< Hoseya 4 >
1 Inu Aisraeli, imvani mawu a Yehova, chifukwa Yehova ali ndi mlandu ndi inu amene mumakhala mʼdzikoli: “Mʼdziko mwanu mulibe kukhulupirika, mulibe chikondi mulibe kulabadira za Mulungu.
Hear the word of the LORD, ye children of Israel: for the LORD hath a controversy with the inhabitants of the land, because [there is] no truth, nor mercy, nor knowledge of God in the land.
2 Muli kutemberera kokha, kunama ndi kupha. Kuba ndi kuchita chigololo; machimo achita kunyanya ndipo akungokhalira kuphana.
By swearing, and lying, and killing, and stealing, and committing adultery, they break out, and blood toucheth blood.
3 Chifukwa chake dziko likulira ndipo onse amene amakhalamo akuvutika; zirombo zakuthengo ndi mbalame zamumlengalenga ndiponso nsomba zamʼnyanja zikufa.
Therefore shall the land mourn, and every one that dwelleth therein shall languish, with the beasts of the field, and with the fowls of heaven; yea, the fishes of the sea also shall be taken away.
4 “Koma wina asapeze mnzake chifukwa, wina aliyense asayimbe mlandu mnzake, pakuti anthu ako ali ngati anthu amene amayimba mlandu wansembe.
Yet let no man strive, nor reprove another: for thy people [are] as they that strive with the priest.
5 Mumapunthwa usana ndi usiku ndipo aneneri amapunthwa nanu pamodzi. Choncho ndidzawononga amayi anu.
Therefore shalt thou fall in the day, and the prophet also shall fall with thee in the night, and I will destroy thy mother.
6 Anthu anga akuwonongeka chifukwa chosadziwa. “Pakuti mwakana kudziwa, Inenso ndidzakukanani monga ansembe anga; chifukwa mwayiwala lamulo la Mulungu wanu, Inenso ndidzayiwala ana anu.
My people are destroyed for lack of knowledge: because thou hast rejected knowledge, I will also reject thee, that thou shalt be no priest to me: seeing thou hast forgotten the law of thy God, I will also forget thy children.
7 Ansembe ankati akachuluka iwo ankandichimwiranso kwambiri; iwo anasinthanitsa ulemerero wawo ndi chinthu china chonyansa.
As they were increased, so they sinned against me: [therefore] will I change their glory into shame.
8 Amalemererapo pa machimo a anthu anga ndipo amafunitsitsa kuti anthuwo azipitiriza kuchimwa.
They eat up the sin of my people, and they set their heart on their iniquity.
9 Ndipo zidzakhala motere: zochitikira anthu ena, zidzachitikiranso ansembe. Ndidzawalanga onsewo chifukwa cha njira zawo, ndidzawabwezera chifukwa cha machitidwe awo.
And there shall be, like people, like priest: and I will punish them for their ways, and reward them their doings.
10 “Iwo azidzadya koma sadzakhuta; azidzachita zachiwerewere koma sadzachulukana, chifukwa anasiya Yehova kuti adzipereke
For they shall eat, and not have enough: they shall commit whoredom, and shall not increase: because they have left off to take heed to the LORD.
11 ku zachiwerewere, ku vinyo wakale ndi watsopano, zimene zimachotsa nzeru zomvetsa zinthu
Whoredom and wine and new wine take away the heart.
12 za anthu anga. Anthu anga amapempha nzeru ku fano lamtengo ndipo ndodo yawo yamtengo imawayankha. Mzimu wachiwerewere umawasocheretsa; iwo sakukhulupirika kwa Mulungu wawo.
My people ask counsel at their stocks, and their staff declareth unto them: for the spirit of whoredoms hath caused [them] to err, and they have gone a whoring from under their God.
13 Amapereka nsembe pamwamba pa mapiri ndi kufukiza lubani pa zitunda, pa tsinde pa mtengo wa thundu, mnjale ndi mkundi, pamene pali mthunzi wabwino. Nʼchifukwa chake ana anu aakazi akuchita zachiwerewere ndipo akazi a ana anu akuchita zigololo.
They sacrifice upon the tops of the mountains, and burn incense upon the hills, under oaks and poplars and elms, because the shadow thereof [is] good: therefore your daughters shall commit whoredom, and your spouses shall commit adultery.
14 “Ine sindidzalanga ana anu aakazi pamene iwo adzachita zachiwerewere, kapena akazi a ana anu pamene adzachita zigololo. Paja inu nomwe amunanu mumayenda ndi akazi achiwerewere, ndipo mumapereka nsembe pamodzi ndi akazi achiwerewere a ku malo opembedzerako. Anthu amene alibe nzeru adzawonongeka ndithu!
I will not punish your daughters when they commit whoredom, nor your spouses when they commit adultery: for themselves are separated with whores, and they sacrifice with harlots: therefore the people [that] doth not understand shall fall.
15 “Ngakhale umachita chigololo, iwe Israeli, Yuda asapezeke ndi mlandu wotere. “Usapite ku Giligala. Usapite ku Beti-Aveni. Ndipo usalumbire kuti, ‘Pali Yehova wamoyo!’
Though thou, Israel, play the harlot, [yet] let not Judah offend; and come not ye unto Gilgal, neither go ye up to Beth-aven, nor swear, The LORD liveth.
16 Aisraeli ndi nkhutukumve, ngosamva ngati ana angʼombe. Kodi Yehova angathe kuwaweta bwanji ngati ana ankhosa pa msipu wabwino?
For Israel slideth back as a backsliding heifer: now the LORD will feed them as a lamb in a large place.
17 Efereimu waphathana ndi mafano; mulekeni!
Ephraim [is] joined to idols: let him alone.
18 Ngakhale pamene zakumwa zawo zatha, amapitiriza kuchita zachiwerewere; atsogoleri awo amakonda kwambiri njira zawo zochititsa manyazi.
Their drink is sour: they have committed whoredom continually: her rulers [with] shame do love, Give ye.
19 Adzachotsedwa ndi kamvuluvulu ndipo adzachita manyazi chifukwa cha nsembe zawo.
The wind hath bound her up in her wings, and they shall be ashamed because of their sacrifices.