< Ahebri 9 >
1 Pangano loyamba lija linali ndi malamulo okhudza chipembedzo, ndi malo opembedzeramo omangidwa ndi anthu.
Torej prva zaveza je resnično imela tudi odredbe o bogoslužju in posvetnem svetišču.
2 Anthu ankamanga chihema. Mʼchipinda choyamba munali choyikapo nyale, tebulo ndi buledi woperekedwa kwa Mulungu. Chipinda chimenechi chinkatchedwa Malo Opatulika.
Kajti postavljeno je bilo šotorsko svetišče; prvo, v katerem je bil svečnik in miza ter hlebi navzočnosti; kar je imenovano Svetišče.
3 Kuseri kwa chinsalu chotchinga chachiwiri kunkatchedwa Malo Opatulika kwambiri.
Za drugim zagrinjalom pa šotorsko svetišče, ki se imenuje Najsvetejše;
4 Mʼmenemo munali guwa lansembe lagolide lofukizirapo lubani. Munalinso Bokosi la Chipangano lokutidwa ndi golide. Mʼbokosimo munali mʼphika wagolide mʼmene ankasungiramo mana ndi ndodo ya Aaroni imene inaphuka ija, ndiponso miyala ya pangano.
ki je imelo zlato kadilnico in skrinjo zaveze v celoti prevlečeno z zlatom, v kateri je bila zlata posoda, ki je imela mano in Aronova palica, ki je vzbrstela ter plošči zaveze;
5 Pamwamba pa bokosilo panali zifanizo za angelo otchedwa akerubi aulemerero, ataphimba chivundikiro cha bokosilo chimene chinali malo okhululukirapo machimo. Koma nʼzosatheka tsopano kufotokoza zinthu mwatsatanetsatane.
in nad njo keruba slave, ki zasenčujeta sedež milosti [skrinje zaveze]; o katerem sedaj ne moremo podrobno govoriti.
6 Zinthu zonsezi zitakonzedwa, ansembe ankalowamo mʼchipinda choyamba chija nthawi ndi nthawi kumatumikiramo.
Torej ko so bile te stvari tako odrejene, so duhovniki, opravljajoč službo Bogu, vedno šli v prvo šotorsko svetišče.
7 Koma Mkulu wa ansembe yekha ndiye ankalowa chipinda chachiwiri chija kamodzi kokha pa chaka. Iye sankalowamo wopanda magazi. Magaziwo ankapereka nsembe kwa Mulungu chifukwa cha iye mwini ndiponso chifukwa cha machimo a anthu amene ankachita mosazindikira.
Toda v drugo je véliki duhovnik odšel sam, enkrat vsako leto, ne brez krvi, ki jo je daroval zase in za grehe ljudi.
8 Mwa njira imeneyi Mzimu Woyera ankaonetsa kuti njira yolowera ku malo opatulika inali isanaonetsedwe pamene Chihema choyamba chinali chilipo.
Sveti Duh tako naznanja, da pot v najsvetejše še ni bila razodeta, dokler je še stalo prvo šotorsko svetišče.
9 Zimenezi nʼzofanizira chabe, ndipo zinkalozera nthawi ino, kusonyeza kuti mphatso ndi nsembe zimene zinkaperekedwa sizinkachotsa chikumbumtima cha wopembedzayo.
Ta je bil podoba za tedaj pripravljeni čas, v katerem so bili darovani tako darovi kakor žrtve, ki niso mogli storiti popolnega, kar se tiče vesti, tistega, ki je službo opravljal.
10 Inali nkhani ya zakudya, ya zakumwa ndi ya miyambo yosiyanasiyana ya masambidwe. Anali malamulo akunja kokha mpaka pa nthawi imene anakonzanso zonse mwatsopano.
To je veljalo samo za jedi in pijače in številna umivanja ter mesene odredbe, naložene nanje do časa preureditve.
11 Koma Khristu atafika monga Mkulu wa ansembe wa zinthu zokoma zimene zilipo tsopano, Iye analowa mʼChihema chachikulu ndiponso changwiro chimene sichinamangidwe ndi munthu, ndiye kuti sichili pansi pano.
Toda Kristus, ki je prišel [kot] véliki duhovnik prihodnjih dobrih stvari, z večjim in popolnejšim šotorskim svetiščem, ne narejenim z rokami, to se pravi, ne od te zgradbe;
12 Iye sanalowemo ndi magazi ambuzi yayimuna, ana angʼombe amphongo, koma analowa Malo Opatulika kamodzi kokha ndi magazi ake, atatikonzera chipulumutso chosatha. (aiōnios )
niti ne s krvjo koz in telet, temveč je s svojo lastno krvjo enkrat vstopil v sveti prostor in za nas dosegel večno odkupitev. (aiōnios )
13 Ngati magazi ambuzi yayimuna, angʼombe yayimuna ndi phulusa la mwana wangʼombe wamkazi zimati zikawazidwa pa odetsedwa zimawayeretsa kotero kuti amakhala oyeretsedwa ku thupi,
Kajti če kri bikov in kozlov ter pepel telice, škropeč nečiste, posvečuje do očiščenja mesa;
14 nʼkoposa kotani magazi a Khristu, amene mwa Mzimu wamuyaya anadzipereka yekha kwa Mulungu kukhala nsembe yopanda chilema. Iye adzayeretsa chikumbumtima chathu pochotsa ntchito za imfa, kuti ife titumikire Mulungu wamoyo. (aiōnios )
koliko bolj bo Kristusova kri, ki je po večnem Duhu samega sebe brez madeža daroval Bogu, očistila vašo vest pred mrtvimi deli, da služite živemu Bogu? (aiōnios )
15 Pa chifukwa chimenechi Khristu ndi mʼkhalapakati wa pangano latsopano, kuti iwo amene anayitanidwa alandire chuma chamuyaya, pakuti Iye tsopano anafa ngati dipo lomasula iwo ku machimo amene anachita ali pansi pa pangano loyamba lija. (aiōnios )
In zaradi tega razloga je on posrednik nove zaveze, da bi s pomočjo smrti, za odkupitev od prestopkov, ki so bili pod prvo zavezo, tisti, ki so poklicani, lahko prejeli obljubo večne dediščine. (aiōnios )
16 Ngati munthu alemba pangano losiyira ena chuma, pafunika kutsimikiza kuti wolemba panganolo wamwaliradi,
Kajti kjer je oporoka, tam mora biti tudi potreba po smrti oporočnika.
17 chifukwa pangano lotere limakhala ndi mphamvu ngati wolembayo wamwalira. Siligwira ntchito pamene wolembayo ali ndi moyo.
Kajti oporoka je veljavna potem, ko so ljudje mrtvi; sicer nima nobene moči, vse dokler oporočnik živi.
18 Nʼchifukwa chake pangano loyamba lija silinachitike popanda kukhetsa magazi.
Nakar niti prva zaveza ni bila posvečena brez krvi.
19 Mose atawawuza anthu onse malamulo, anatenga magazi a ana angʼombe amphongo ndi ambuzi yayimuna pamodzi ndi madzi, ubweya wofiira ndiponso chitsamba chotchedwa hisope, ndi kuwaza pa buku ndi anthu onse.
Kajti ko je Mojzes vsem ljudem govoril vsak predpis, glede na postavo, je vzel kri telet in kozlov, z vodo in škrlatno volno ter izop in poškropil tako knjigo kakor vse ljudi,
20 Iye anati, “Awa ndi magazi a pangano limene Mulungu wakulamulirani kuti mulisunge.”
rekoč: »To je kri zaveze, ki vam jo je Bog ukazal.«
21 Momwemonso Mose anawaza magazi pa Chihema chija ndiponso pa zipangizo zonse zogwiritsa ntchito pa chipembedzo.
Poleg tega je s krvjo poškropil tako šotorsko svetišče kakor vse posode za služenje.
22 Monga mwa malamulo titha kunena kuti, pafupifupi zinthu zonse zimayeretsedwa ndi magazi ndipo popanda kukhetsa magazi palibe kukhululukidwa machimo.
In skoraj vse stvari se po postavi očiščuje s krvjo; in brez prelivanja krvi ni odpuščanja.
23 Tsono panafunika kuti zinthu zingofanizira zenizeni za kumwamba, ziyeretsedwe ndi nsembe zimenezi, koma zinthu za kumwamba zenizenizo kuti ziyeretsedwe panafunika nsembe zina zoposa zimenezo.
Bilo je torej potrebno, da naj bi bili vzori stvari v nebesih očiščeni s temi; toda same nebeške stvari [pa] z boljšimi žrtvami kakor te.
24 Pakuti Khristu sanalowe mʼmalo opatulika omangidwa ndi anthu amene anali chifaniziro cha malo enieniwo. Iye analowa kumwamba kwenikweniko kuti azionekera pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.
Kajti Kristus ni vstopil v svete prostore, narejene z rokami, ki so slike resničnih; temveč v sama nebesa, da se sedaj za nas pokaže v Božji prisotnosti.
25 Iye sanalowe kumwamba kuti azikadziperekanso nsembe kachiwiri monga momwe mkulu wa ansembe ankachitira chaka ndi chaka ku Malo Opatulika kwambiri ndi magazi amene sanali ake.
Niti ne, da bi samega sebe pogosto daroval, kakor véliki duhovnik vsako leto s krvjo drugih vstopa v sveti prostor;
26 Zikanatero bwenzi Khristu atamva zowawa kambirimbiri chilengedwere cha dziko lapansi. Koma tsopano anaoneka kamodzi kokha chifukwa cha onse pa nthawi yotsiriza kuti achotse tchimo podzipereka yekha nsembe. (aiōn )
kajti potem bi moral od ustanovitve sveta pogosto trpeti. Toda sedaj se je prikazal enkrat ob koncu sveta, da z žrtvovanjem samega sebe odstrani greh. (aiōn )
27 Popeza kunayikika kwa munthu kufa kamodzi ndipo kenaka kuweruzidwa,
In kakor je določeno ljudem enkrat umreti, toda po tem sodba;
28 momwemonso Khristu anadzipereka nsembe kamodzi kokha kuchotsa machimo a anthu ambiri. Ndipo Iye adzaonekanso kachiwiri, osati kudzachotsa tchimo, koma kudzapereka chipulumutso kwa amene akumudikira.
tako je bil Kristus enkrat darovan, da nosi grehe mnogih; in tem, ki ga pričakujejo, se bo drugič prikazal brez greha v rešitev duš.