< Ahebri 7 >

1 Melikizedeki ameneyu anali mfumu ya ku Salemu, ndiponso wansembe wa Mulungu Wammwambamwamba. Anakumana ndi Abrahamu pamene ankabwerera kuchokera ku nkhondo atagonjetsa mafumu aja, Melikizedeki anakumana naye namudalitsa.
Když se totiž Abraham vracel z vítězného válečného tažení, při kterém vysvobodil svého synovce Lota, vyšel mu vstříc král pokoje a spravedlnosti, kněz Nejvyššího – Malkísedek ze Sálemu.
2 Ndipo Abrahamu anamupatsa chakhumi cha zonse anafunkha. Choyamba dzina la Melikizedeki likutanthauza, “Mfumu ya chilungamo,” kenakanso, “Mfumu ya Salemu,” kutanthauza, “Mfumu ya mtendere.”
3 Alibe abambo kapena mayi, alibe chiyambi kapena chitsiriziro cha moyo wake. Iye ali ngati Mwana wa Mulungu ndipo akupitirira kukhala wansembe wamuyaya.
Neznáme jeho rodiče ani rodokmen, nevíme, kdy se narodil, ani kdy zemřel. Abraham mu odevzdal desátky z kořisti a přijal od něho požehnání jako potvrzení slibů, kterých se mu od Boha dostalo. V Abrahamovi se před Malkísedekem sklonil a desátky mu odevzdal i praotec kněžského rodu Lévi, jehož potomci později podle ustanovení zákona konali kněžskou službu a vybírali desátek.
4 Mukuona tsono kuti munthuyo anali wamkulu ndithu, pakuti Abrahamu kholo lathu anamupatsa chakhumi cha zimene anafunkha.
5 Tsono lamulo likuti, ana a Levi amene amakhala ansembe azilandira chakhumi kuchokera kwa Aisraeli, abale awo ngakhale kuti abale awowo ndi ochokera kwa Abrahamu.
6 Melikizedeki sanali wochokera kwa Levi, komabe analandira chakhumi kuchokera kwa Abrahamu nadalitsa Abrahamuyo amene analandira malonjezo a Mulungu.
7 Mosakayika konse, munthu amene amadalitsa ndi wamkulu kuposa amene akudalitsidwayo.
8 Ansembe amene amalandira chakhumi amafa, choncho Melikizedeki ndi wamkulu kuwaposa iwo chifukwa Malemba amamuchitira umboni kuti ndi wamoyo.
9 Wina angathe kunena kuti Levi, amene amalandira chakhumi, anapereka chakhumicho kudzera mwa Abrahamu,
10 chifukwa pamene Melikizedeki anakumana ndi Abrahamu nʼkuti Levi ali mʼthupi la kholo lake.
11 Kukanatheka kukhala wangwiro mwa unsembe wa Levi, pakuti Malamulo anapatsidwa kwa anthu mwa unsembe wa Levi, nʼchifukwa chiyani panafunikanso wansembe wina kuti abwere, wofanana ndi Melikizedeki, osati Aaroni?
Lévijská služba nebyla s to přivést Boží lid k dokonalosti. Proto bylo třeba jiné služby a jiného kněze – a to podle řádu Malkísedekova. Je zřejmé, že přenesením kněžství zaniká zákonité oprávnění pro trvání lévijské služby.
12 Pakuti pamene unsembe usintha, malamulonso amayenera kusintha.
13 Ambuye athu Yesu, amene mawuwa akunena za Iye, anali wa fuko lina, ndipo palibe aliyense wochokera fuko lakelo amene anatumikira pa guwa lansembe.
14 Pakuti nʼzodziwika bwino kuti Ambuye athu anachokera fuko la Yuda. Kunena za fuko limeneli, Mose sananenepo kanthu za ansembe.
Náš Pán, jak všichni víme, pochází z Judova pokolení, jehož členy Mojžíš nikdy nepověřil kněžskou službou a žádný člen jeho rodu ji také nikdy nekonal.
15 Ndipo zimene tanenazi zimamveka bwino ngati tiona kuti pafika wansembe wina wofanana ndi Melikizedeki.
Je proto zřejmé, že v něm povstává nový kněz podle řádu Malkísedekova,
16 Yesu sanakhale wansembe chifukwa cha malamulo monga mwa mabadwidwe ake koma mwamphamvu ya moyo wosatha.
který svou hodnost nedědí na základě lévijského zákona, ale ujímá se jí mocí své nesmrtelnosti.
17 Pakuti Mulungu anamuchitira umboni kuti, “Iwe ndi wansembe wamuyaya, monga mwa dongosolo la unsembe wa Melikizedeki.” (aiōn g165)
To dosvědčuje žalmista, když říká: „Ty jsi kněz na věky podle řádu Malkísedekova.“ (aiōn g165)
18 Choncho lamulo loyamba lachotsedwa chifukwa linali lofowoka ndi lopanda phindu.
Předchozí zákonné ustanovení o kněžské službě bylo zrušeno, protože se ukázalo jako slabé a neužitečné.
19 Tsono Malamulo sangathe kusandutsa chilichonse kukhala changwiro, koma mʼmalo mwake mwalowa chiyembekezo chabwino, chimenechi timayandikira nacho kwa Mulungu.
Vždyť samo o sobě nikoho nepřivedlo k dokonalosti. Vystřídala je lepší naděje, jejímž prostřednictvím se přibližujeme k Bohu.
20 Izi sizinachitiketu wopanda lumbiro. Ena ankakhala ansembe popanda lumbiro.
Toto přenesení kněžství se nestalo bez přísahy. Kněží bývali jmenováni bez přísahy, ale Ježíš byl ustanoven s přísahou, poněvadž mu bylo řečeno:
21 Koma Yesu ankakhala wansembe ndi lumbiro pamene Mulungu anati, “Ambuye analumbira ndipo sangasinthe maganizo ake, ‘Iwe ndi wansembe wamuyaya.’” (aiōn g165)
„Pán přísahal a nebude toho litovat: Ty jsi kněz na věky podle řádu Malkísedekova.“ (aiōn g165)
22 Chifukwa cha lumbiroli, Yesu wakhala Nkhoswe ya Pangano lopambana.
Proto se Ježíš stal ručitelem lepší smlouvy.
23 Tsono ansembe akale aja analipo ambiri, popeza imfa imawalepheretsa kupitiriza ntchitoyi.
Kněží bylo mnoho. Protože byli smrtelní, nastupoval jeden za druhým. Žádný nemohl konat úřad do nekonečna.
24 Koma Yesu popeza ndi wamuyaya, unsembe wake ndi wosatha. (aiōn g165)
Ježíš však nepotřebuje předávat úřad dalšímu, protože zůstává na věky. (aiōn g165)
25 Chifukwa chake Iye amapulumutsa kwathunthu amene amabwera kwa Mulungu kudzera mwa Iyeyo. Iye ali ndi moyo nthawi zonse kuti adziwapempherera iwo.
Proto přináší dokonalé spasení těm, kteří jeho prostřednictvím přicházejí k Bohu. Je stále připraven zasáhnout v jejich prospěch.
26 Uyu ndi Mkulu wa ansembe amene tikumufuna chifukwa ndi woyera, wopanda choyipa kapena chodetsa chilichonse, wosiyana ndi anthu ochimwa, ndiponso wokwezedwa kuposa zonse zakumwambaku.
Takového velekněze jsme potřebovali: svatého, nevinného, neposkvrněného, odděleného od hříšníků a vyššího než sama nebesa,
27 Kusiyana ndi akulu a ansembe ena aja, Yesu sanafunike kupereka nsembe tsiku ndi tsiku poyamba chifukwa cha machimo ake, ndipo kenaka chifukwa cha machimo a anthu ena. Iye anadzipereka nsembe chifukwa cha machimo awo kamodzi kokha pamene anadzipereka yekha.
který není povinen přinášet každý den oběť napřed za své hříchy a pak za hříchy lidu. Obětoval sama sebe.
28 Pakuti lamulo limasankha anthu amene ndi ofowoka kukhala akulu a ansembe; koma lumbiro, lomwe linabwera pambuyo pa lamulo, linasankha Mwana, amene anapangidwa kukhala wangwiro kwamuyaya. (aiōn g165)
Zákon dosazoval za velekněze lidi podrobené slabosti, ale slovo přísahy vynesené po vydání zákona ustanovilo na věky veleknězem Syna dokonalého. (aiōn g165)

< Ahebri 7 >