< Hoseya 11 >

1 “Israeli ali mwana, ndinamukonda, ndipo ndinayitana mwana wanga kuti atuluke mu Igupto.
כי נער ישראל ואהבהו וממצרים קראתי לבני
2 Koma ndimati ndikamapitiriza kuyitana iwo amandithawa kupita kutali. Ankapereka nsembe kwa Abaala ndipo ankafukiza lubani kwa mafano.
קראו להם כן הלכו מפניהם--לבעלים יזבחו ולפסלים יקטרון
3 Ndi Ine amene ndinaphunzitsa Efereimu kuyenda, ndipo ndinawagwira pa mkono; koma iwo sanazindikire kuti ndine amene ndinawachiritsa.
ואנכי תרגלתי לאפרים קחם על זרועתיו ולא ידעו כי רפאתים
4 Ndinawatsogolera ndi zingwe zachifundo cha anthu ndi zomangira za chikondi; ndinachotsa goli mʼkhosi mwawo ndipo ndinawerama nʼkuwadyetsa.
בחבלי אדם אמשכם בעבתות אהבה ואהיה להם כמרימי על על לחיהם ואט אליו אוכיל
5 “Sadzabwerera ku Igupto, koma Asiriya ndiye adzakhala mfumu yawo pakuti akana kutembenuka.
לא ישוב אל ארץ מצרים ואשור הוא מלכו כי מאנו לשוב
6 Malupanga adzangʼanima mʼmizinda yawo, ndipo adzawononga mipiringidzo ya zipata zawo nadzathetseratu malingaliro awo.
וחלה חרב בעריו וכלתה בדיו ואכלה--ממעצותיהם
7 Anthu anga atsimikiza zondifulatira Ine. Ngakhale atayitana Wammwambamwamba, sizidzatheka kuti Iye awakwezenso.
ועמי תלואים למשובתי ואל על יקראהו--יחד לא ירומם
8 “Kodi ndingakusiye bwanji iwe Efereimu? Kodi ndingakupereke bwanji iwe Israeli? Kodi ndingakuchitire bwanji zimene ndinachitira Adima? Kodi ndingathe bwanji kukuchitira zimene ndinachitira Zeboimu? Mtima wanga wakana kutero; chifundo changa chonse chikusefukira.
איך אתנך אפרים אמגנך ישראל--איך אתנך כאדמה אשימך כצבאים נהפך עלי לבי יחד נכמרו נחומי
9 Sindidzalola kuti ndikulange ndi mkwiyo wanga woopsa, kapena kutembenuka ndi kuwononga Efereimu. Pakuti Ine ndine Mulungu osati munthu, Woyerayo pakati panu. Sindidzabwera mwaukali.
לא אעשה חרון אפי לא אשוב לשחת אפרים כי אל אנכי ולא איש--בקרבך קדוש ולא אבוא בעיר
10 Iwo adzatsatira Yehova; Iye adzabangula ngati mkango. Akadzabangula, ana ake adzabwera akunjenjemera kuchokera kumadzulo.
אחרי יהוה ילכו כאריה ישאג כי הוא ישאג ויחרדו בנים מים
11 Adzabwera akunjenjemera ngati mbalame kuchokera ku Igupto, ngati nkhunda kuchokera ku Asiriya. Ine ndidzawakhazikanso mʼnyumba zawo,” akutero Yehova.
יחרדו כצפור ממצרים וכיונה מארץ אשור והושבתים על בתיהם נאם יהוה
12 Efereimu wandizungulira ndi mabodza, nyumba ya Israeli yandizungulira ndi chinyengo. Ndipo Yuda wawukira Mulungu, wawukira ngakhale Woyerayo amene ndi wokhulupirika.
סבבני בכחש אפרים ובמרמה בית ישראל ויהודה עד רד עם אל ועם קדושים נאמן

< Hoseya 11 >