< Ahebri 9 >

1 Pangano loyamba lija linali ndi malamulo okhudza chipembedzo, ndi malo opembedzeramo omangidwa ndi anthu.
Мав же і перший заповіт постанови богослужби та земну святиню.
2 Anthu ankamanga chihema. Mʼchipinda choyamba munali choyikapo nyale, tebulo ndi buledi woperekedwa kwa Mulungu. Chipinda chimenechi chinkatchedwa Malo Opatulika.
Була́ бо уряджена перша скинія, яка зветься „Святе“, а в ній був світильни́к, і стіл, і жертовні хліби.
3 Kuseri kwa chinsalu chotchinga chachiwiri kunkatchedwa Malo Opatulika kwambiri.
А за другою засло́ною скинія, що зветься „Святе́ Святих“.
4 Mʼmenemo munali guwa lansembe lagolide lofukizirapo lubani. Munalinso Bokosi la Chipangano lokutidwa ndi golide. Mʼbokosimo munali mʼphika wagolide mʼmene ankasungiramo mana ndi ndodo ya Aaroni imene inaphuka ija, ndiponso miyala ya pangano.
Мала вона золоту кадильницю й ковче́га заповіту, усюди обку́того золотом, а в нім золота посу́дина з ма́нною, і розцві́ле жезло́ Ааро́нове та табли́ці заповіту.
5 Pamwamba pa bokosilo panali zifanizo za angelo otchedwa akerubi aulemerero, ataphimba chivundikiro cha bokosilo chimene chinali malo okhululukirapo machimo. Koma nʼzosatheka tsopano kufotokoza zinthu mwatsatanetsatane.
А над ним херуви́ми слави, що затінювали престола благодаті, про що говорити докладно тепер не потрібно.
6 Zinthu zonsezi zitakonzedwa, ansembe ankalowamo mʼchipinda choyamba chija nthawi ndi nthawi kumatumikiramo.
При такому ж уря́дженні до першої скинії вхо́дили за́вжди священики, пра́влячи служби Богові,
7 Koma Mkulu wa ansembe yekha ndiye ankalowa chipinda chachiwiri chija kamodzi kokha pa chaka. Iye sankalowamo wopanda magazi. Magaziwo ankapereka nsembe kwa Mulungu chifukwa cha iye mwini ndiponso chifukwa cha machimo a anthu amene ankachita mosazindikira.
а до другої раз на рік сам первосвященик, не без крови, яку він прино́сить за себе й за лю́дські провини.
8 Mwa njira imeneyi Mzimu Woyera ankaonetsa kuti njira yolowera ku malo opatulika inali isanaonetsedwe pamene Chihema choyamba chinali chilipo.
Святий Дух виявляє оцим, що ще не відкрита дорога в святиню, коли ще стоїть перша скинія.
9 Zimenezi nʼzofanizira chabe, ndipo zinkalozera nthawi ino, kusonyeza kuti mphatso ndi nsembe zimene zinkaperekedwa sizinkachotsa chikumbumtima cha wopembedzayo.
Вона образ для ча́су теперішнього, за якого прино́сяться да́ри та жертви, що того не можуть вдоскона́лити, щодо сумління того, хто служить,
10 Inali nkhani ya zakudya, ya zakumwa ndi ya miyambo yosiyanasiyana ya masambidwe. Anali malamulo akunja kokha mpaka pa nthawi imene anakonzanso zonse mwatsopano.
що тільки в потравах та в напо́ях, та в різних обмива́ннях, в уставах тілесних, — установлено їх аж до ча́су направи.
11 Koma Khristu atafika monga Mkulu wa ansembe wa zinthu zokoma zimene zilipo tsopano, Iye analowa mʼChihema chachikulu ndiponso changwiro chimene sichinamangidwe ndi munthu, ndiye kuti sichili pansi pano.
Але́ Христос, Первосвященик майбутнього доброго, прийшов із більшою й досконалішою скинією, нерукотво́рною, цебто не цього втво́рення,
12 Iye sanalowemo ndi magazi ambuzi yayimuna, ana angʼombe amphongo, koma analowa Malo Opatulika kamodzi kokha ndi magazi ake, atatikonzera chipulumutso chosatha. (aiōnios g166)
і не з кров'ю козлів та телят, але з власною кров'ю увійшов до святині один раз, та й набу́в вічне відку́плення. (aiōnios g166)
13 Ngati magazi ambuzi yayimuna, angʼombe yayimuna ndi phulusa la mwana wangʼombe wamkazi zimati zikawazidwa pa odetsedwa zimawayeretsa kotero kuti amakhala oyeretsedwa ku thupi,
Бо коли кров козлів та телят та попіл із я́лівок, як покро́пить нечистих, освячує їх на очи́щення тіла,
14 nʼkoposa kotani magazi a Khristu, amene mwa Mzimu wamuyaya anadzipereka yekha kwa Mulungu kukhala nsembe yopanda chilema. Iye adzayeretsa chikumbumtima chathu pochotsa ntchito za imfa, kuti ife titumikire Mulungu wamoyo. (aiōnios g166)
скільки ж більш кров Христа, що Себе непорочного Богу приніс Вічним Духом, очистить наше сумління від мертвих учинків, щоб служити нам Богові Живому! (aiōnios g166)
15 Pa chifukwa chimenechi Khristu ndi mʼkhalapakati wa pangano latsopano, kuti iwo amene anayitanidwa alandire chuma chamuyaya, pakuti Iye tsopano anafa ngati dipo lomasula iwo ku machimo amene anachita ali pansi pa pangano loyamba lija. (aiōnios g166)
Тому Він — Посере́дник Ново́го Заповіту, щоб через смерть, — що була́ для відку́плення від пере́ступів, учинених за першого заповіту, — покликані прийняли́ обі́тницю вічного спа́дку. (aiōnios g166)
16 Ngati munthu alemba pangano losiyira ena chuma, pafunika kutsimikiza kuti wolemba panganolo wamwaliradi,
Бо де заповіт, там має відбутися смерть заповітника,
17 chifukwa pangano lotere limakhala ndi mphamvu ngati wolembayo wamwalira. Siligwira ntchito pamene wolembayo ali ndi moyo.
заповіт бо важливий по мертвих, бо нічого не варт він, як живе заповітник.
18 Nʼchifukwa chake pangano loyamba lija silinachitike popanda kukhetsa magazi.
Тому й перший заповіт освячений був не без крови:
19 Mose atawawuza anthu onse malamulo, anatenga magazi a ana angʼombe amphongo ndi ambuzi yayimuna pamodzi ndi madzi, ubweya wofiira ndiponso chitsamba chotchedwa hisope, ndi kuwaza pa buku ndi anthu onse.
Коли бо Мойсей сповістив усі заповіді за Зако́ном усьому наро́дові, він узяв кров козлів та телят із водою й червоною вовною та з ісопом, та й покропив і саму оту книгу, і людей,
20 Iye anati, “Awa ndi magazi a pangano limene Mulungu wakulamulirani kuti mulisunge.”
проказуючи: „Це кров заповіту, що його наказав для вас Бог!“
21 Momwemonso Mose anawaza magazi pa Chihema chija ndiponso pa zipangizo zonse zogwiritsa ntchito pa chipembedzo.
Так само і скинію, і ввесь по́суд служебний покропи́в він кров'ю.
22 Monga mwa malamulo titha kunena kuti, pafupifupi zinthu zonse zimayeretsedwa ndi magazi ndipo popanda kukhetsa magazi palibe kukhululukidwa machimo.
І майже все за Зако́ном кров'ю очищується, а без пролиття́ крови немає відпу́щення.
23 Tsono panafunika kuti zinthu zingofanizira zenizeni za kumwamba, ziyeretsedwe ndi nsembe zimenezi, koma zinthu za kumwamba zenizenizo kuti ziyeretsedwe panafunika nsembe zina zoposa zimenezo.
Отож, треба було́, щоб образи небесного очищалися цими, а небесне саме кращими від оцих же́ртвами.
24 Pakuti Khristu sanalowe mʼmalo opatulika omangidwa ndi anthu amene anali chifaniziro cha malo enieniwo. Iye analowa kumwamba kwenikweniko kuti azionekera pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.
Бо Христос увійшов не в рукотво́рну святиню, що була на взір правдивої, але в саме небо, щоб з'явитись тепер перед Божим лицем за нас,
25 Iye sanalowe kumwamba kuti azikadziperekanso nsembe kachiwiri monga momwe mkulu wa ansembe ankachitira chaka ndi chaka ku Malo Opatulika kwambiri ndi magazi amene sanali ake.
і не тому́, щоб часто прино́сити в жертву Себе, як первосвященик входить у святиню кожнорічно з кров'ю чужою,
26 Zikanatero bwenzi Khristu atamva zowawa kambirimbiri chilengedwere cha dziko lapansi. Koma tsopano anaoneka kamodzi kokha chifukwa cha onse pa nthawi yotsiriza kuti achotse tchimo podzipereka yekha nsembe. (aiōn g165)
бо інакше Він мусів би часто страждати ще від закла́дин світу, а тепер Він з'явився один раз на схи́лку віків, щоб власною жертвою знищити гріх. (aiōn g165)
27 Popeza kunayikika kwa munthu kufa kamodzi ndipo kenaka kuweruzidwa,
І як лю́дям призна́чено вмерти один раз, потім же суд,
28 momwemonso Khristu anadzipereka nsembe kamodzi kokha kuchotsa machimo a anthu ambiri. Ndipo Iye adzaonekanso kachiwiri, osati kudzachotsa tchimo, koma kudzapereka chipulumutso kwa amene akumudikira.
так і Христос один раз був у жертву прине́сений, щоб „поне́сти гріхи багатьох“, і не в справі гріха другий раз з'явитися тим, хто чекає Його на спасі́ння.

< Ahebri 9 >