< Ahebri 4 >
1 Popeza lonjezo lakuti tidzalowe mu mpumulo umene anatilonjeza lilipobe, tiyeni tisamale kuti pasakhale wina aliyense mwa inu wodzalephera kulowamo.
φοβηθωμεν ουν μηποτε καταλειπομενης επαγγελιας εισελθειν εις την καταπαυσιν αυτου δοκη τις εξ υμων υστερηκεναι
2 Pakuti Uthenga Wabwino unalalikidwa kwa ife, monganso iwo aja; koma iwo sanapindule nawo uthengawo chifukwa anangomva koma osakhulupirira.
και γαρ εσμεν ευηγγελισμενοι καθαπερ κακεινοι αλλ ουκ ωφελησεν ο λογος της ακοης εκεινους μη συγκεκραμενος τη πιστει τοις ακουσασιν
3 Tsono ife amene takhulupirira talowa mu mpumulo, monga momwe Mulungu akunenera kuti, “Ndili wokwiya ndinalumbira kuti, ‘Iwo sadzalowa konse mu mpumulo wanga.’” Ananena zimenezi ngakhale anali atatsiriza kale ntchito yolenga dziko lapansi.
εισερχομεθα γαρ εις την καταπαυσιν οι πιστευσαντες καθως ειρηκεν ως ωμοσα εν τη οργη μου ει εισελευσονται εις την καταπαυσιν μου καιτοι των εργων απο καταβολης κοσμου γενηθεντων
4 Pena pake wayankhula za tsiku lachisanu ndi chiwiri mʼmawu awa: “Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri, Mulungu anapumula ku ntchito zake zonse.”
ειρηκεν γαρ που περι της εβδομης ουτως και κατεπαυσεν ο θεος εν τη ημερα τη εβδομη απο παντων των εργων αυτου
5 Pa ndime inonso akunena za zomwezo pamene akuti, “Iwo sadzalowa konse mu mpumulo wanga.”
και εν τουτω παλιν ει εισελευσονται εις την καταπαυσιν μου
6 Popeza kwatsalabe kuti ena adzalowe mu mpumulowo, koma aja anayamba kumva Uthenga Wabwino sanalowe chifukwa cha kusamvera kwawo.
επει ουν απολειπεται τινας εισελθειν εις αυτην και οι προτερον ευαγγελισθεντες ουκ εισηλθον δι απειθειαν
7 Nʼchifukwa chake Mulungu anayikanso tsiku lina limene analitcha “Lero.” Patapita nthawi yayitali Iye anayankhula za tsiku lomweli kudzera mwa Davide, monga ndinanena kale kuti, “Lero mukamva mawu ake, musawumitse mitima yanu.”
παλιν τινα οριζει ημεραν σημερον εν δαβιδ λεγων μετα τοσουτον χρονον καθως ειρηται σημερον εαν της φωνης αυτου ακουσητε μη σκληρυνητε τας καρδιας υμων
8 Ngati Yoswa akanalowetsa anthu mu mpumulo, Mulungu sakananena pambuyo pake za tsiku lina.
ει γαρ αυτους ιησους κατεπαυσεν ουκ αν περι αλλης ελαλει μετα ταυτα ημερας
9 Kotero tsono kwatsala mpumulo wa Sabata kwa anthu a Mulungu;
αρα απολειπεται σαββατισμος τω λαω του θεου
10 Pakuti aliyense amene analowa mu mpumulo wa Mulungu anapuma pa ntchito zake, monga momwe Mulungu anachitira.
ο γαρ εισελθων εις την καταπαυσιν αυτου και αυτος κατεπαυσεν απο των εργων αυτου ωσπερ απο των ιδιων ο θεος
11 Tiyeni tsono tiyesetse kulowa mu mpumulo, kuti pasapezeke wina aliyense wolephera potsatira chitsanzo chawo cha kusamvera.
σπουδασωμεν ουν εισελθειν εις εκεινην την καταπαυσιν ινα μη εν τω αυτω τις υποδειγματι πεση της απειθειας
12 Paja Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu. Ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse. Amalowa mpaka molumikizirana moyo ndi mzimu, ndiponso molumikizirana fundo ndi mafuta a mʼmafupa. Amaweruza malingaliro ndi zokhumba za mʼmitima.
ζων γαρ ο λογος του θεου και ενεργης και τομωτερος υπερ πασαν μαχαιραν διστομον και διικνουμενος αχρι μερισμου ψυχης τε και πνευματος αρμων τε και μυελων και κριτικος ενθυμησεων και εννοιων καρδιας
13 Palibe kanthu kobisika pamaso pa Mulungu. Zinthu zonse zili poyera ndi zovundukuka pamaso pa Iye amene tiyenera kumufotokozera zonse zimene tachita.
και ουκ εστιν κτισις αφανης ενωπιον αυτου παντα δε γυμνα και τετραχηλισμενα τοις οφθαλμοις αυτου προς ον ημιν ο λογος
14 Popeza kuti tili ndi Mkulu wa ansembe wopambana, amene analowa kale kumwamba, Yesu Mwana wa Mulungu, tiyeni tigwiritsitse chikhulupiriro chathu chimene timavomereza.
εχοντες ουν αρχιερεα μεγαν διεληλυθοτα τους ουρανους ιησουν τον υιον του θεου κρατωμεν της ομολογιας
15 Pakuti sitili ndi Mkulu wa ansembe amene sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofowoka zathu. Koma tili naye amene anayesedwa mʼnjira zonse monga ife, koma sanachimwe.
ου γαρ εχομεν αρχιερεα μη δυναμενον συμπαθησαι ταις ασθενειαις ημων πεπειραμενον δε κατα παντα καθ ομοιοτητα χωρις αμαρτιας
16 Tiyeni tsono tiyandikire ku mpando waufumu, wachisomo mopanda mantha, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo chotithandiza pa nthawi yeniyeni.
προσερχωμεθα ουν μετα παρρησιας τω θρονω της χαριτος ινα λαβωμεν ελεον και χαριν ευρωμεν εις ευκαιρον βοηθειαν