eorum urtica hereditabit, lappa in tabernaculis eorum.
7 Masiku achilango akubwera, masiku obwezera ali pafupi. Israeli adziwe zimenezi. Chifukwa machimo anu ndi ochuluka kwambiri ndipo udani wanu pa Mulungu ndi waukulu kwambiri. Mneneri amamuyesa chitsiru, munthu wanzeru za kwa Mulungu ngati wamisala.
Venerunt dies visitationis, venerunt dies retributionis: scitote Israel stultum prophetam, insanum virum spiritualem, propter multitudinem iniquitatis tuæ, et multitudinem amentiæ.
8 Mneneri pamodzi ndi Mulungu wanga ndiwo alonda a Efereimu, koma mneneri amutchera misampha mʼnjira zake zonse, ndipo udani ukumudikira mʼnyumba ya Mulungu wake.
Speculator Ephraim cum Deo meo: propheta laqueus ruinæ factus est super omnes vias eius, insania in domo Dei eius.
9 Iwo azama mu zachinyengo monga masiku a Gibeya. Mulungu adzakumbukira zolakwa zawo ndipo adzawalanga chifukwa cha machimo awo.
Profunde peccaverunt, sicut in diebus Gabaa: recordabitur iniquitatis eorum, et visitabit peccata eorum.
10 “Pamene ndinamupeza Israeli zinali ngati kupeza mphesa mʼchipululu. Nditaona makolo anu, zinali ngati ndikuona nkhuyu zoyambirira kupsa. Koma atafika ku Baala Peori, anadzipereka ku fano lija lochititsa manyazi ndipo anakhala onyansa ngati chinthu chimene anachikondacho.
Quasi uvas in deserto inveni Israel: quasi prima poma ficulneæ in cacumine eius vidi patres eorum: ipsi autem intraverunt ad Beelphegor, et abalienati sunt in confusionem, et facti sunt abominabiles sicut ea, quæ dilexerunt.
11 Ulemerero wa Efereimu udzawuluka ngati mbalame. Sipadzakhalanso kubereka ana, kuyembekezera kapena kutenga pathupi.
Ephraim quasi avis avolavit, gloria eorum a partu, et ab utero, et a conceptu.
12 Ngakhale atalera ana ndidzachititsa kuti mwana aliyense amwalire. Tsoka kwa anthuwo pamene Ine ndidzawafulatira!
Quod et si enutrierint filios suos, absque liberis eos faciam in hominibus: sed et væ eis cum recessero ab eis.
13 Ndaona Efereimu ngati Turo, atadzalidwa pa nthaka ya chonde. Koma Efereimu adzatsogolera ana ake kuti akaphedwe.”
Ephraim, ut vidi, Tyrus erat fundata in pulchritudine: et Ephraim educet ad interfectorem filios suos.
14 Inu Yehova, muwapatse. Kodi mudzawapatsa chiyani? Apatseni mimba yomangopita padera ndi mawere owuma.
Da eis Domine. Quid dabis eis? Da eis vulvam sine liberis, et ubera arentia.
15 “Chifukwa cha zoyipa zawo zonse ku Giligala, Ine ndinawada kumeneko. Chifukwa cha machitidwe awo auchimo, ndidzawapirikitsa mʼnyumba yanga. Sindidzawakondanso; atsogoleri awo onse ndi owukira.
Omnes nequitiæ eorum in Galgal, quia ibi exosos habui eos: propter malitiam adinventionum eorum de domo mea eiiciam eos: non addam ut diligam eos, omnes principes eorum recedentes.
16 Efereimu wathedwa, mizu yake yauma sakubalanso zipatso. Ngakhale atabereka ana, Ine ndidzapha ana awo okondedwawo.”
Percussus est Ephraim, radix eorum exsiccata est: fructum nequaquam facient. Quod et si genuerint, interficiam amantissima uteri eorum.
17 Mulungu wanga adzawakana chifukwa sanamumvere Iye; adzakhala oyendayenda pakati pa anthu a mitundu ina.
Abiiciet eos Deus meus, quia non audierunt eum: et erunt vagi in nationibus.