< Hoseya 12 >

1 Efereimu amadya mpweya; tsiku lonse amasaka mphepo ya kummawa ndipo amachulukitsa mabodza ndi chiwawa. Amachita mgwirizano ndi Asiriya ndipo amatumiza mphatso za mafuta a olivi ku Igupto.
Ephraim feedeth on wind, and followeth after the east wind: he daily multiplieth lies and desolation; and they do make a covenant with the Assyrians, and oil is carried into Egypt.
2 Yehova akuyimba mlandu Yuda; Iye adzalanga Yakobo molingana ndi makhalidwe ake, adzamulanga molingana ndi ntchito zake.
The LORD hath also a controversy with Judah, and will punish Jacob according to his ways; according to his doings will he recompense him.
3 Akali mʼmimba mwa amayi ake, Yakobo anagwira chidendene cha mʼbale wake; iye atakula analimbana ndi Mulungu.
He took his brother by the heel in the womb, and by his strength he had power with God:
4 Yakobo analimbana ndi mngelo ndipo anapambana; analira napempha kuti amukomere mtima. Mulungu anakumana naye ku Beteli ndipo anayankhula naye kumeneko,
Yea, he had power over the angel, and prevailed: he wept, and made supplication to him: he found him in Bethel, and there he spoke with us;
5 Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, Yehova ndiye dzina lake lotchuka!
Even the LORD God of hosts; the LORD is his memorial.
6 Koma inu muyenera kubwerera kwa Mulungu wanu; pitirizani chikondi ndi chiweruzo cholungama, ndipo muzidikira Mulungu wanu nthawi zonse.
Therefore turn thou to thy God: keep mercy and judgment, and wait on thy God continually.
7 Munthu wamalonda amagwiritsa ntchito masikelo achinyengo; iyeyo amakonda kubera anthu.
He is a merchant, the balances of deceit are in his hand: he loveth to oppress.
8 Efereimu amadzitama ponena kuti, “Ndine wolemera kwambiri; ndili ndi chuma chambiri. Palibe amene angandiloze chala chifukwa cha kulemera kwanga.”
And Ephraim said, Yet I have become rich, I have found for myself substance: in all my labours they shall find no iniquity in me that were sin.
9 “Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakutulutsa mu Igupto. Ndidzakukhazikaninso mʼmatenti, monga munkachitira masiku aja pa nthawi ya zikondwerero zanu.
And I that am the LORD thy God from the land of Egypt will yet make thee to dwell in tabernacles, as in the days of the solemn feast.
10 Ndinayankhula ndi aneneri, ndinawaonetsa masomphenya ambiri, ndipo ndinawawuza mafanizo kudzera mwa iwo.”
I have also spoken by the prophets, and I have multiplied visions, and used similitudes, by the ministry of the prophets.
11 Kodi Giliyadi ndi woyipa? Anthu ake ndi achabechabe! Kodi amapereka nsembe za ngʼombe zazimuna ku Giligala? Maguwa awo ansembe adzakhala ngati milu ya miyala mʼmunda molimidwa.
Is there iniquity in Gilead? surely they are vanity: they sacrifice bulls in Gilgal; yea, their altars are as heaps in the furrows of the fields.
12 Yakobo anathawira ku dziko la Aramu, Israeli anagwira ntchito kuti apeze mkazi, ndipo anaweta nkhosa kuti akwatire mkaziyo.
And Jacob fled into the country of Syria, and Israel served for a wife, and for a wife he kept sheep.
13 Yehova anagwiritsa ntchito mneneri kuti atulutse Israeli mu Igupto; kudzera mwa mneneriyo Iye anawasamalira.
And by a prophet the LORD brought Israel out of Egypt, and by a prophet was he preserved.
14 Koma Efereimu wamukwiyitsa kwambiri. Nʼchifukwa chake Yehova adzawalanga ndi imfa. Adzawalanga chifukwa anamuchititsa manyazi kwambiri.
Ephraim provoked him to anger most bitterly: therefore shall he leave his blood upon him, and his reproach shall his Lord return to him.

< Hoseya 12 >