< Hoseya 2 >

1 “Nena kwa abale ako kuti, ‘Ndinu anthu anga,’ kwa alongo ako kuti ‘Ndinu okondedwa anga.’”
אמרו לאחיכם עמי ולאחותיכם רחמה׃
2 “Dzudzulani amayi anu, adzudzuleni iwo, pakuti si mkazi wanga, ndipo ine sindine mwamuna wake. Iyeyo achotse maonekedwe adama pa nkhope yake, ndi kusakhulupirika pa mawere ake.
ריבו באמכם ריבו כי היא לא אשתי ואנכי לא אישה ותסר זנוניה מפניה ונאפופיה מבין שדיה׃
3 Akapanda kutero ndidzamuvula, ndipo adzakhala wamaliseche monga tsiku limene anabadwa; ndidzamuwumitsa ngati chipululu, adzakhala ngati dziko lopanda madzi, ndi kumupha ndi ludzu.
פן אפשיטנה ערמה והצגתיה כיום הולדה ושמתיה כמדבר ושתה כארץ ציה והמתיה בצמא׃
4 Sindidzaonetsa chikondi changa pa ana ake, chifukwa ndi ana a mʼchiwerewere.
ואת בניה לא ארחם כי בני זנונים המה׃
5 Amayi awo akhala akuchita zachiwerewere ndipo anawabereka anawo akuchita zinthu zochititsa manyazi. Iwo anati, ‘Ine ndidzatsatira zibwenzi zanga, zimene zimandipatsa chakudya ndi madzi, ubweya ndi thonje, mafuta ndi chakumwa.’
כי זנתה אמם הבישה הורתם כי אמרה אלכה אחרי מאהבי נתני לחמי ומימי צמרי ופשתי שמני ושקויי׃
6 Choncho njira yake ndidzayitseka ndi minga; ndidzamuzinga ndi khoma kotero kuti sadzapezanso njira yotulukira.
לכן הנני שך את דרכך בסירים וגדרתי את גדרה ונתיבותיה לא תמצא׃
7 Adzathamangira zibwenzi zake koma sadzazipeza; adzazifunafuna koma sadzazipeza. Pamenepo iye adzati, ‘Ndibwerera kwa mwamuna wanga woyamba uja, pakuti ndinali pabwino ndi iyeyo kusiyanitsa ndi pano.’
ורדפה את מאהביה ולא תשיג אתם ובקשתם ולא תמצא ואמרה אלכה ואשובה אל אישי הראשון כי טוב לי אז מעתה׃
8 Iye sanazindikire kuti ndine amene ndinkamupatsa tirigu, vinyo watsopano ndi mafuta. Ndine amene ndinkamukhuthulira siliva ndi golide, zimene ankapangira mafano a Baala.
והיא לא ידעה כי אנכי נתתי לה הדגן והתירוש והיצהר וכסף הרביתי לה וזהב עשו לבעל׃
9 “Choncho Ine ndidzamulanda tirigu wanga pa nthawi yokolola, ndi vinyo wanga watsopano pa nthawi yopsinya mphesa. Ndidzamulanda ubweya ndi thonje langa, zomwe akanaphimba nazo umaliseche wake.
לכן אשוב ולקחתי דגני בעתו ותירושי במועדו והצלתי צמרי ופשתי לכסות את ערותה׃
10 Motero tsopano ndidzaonetsa maliseche ake pamaso pa zibwenzi zake; palibe ndi mmodzi yemwe adzamupulumutse mʼmanja mwanga.
ועתה אגלה את נבלתה לעיני מאהביה ואיש לא יצילנה מידי׃
11 Ndidzathetsa zikondwerero zake zonse: zikondwerero zake za chaka ndi chaka, za mwezi watsopano, za pa masiku a Sabata ndi maphwando ake onse a pa masiku okhazikitsidwa.
והשבתי כל משושה חגה חדשה ושבתה וכל מועדה׃
12 Ndidzawononga mitengo yake ya mpesa ndi mitengo yake yamkuyu, imene iye ankanena kuti inali malipiro ake ochokera kwa zibwenzi zake. Ndidzayisandutsa chithukuluzi, ndipo zirombo zakuthengo zidzadya zipatsozo.
והשמתי גפנה ותאנתה אשר אמרה אתנה המה לי אשר נתנו לי מאהבי ושמתים ליער ואכלתם חית השדה׃
13 Ndidzamulanga chifukwa cha masiku amene anafukiza lubani kwa Abaala; anadzikongoletsa povala mphete ndi mikanda yamtengowapatali ndipo anathamangira zibwenzi zake, koma Ine anandiyiwala,” akutero Yehova.
ופקדתי עליה את ימי הבעלים אשר תקטיר להם ותעד נזמה וחליתה ותלך אחרי מאהביה ואתי שכחה נאם יהוה׃
14 “Koma tsopano ndidzamukopa mkaziyo; ndidzapita naye ku chipululu ndipo ndidzamuyankhula mwachikondi.
לכן הנה אנכי מפתיה והלכתיה המדבר ודברתי על לבה׃
15 Kumeneko ndidzamubwezera minda yake ya mpesa, ndipo ndidzasandutsa Chigwa cha Akori kukhala khomo la chiyembekezo. Kumeneko iye adzayimba nyimbo monga mʼmasiku a ubwana wake, monga tsiku limene anatuluka ku Igupto.
ונתתי לה את כרמיה משם ואת עמק עכור לפתח תקוה וענתה שמה כימי נעוריה וכיום עלתה מארץ מצרים׃
16 “Tsiku limeneli,” Yehova akuti, “udzandiyitana kuti, ‘Amuna anga;’ sudzandiyitananso kuti, ‘Mbuye wanga.’
והיה ביום ההוא נאם יהוה תקראי אישי ולא תקראי לי עוד בעלי׃
17 Ndidzachotsa mayina a Abaala pakamwa pake; sadzatchulanso mayina awo popemphera.
והסרתי את שמות הבעלים מפיה ולא יזכרו עוד בשמם׃
18 Tsiku limenelo ndidzachita pangano ndi zirombo zakuthengo ndi mbalame zamumlengalenga ndiponso zolengedwa zokwawa pansi kuti ziyanjane ndi anthu anga. Ndidzachotsa mʼdzikomo uta, lupanga ndi zida zonse zankhondo, kuti onse apumule mwamtendere.
וכרתי להם ברית ביום ההוא עם חית השדה ועם עוף השמים ורמש האדמה וקשת וחרב ומלחמה אשבור מן הארץ והשכבתים לבטח׃
19 Ndidzakutomera kuti ukhale mkazi wanga mpaka muyaya; ndidzakutomera mwachilungamo, mwaungwiro, mwachikondi ndi mwachifundo.
וארשתיך לי לעולם וארשתיך לי בצדק ובמשפט ובחסד וברחמים׃
20 Ndidzakutomera mokhulupirika ndipo udzadziwa Yehova.
וארשתיך לי באמונה וידעת את יהוה׃
21 “Tsiku limenelo Ine ndidzayankha,” akutero Yehova. “Ndidzayankha mlengalenga pempho lake lofuna mitambo ndipo mvula idzagwa pa dziko lapansi;
והיה ביום ההוא אענה נאם יהוה אענה את השמים והם יענו את הארץ׃
22 ndipo nthaka idzamvera kupempha kwa tirigu, vinyo ndi mafuta, ndipo zidzamvera Yezireeli.
והארץ תענה את הדגן ואת התירוש ואת היצהר והם יענו את יזרעאל׃
23 Ndidzadzala Israeli mʼdziko kuti akhale wanga: ndidzaonetsa chikondi changa kwa anthu amene ndinkawatchula dzina loti, ‘Sakondedwa.’ Ndidzawawuza amene ndinkawatchula dzina loti, ‘Si anthu anga,’ kuti, ‘Ndinu anthu wanga;’ ndipo adzanena kuti, ‘ndinu Mulungu wathu,’”
וזרעתיה לי בארץ ורחמתי את לא רחמה ואמרתי ללא עמי עמי אתה והוא יאמר אלהי׃

< Hoseya 2 >