< Hoseya 7 >
1 Pamene ndichiritsa Israeli, machimo a Efereimu amaonekera poyera ndiponso milandu ya Samariya sibisika. Iwo amachita zachinyengo, mbala zimathyola nyumba, achifwamba amalanda anthu katundu mʼmisewu.
わたしがイスラエルをいやすとき、エフライムの不義と、サマリヤの悪しきわざとは現れる。彼らは偽りをおこない、内では盗びとが押し入り、外では山賊の群れが襲いきたる。
2 Koma sazindikira kuti Ine ndimakumbukira zoyipa zawo zonse. Azunguliridwa ndi zolakwa zawo; ndipo sizichoka mʼmaso mwanga.
しかし、彼らはわたしが彼らのすべての悪を覚えていることを悟らない。今、そのわざは彼らを囲んで、わたしの顔の前にある。
3 “Anthuwa amasangalatsa mfumu ndi zoyipa zawozo, akalonga amasekerera mabodza awo.
彼らはその悪をもって王を喜ばせ、その偽りをもって君たちを喜ばせる。
4 Onsewa ndi anthu azigololo, otentha ngati moto wa mu uvuni, umene wophika buledi sasonkhezera kuyambira pamene akukanda buledi mpaka atafufuma.
彼らはみな姦淫を行う者で、パンを焼く者が熱くする炉のようだ。パンを焼く者は、ねり粉をこねてから、それがふくれるまで、しばらく、火をおこす事をしないだけだ。
5 Pa tsiku la chikondwerero cha mfumu yathu akalonga amaledzera ndi vinyo, ndipo amalowa mʼgulu la anthu achipongwe.
われわれの王の日に、つかさたちは酒の熱によって病みわずらい、王はあざける者と共に手を伸べた。
6 Mitima yawo ili ngati uvuni; amayandikira Mulungu mwachiwembu. Ukali wawo umanyeka usiku wonse, mmawa umayaka ngati malawi a moto.
彼らは陰謀をもってその心を炉のように燃やす。その怒りは夜通しくすぶり、朝になると炎のように燃える。
7 Onsewa ndi otentha ngati uvuni, amapha olamulira awo. Mafumu awo onse amagwa, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amandiyitana Ine.
彼らは皆、炉のように熱くなって、そのさばきびとを焼き滅ぼす。そのもろもろの王は皆たおれる。彼らの中にはわたしを呼ぶ者がひとりもない。
8 “Efereimu wasakanikirana ndi mitundu ya anthu ena; Efereimu ndi buledi amene wapsa mbali imodzi.
エフライムはもろもろの民の中に入り混じる。エフライムは火にかけて、かえさない菓子である。
9 Alendo atha mphamvu zake, koma iye sakuzindikira. Tsitsi lake layamba imvi koma iye sakudziwa.
他国人らは彼の力を食い尽すが、彼はそれを知らない。しらがが混じってはえても、それを悟らない。
10 Kunyada kwake Israeli kukumutsutsa, koma pa zonsezi iye sakubwerera kwa Yehova Mulungu wake kapena kumufunafuna.
イスラエルの誇は自らに向かって証言している、彼らはこのもろもろの事があっても、なおその神、主に帰らず、また主を求めない。
11 “Efereimu ali ngati nkhunda yopusa yopanda nzeru. Amayitana Igupto namapita ku Asiriya.
エフライムは知恵のない愚かな、はとのようだ。彼らはエジプトに向かって呼び求め、またアッスリヤへ行く。
12 Akamadzapita, ndidzawakola ndi ukonde wanga; ndidzawagwetsa pansi ngati mbalame zamumlengalenga. Ndikadzamva kuti asonkhana pamodzi ndidzawakola.
彼らが行くとき、わたしは彼らの上に網を張って、空の鳥のように引き落し、その悪しきおこないのゆえに、彼らを懲らしめる。
13 Tsoka kwa iwo, chifukwa andisiya Ine! Chiwonongeko kwa iwo, chifukwa andiwukira! Ndimafunitsitsa kuwapulumutsa koma amayankhula za Ine monama.
わざわいなるかな、彼らはわたしを離れて迷い出た。滅びは彼らに臨む。彼らがわたしに向かって罪を犯したからだ。わたしは彼らをあがなおうと思うが、彼らはわたしに逆らって偽りを言う。
14 Iwo salirira kwa Ine kuchokera pansi pa mtima, koma amalira mofuwula ali pa bedi pawo. Amadzichekacheka chifukwa chofuna tirigu ndi vinyo watsopano, koma amandifulatira.
彼らは真心をもってわたしを呼ばず、ただ床の上で悲しみ叫ぶ。彼らは穀物と酒のためには集まるが、わたしに逆らう。
15 Ine ndinawaphunzitsa ndikuwalimbitsa, koma amandikonzera chiwembu.
わたしは彼らを教え、その腕を強くしたが、彼らはわたしに逆らって、悪しき事をはかる。
16 Iwo satembenukira kwa Wammwambamwamba; ali ngati uta woonongeka. Atsogoleri awo adzaphedwa ndi lupanga chifukwa cha mawu awo achipongwe. Motero iwo adzasekedwa mʼdziko la Igupto.
彼らはバアルに帰る。彼らはあざむく弓のようだ。彼らの君たちはその舌の高ぶりのために、つるぎに倒れる。これはエジプトの国で人々のあざけりとなる。