< Hoseya 5 >

1 “Ansembe inu, imvani izi! Inu Aisraeli, tcherani khutu! Inu nyumba yaufumu, mvetserani! Chiweruzo ichi ndi chotsutsa inu: Inu munali ngati msampha ku Mizipa, munali ngati ukonde woyalidwa pa phiri la Tabori.
שמעו זאת הכהנים והקשיבו בית ישראל ובית המלך האזינו--כי לכם המשפט כי פח הייתם למצפה ורשת פרושה על תבור
2 Owukira azama mʼmoyo wakupha, Ine ndidzawalanga onsewo.
ושחטה שטים העמיקו ואני מוסר לכלם
3 Ndimadziwa zonse za Efereimu; Aisraeli ndi osabisika kwa Ine. Efereimu wayamba tsopano kuchita zachiwerewere; Israeli wadziyipitsa.
אני ידעתי אפרים וישראל לא נכחד ממני כי עתה הזנית אפרים נטמא ישראל
4 “Ntchito zawo siziwalola kubwerera kwa Mulungu wawo. Mʼmitima mwawo muli mzimu wachiwerewere; Iwo sadziwa Yehova.
לא יתנו מעלליהם לשוב אל אלהיהם כי רוח זנונים בקרבם ואת יהוה לא ידעו
5 Kudzikuza kwa Israeli kwakhala umboni womutsutsa; Aisraeli, ngakhale Aefereimu, anagwa mʼmachimo awo; Yudanso anagwa nawo pamodzi.
וענה גאון ישראל בפניו וישראל ואפרים יכשלו בעונם--כשל גם יהודה עמם
6 Pamene adzapita ndi nkhosa zawo ndi ngʼombe zawo kukapereka nsembe kwa Yehova, iwo sadzamupeza; Iye wawachokera.
בצאנם ובבקרם ילכו לבקש את יהוה--ולא ימצאו חלץ מהם
7 Iwo ndi osakhulupirika kwa Yehova; amabereka ana amʼchigololo ndipo chikondwerero chawo cha mwezi watsopano chidzawawononga pamodzi ndi minda yawo.
ביהוה בגדו כי בנים זרים ילדו עתה יאכלם חדש את חלקיהם
8 “Womba lipenga mu Gibeya, liza mbetete mu Rama. Fuwulani mfuwu wankhondo mu Beti-Aveni; iwe Benjamini tsogolera.
תקעו שופר בגבעה חצצרה ברמה הריעו בית און אחריך בנימין
9 Efereimu adzasanduka bwinja pa tsiku la chilango. Ine ndikulengeza zomwe zidzachitikadi pakati pa mafuko a Israeli.
אפרים לשמה תהיה ביום תוכחה בשבטי ישראל הודעתי נאמנה
10 Atsogoleri a Yuda ali ngati anthu amene amasuntha miyala ya mʼmalire. Ndidzawakhutulira ukali wanga ngati madzi a chigumula.
היו שרי יהודה כמסיגי גבול עליהם אשפוך כמים עברתי
11 Efereimu waponderezedwa, akulangidwa chifukwa chotsatira mafano.
עשוק אפרים רצוץ משפט כי הואיל הלך אחרי צו
12 Ine ndili ngati njenjete kwa Efereimu, ngati chinthu chowola kwa anthu a ku Yuda.
ואני כעש לאפרים וכרקב לבית יהודה
13 “Efereimu ataona nthenda yake, ndi Yuda ataona zilonda zake, pamenepo Efereimu anatembenukira kwa Asiriya, ndipo anawatumizira mfumu yayikulu kudzawathandiza. Koma mfumuyo singathe kukuchizani, singathe kuchiritsa mabala anu.
וירא אפרים את חליו ויהודה את מזרו וילך אפרים אל אשור וישלח אל מלך ירב והוא לא יוכל לרפא לכם ולא יגהה מכם מזור
14 Pakuti Ine ndidzakhala ngati mkango kwa Efereimu. Ngati mkango wamphamvu kwa Yuda. Ndidzawakhadzula nʼkuchokapo; ndidzawatenga ndipo palibe amene adzawalanditse.
כי אנכי כשחל לאפרים וככפיר לבית יהודה אני אני אטרף ואלך אשא ואין מציל
15 Ndipo ndidzabwerera ku malo anga mpaka anthu anga atavomereza kulakwa kwawo. Ndipo iwo adzafunafuna nkhope yanga; mʼmasautso awo adzandifunitsitsa Ine.”
אלך אשובה אל מקומי עד אשר יאשמו ובקשו פני בצר להם ישחרנני

< Hoseya 5 >