< Hoseya 10 >

1 Israeli anali mpesa wotambalala; anabereka zipatso zambiri. Pamene zipatso zawo zinanka zichuluka, anawonjezera kumanga maguwa ansembe. Pamene dziko lake linkatukuka, anakongoletsa miyala yake yopatulika.
גפן בוקק ישראל פרי ישוה לו כרב לפריו הרבה למזבחות--כטוב לארצו היטיבו מצבות
2 Mtima wawo ndi wonyenga ndipo tsopano ayenera kulangidwa chifukwa cha kulakwa kwawo. Yehova adzagumula maguwa awo ansembe ndi kuwononga miyala yawo yopatulika.
חלק לבם עתה יאשמו הוא יערף מזבחותם ישדד מצבותם
3 Pamenepo anthuwo adzanena kuti, “Ife tilibe mfumu chifukwa sitinaope Yehova. Koma ngakhale tikanakhala ndi mfumu, kodi mfumuyo ikanatichitira chiyani?”
כי עתה יאמרו אין מלך לנו כי לא יראנו את יהוה והמלך מה יעשה לנו
4 Mafumu amalonjeza zambiri, amalumbira zabodza pochita mapangano. Kotero maweruzo amaphuka ngati zitsamba zakupha mʼmunda umene walimidwa.
דברו דברים אלות שוא כרת ברית ופרח כראש משפט על תלמי שדי
5 Anthu amene amakhala mu Samariya akuchita mantha chifukwa cha fano la mwana wangʼombe ku Beti-Aveni. Anthu ake adzalirira fanolo, chimodzimodzinso ansembe ake adamawo, amene anakondwera ndi kukongola kwake, chifukwa lachotsedwa pakati pawo ndi kupita ku ukapolo.
לעגלות בית און יגורו שכן שמרון כי אבל עליו עמו וכמריו עליו יגילו--על כבודו כי גלה ממנו
6 Fanolo lidzatengedwa kupita ku Asiriya ngati mphatso kwa mfumu yayikulu. Efereimu adzachititsidwa manyazi chifukwa cha mafano ake amitengo.
גם אותו לאשור יובל מנחה למלך ירב בשנה אפרים יקח ויבוש ישראל מעצתו
7 Samariya ndi mfumu yake adzatengedwa kupita kutali ngati kanthambi koyenda pa madzi.
נדמה שמרון מלכה כקצף על פני מים
8 Malo opembedzerako mafano a ku Aveni adzawonongedwa. Ili ndiye tchimo la Israeli. Minga ndi mitungwi zidzamera ndi kuphimba maguwa awo ansembe. Kenaka anthu adzawuza mapiri kuti, “Tiphimbeni!” ndipo adzawuza zitunda kuti, “Tigwereni!”
ונשמדו במות און חטאת ישראל--קוץ ודרדר יעלה על מזבחותם ואמרו להרים כסונו ולגבעות נפלו עלינו
9 “Iwe Israeli, wachimwa kuyambira mʼmasiku a Gibeya, ndipo wakhala uli pomwepo. Kodi nkhondo sinagonjetse anthu ochita zoyipa ku Gibeya?
מימי הגבעה חטאת ישראל שם עמדו לא תשיגם בגבעה מלחמה על בני עלוה
10 Pamene ndifunire, ndidzalanga anthuwo; mitundu ya anthu idzasonkhanitsidwa kudzalimbana nawo, kuwayika mʼndende chifukwa cha uchimo wawo waukulu.
באותי ואסרם ואספו עליהם עמים באסרם לשתי עינתם (עונותם)
11 Efereimu ndi mwana wangʼombe wamkazi wophunzitsidwa amene amakonda kupuntha tirigu, choncho Ine ndidzayika goli mʼkhosi lake lokongolalo. Ndidzasenzetsa Efereimu goli, Yuda ayenera kulima, ndipo Yakobo ayenera kutipula.
ואפרים עגלה מלמדה אהבתי לדוש ואני עברתי על טוב צוארה ארכיב אפרים יחרוש יהודה ישדד לו יעקב
12 Mufese nokha chilungamo ndipo mudzakolola chipatso cha chikondi changa chosasinthika. Ndipo tipulani munda wanu wosalimidwawo; pakuti ino ndi nthawi yofunafuna Yehova, mpaka Iye atabwera kudzakugwetserani mivumbi ya chilungamo.
זרעו לכם לצדקה קצרו לפי חסד נירו לכם ניר ועת לדרוש את יהוה עד יבוא וירה צדק לכם
13 Koma inu munadzala zolakwa, mwakolola zoyipa; mwadya chipatso cha chinyengo. Chifukwa mumadalira mphamvu zanu ndiponso ankhondo anu ochulukawo,
חרשתם רשע עולתה קצרתם אכלתם פרי כחש--כי בטחת בדרכך ברב גבוריך
14 phokoso lankhondo lidzamveka pakati pa anthu anga kotero kuti malinga anu onse adzawonongeka, monga momwe Salimani anawonongera Beti-Aribeli pa nthawi ya nkhondo; pamene anapha amayi pamodzi ndi ana awo omwe.
וקאם שאון בעמך וכל מבצריך יושד כשד שלמן בית ארבאל ביום מלחמה אם על בנים רטשה
15 Momwemonso zidzakuchitikira, iwe Beteli chifukwa kuyipa kwako ndi kwakukulu. Tsiku limeneli likadzafika, mfumu ya Israeli idzawonongedwa kwathunthu.
ככה עשה לכם בית אל מפני רעת רעתכם בשחר נדמה נדמה מלך ישראל

< Hoseya 10 >