< Hoseya 6 >
1 “Bwerani, tiyeni tibwerere kwa Yehova. Iye watikhadzula, koma adzatichiritsa. Iye wativulaza, koma adzamanga mabala athu.
2 Pakapita masiku awiri adzatitsitsimutsa; pa tsiku lachitatu Iye adzatiukitsa kuti tikhale ndi moyo pamaso pake.
3 Tiyeni timudziwe Yehova, tiyeni tilimbike kumudziwa Iye. Adzabwera kwa ife mosakayikira konse ngati kutuluka kwa dzuwa; adzabwera kwa ife ngati mvula ya mʼchilimwe, ngati mvula ya nthawi yamphukira imene imakhathamiritsa nthaka.”
4 Iwe Efereimu, kodi ndichite nawe chiyani? Kodi ndichite nawe chiyani, iwe Yuda? Chikondi chanu chili ngati nkhungu yammawa, ngati mame a mmamawa amene amakamuka msanga.
5 Choncho ndakuwazani ngati nkhuni kudzera mwa aneneri anga, ndakuphani ndi mawu a pakamwa panga; chigamulo changa chinangʼanima ngati mphenzi pa inu.
6 Pakuti Ine ndimafuna chifundo osati nsembe, ndi kudziwa Mulungu kulekana ndi nsembe zopsereza.
7 Monga Adamu, anthuwa aphwanya pangano langa, iwo sanakhulupirike kwa Ine.
8 Giliyadi ndi mzinda wa anthu ochita zoyipa, okhala ndi zizindikiro za kuphana.
9 Monga momwe mbala zimadikirira anthu, magulu a ansembe amachitanso motero; iwo amapha anthu pa njira yopita ku Sekemu, kupalamula milandu yochititsa manyazi.
10 Ndaona chinthu choopsa kwambiri mʼnyumba ya Israeli. Kumeneko Efereimu akuchita zachiwerewere, ndipo Israeli wadzidetsa.
11 “Kunenanso za iwe Yuda, udzakolola chilango. “Pamene ndiwabwezere anthu anga zinthu zabwino.”