< Hoseya 14 >
1 Iwe Israeli bwerera kwa Yehova Mulungu wako. Machimo anu ndi amene akugwetsani!
2 Bweretsani zopempha zanu ndipo bwererani kwa Yehova. Munene kwa Iye kuti, “Tikhululukireni machimo athu onse ndi kutilandira mokoma mtima, kuti tithe kukuyamikani ndi mawu a pakamwa pathu.
3 Asiriya sangatipulumutse; ife sitidzakwera pa akavalo ankhondo, sitidzanenanso kuti, ‘Milungu yathu’ kwa zimene manja athu omwe anazipanga, pakuti ndinu amene mumachitira chifundo ana amasiye.”
4 Ine ndidzachiza kusakhulupirika kwawo ndipo ndidzawakonda mwaufulu pakuti ndaleka kuwakwiyira.
5 Ndidzakhala ngati mame kwa Israeli Ndipo iye adzachita maluwa ngati kakombo. Adzazika mizu yake pansi ngati mkungudza wa ku Lebanoni;
6 mphukira zake zidzakula. Kukongola kwake kudzakhala ngati mtengo wa olivi, kununkhira kwake ngati mkungudza wa ku Lebanoni.
7 Anthu adzakhalanso mu mthunzi wake. Iye adzakula bwino ngati tirigu. Adzachita maluwa ngati mphesa ndipo kutchuka kwake kudzakhala ngati vinyo wochokera ku Lebanoni.
8 Efereimu adzati, “Ndidzachita nawonso chiyani mafano? Ine ndidzamuyankha ndi kumusamalira. Ine ndili ngati mtengo wa payini wobiriwira; zipatso zako zimachokera kwa Ine.”
9 Ndani ali ndi nzeru? Adzazindikire zinthu izi. Ndani amene amamvetsa zinthu? Adzamvetse izi. Njira za Yehova ndi zolungama; anthu olungama amayenda mʼmenemo, koma anthu owukira amapunthwamo.