< Ahebri 5 >

1 Mkulu wa ansembe aliyense amasankhidwa kuchokera pakati pa anthu ndipo amayikidwa kuti aziwayimirira pamaso pa Mulungu, kuti azipereka mphatso ndi nsembe chifukwa cha machimo.
Omnis namque Pontifex ex hominibus assumptus, pro hominibus constituitur in iis, quæ sunt ad Deum, ut offerat dona, et sacrificia pro peccatis:
2 Popeza kuti iye mwini ali ndi zofowoka zake, amatha kuwalezera mtima amene ali osadziwa ndi osochera.
qui condolere possit iis, qui ignorant, et errant: quoniam et ipse circumdatus est infirmitate:
3 Chifukwa cha ichi, iye amadziperekera nsembe chifukwa cha machimo ake omwe ndiponso chifukwa cha machimo a anthu ena.
et propterea debet, quemadmodum pro populo, ita etiam et pro semetipso offerre pro peccatis.
4 Palibe amene amadzipatsa yekha ulemu wotere, koma amachita kuyitanidwa ndi Mulungu monga momwe anayitanidwira Aaroni.
Nec quisquam sumit sibi honorem, sed qui vocatur a Deo, tamquam Aaron.
5 Nʼchifukwa chake Khristu sanadzipatse yekha ulemu wokhala Mkulu wa ansembe. Koma Mulungu anamuwuza kuti, “Iwe ndiwe Mwana wanga; Ine lero ndakhala Atate ako.”
Sic et Christus non semetipsum clarificavit ut pontifex fieret: sed qui locutus est ad eum: Filius meus es tu, ego hodie genui te.
6 Ndipo penanso anati, “Iwe ndiwe wansembe mpaka muyaya, monga mwa unsembe wa Melikizedeki.” (aiōn g165)
Quemadmodum et in alio loco dicit: Tu es sacerdos in æternum, secundum ordinem Melchisedech. (aiōn g165)
7 Yesu, pa nthawi imene anali munthu pa dziko lapansi pano, anapereka mapemphero ake ndi zopempha mofuwula ndi misozi kwa Iye amene akanamupulumutsa ku imfa, ndipo anamumvera chifukwa anagonjera modzipereka.
Qui in diebus carnis suæ preces, supplicationesque ad eum, qui possit illum salvum facere a morte cum clamore valido, et lacrymis offerens, exauditus est pro sua reverentia:
8 Ngakhale Iye anali Mwana wa Mulungu anaphunzira kumvera pomva zowawa.
Et quidem cum esset Filius Dei, didicit ex iis, quæ passus est, obedientiam:
9 Atasanduka wangwiro kotheratu, anakhala gwero la chipulumutso chosatha kwa onse omvera Iye. (aiōnios g166)
et consummatus, factus est omnibus obtemperantibus sibi, causa salutis æternæ, (aiōnios g166)
10 Ndipo Mulungu anamuyika kukhala Mkulu wa ansembe, monga mwa dongosolo la unsembe wa Melikizedeki.
appellatus a Deo pontifex iuxta ordinem Melchisedech.
11 Tili ndi zambiri zoti tinganene pa zimenezi, koma ndi zovuta kukufotokozerani chifukwa ndinu ochedwa kuphunzira.
De quo nobis grandis sermo, et ininterpretabilis ad dicendum: quoniam imbecilles facti estis ad audiendum.
12 Ngakhale kuti pa nthawi ino munayenera kukhala aphunzitsi, pakufunikabe munthu wina kuti abwerezenso kudzakuphunzitsani maphunziro oyambira a choonadi cha Mulungu. Ndinu ofunika mkaka osati chakudya cholimba!
Etenim cum deberetis magistri esse propter tempus: rursum indigetis ut vos doceamini quæ sint elementa exordii sermonum Dei: et facti estis quibus lacte opus sit, non solido cibo.
13 Aliyense amene amangodya mkaka okha, akanali mwana wakhanda, sakudziwa bwino chiphunzitso cha chilungamo.
Omnis enim, qui lactis est particeps, expers est sermonis iustitiæ, parvulus enim est.
14 Koma chakudya cholimba ndi cha anthu okhwima msinkhu, amene pogwiritsa ntchito nzeru zawo, aphunzira kusiyanitsa chabwino ndi choyipa.
Perfectorum autem est solidus cibus: eorum, qui pro consuetudine exercitatos habent sensus ad discretionem boni ac mali.

< Ahebri 5 >