< Hoseya 13 >

1 Kale Efereimu ankati akayankhula, anthu ankanjenjemera; anali wolemekezeka mu Israeli. Koma analakwa popembedza Baala, motero anafa.
כדבר אפרים רתת נשא הוא בישראל ויאשם בבעל וימת
2 Tsopano akunka nachimwirachimwirabe; akudzipangira mafano pogwiritsa ntchito siliva wawo, zifanizo zopangidwa mwaluso, zonsezo zopangidwa ndi amisiri. Amanena za anthu awa kuti, “Amatenga munthu ndi kumupereka nsembe ndipo amapsompsona fano la mwana wangʼombe.”
ועתה יוספו לחטא ויעשו להם מסכה מכספם כתבונם עצבים מעשה חרשים כלה להם הם אמרים זבחי אדם עגלים ישקון
3 Choncho adzakhala ngati nkhungu yammawa, ngati mame amene amakamuka msanga, ngati mungu wowuluka kuchokera pa malo opunthira tirigu, ngati utsi umene ukutulukira pa zenera.
לכן יהיו כענן בקר וכטל משכים הלך כמץ יסער מגרן וכעשן מארבה
4 Koma Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani mu Igupto. Simuyenera kudziwa Mulungu wina, koma Ine ndekha, palibe Mpulumutsi wina kupatula Ine.
ואנכי יהוה אלהיך מארץ מצרים ואלהים זולתי לא תדע ומושיע אין בלתי
5 Ndinakusamalira mʼchipululu, mʼdziko lotentha kwambiri.
אני ידעתיך במדבר--בארץ תלאבות
6 Pamene ndinawadyetsa, iwo anakhuta; iwo atakhuta anayamba kunyada; ndipo anandiyiwala Ine.
כמרעיתם וישבעו--שבעו וירם לבם על כן שכחוני
7 Motero ndidzawalumphira ngati mkango, ndidzawabisalira mu msewu ngati kambuku.
ואהי להם כמו שחל--כנמר על דרך אשור
8 Ngati chimbalangondo cholandidwa ana ake, ndidzawambwandira ndi kuwathyolathyola. Ndidzawapwepweta ngati mkango; chirombo chakuthengo chidzawakhadzula.
אפגשם כדב שכול ואקרע סגור לבם ואכלם שם כלביא חית השדה תבקעם
9 “Iwe Israeli, wawonongedwa, chifukwa ukutsutsana ndi Ine, ukutsutsana ndi mthandizi wako.
שחתך ישראל כי בי בעזרך
10 Kodi mfumu yako ili kuti, kuti ikupulumutse? Olamulira ako a mʼmizinda yonse ali kuti, amene iwe unanena za iwo kuti, ‘Patseni mfumu ndi akalonga?’
אהי מלכך אפוא ויושיעך בכל עריך ושפטיך--אשר אמרת תנה לי מלך ושרים
11 Choncho Ine ndinakupatsani mfumu mwachipseramtima, ndipo ndinayichotsa mwaukali.
אתן לך מלך באפי ואקח בעברתי
12 Kulakwa kwa Efereimu kwasungidwa, machimo ake alembedwa mʼbuku.
צרור עון אפרים צפונה חטאתו
13 Zowawa zonga za mayi pa nthawi yobala mwana zamugwera, koma iye ndi mwana wopanda nzeru, pamene nthawi yake yobadwa yafika iyeyo safuna kutuluka mʼmimba mwa amayi ake.
חבלי יולדה יבאו לו הוא בן לא חכם כי עת לא יעמד במשבר בנים
14 “Ndidzawapulumutsa ku mphamvu ya manda; ndidzawawombola ku imfa. Kodi iwe imfa, miliri yako ili kuti? Kodi iwe manda, kuwononga kwako kuli kuti? “Sindidzachitanso chifundo, (Sheol h7585)
מיד שאול אפדם ממות אגאלם אהי דבריך מות אהי קטבך שאול--נחם יסתר מעיני (Sheol h7585)
15 ngakhale Efereimu akondwe pakati pa abale ake, mphepo ya kummawa yochokera kwa Yehova idzabwera, ikuwomba kuchokera ku chipululu. Kasupe wake adzaphwa ndipo chitsime chake chidzawuma. Chuma chake chonse chamtengowapatali chidzafunkhidwa ndipo chidzatengedwa.
כי הוא בין אחים יפריא יבוא קדים רוח יהוה ממדבר עלה ויבוש מקורו ויחרב מעינו--הוא ישסה אוצר כל כלי חמדה
16 Anthu a ku Samariya adzalangidwa chifukwa cha zolakwa zawo, chifukwa anawukira Mulungu wawo. Adzaphedwa ndi lupanga; ana awo adzaphedwa mowamenyetsa pansi, akazi awo oyembekezera adzatumbulidwa pa mimba.”
תאשם שמרון כי מרתה באלהיה בחרב יפלו--עלליהם ירטשו והריותיו יבקעו

< Hoseya 13 >